Deuteronomo 32:1-52
32 “Tamverani kumwamba inu, ndipo ine ndilankhula,Dziko lapansi limve mawu a pakamwa panga.
2 Malangizo anga adzagwa ngati mvula,Mawu anga adzatsika ngati mame,Ngati mvula yowaza pa udzu,Ngatinso mvula yamphamvu pazomera.
3 Chifukwa ndidzalengeza dzina la Yehova.+
Anthu inu, lengezani za ukulu wa Mulungu wathu!+
4 Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro,+Njira zake zonse ndi zolungama.+
Mulungu wokhulupirika,+ amene sachita zinthu zopanda chilungamo.+Iye ndi wolungama ndi wowongoka.+
5 Iwo ndi amene achita zinthu zoipa.+
Iwo si ana ake, ali ndi vuto ndi iwowo.+
Iwo ndi mʼbadwo wopotoka maganizo komanso wachinyengo!+
6 Kodi Yehova mukuyenera kumuchitira zimenezi,+Anthu opusa ndi opanda nzeru inu?+
Kodi iye si Atate wanu amene anakulengani,+Amene anakupangani ndi kukukhazikitsani monga mtundu?
7 Kumbukirani masiku akale,Ganizirani zaka za mibadwo ya mʼmbuyo.
Funsani bambo anu ndipo akuuzani,+Amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozerani.
8 Pamene Wamʼmwambamwamba anapereka cholowa ku mitundu ya anthu,+Pamene analekanitsa ana a Adamu,*+Anaika malire a anthu ena onse+Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+
9 Pakuti anthu a Yehova ndi gawo lake.+Yakobo ndiye cholowa chake.+
10 Anamupeza mʼdziko lachipululu,+Mʼchipululu chopanda kanthu, molira zilombo.+
Anamuzungulira kuti amuteteze, anamusamalira,+Ndipo anamuteteza ngati mwana wa diso lake.+
11 Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera chisa chake,Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,Mmene chimatambasulira mapiko ake, kuti chitenge anawo,Nʼkuwanyamula pamapiko ake,+
12 Ndi Yehova yekha amene anapitiriza kumutsogolera,*+Panalibe mulungu wachilendo amene anali naye.+
13 Anamuyendetsa pamapiri a dziko lapansi,+Moti anadya zokolola za mʼmunda.+
Anamudyetsa uchi wochokera mʼthanthwe,Ndi mafuta ochokera mʼmwala wa nsangalabwi.
14 Anamudyetsanso mafuta a mkaka wa ngʼombe ndi mkaka wa nkhosa,Pamodzi ndi nkhosa zabwino kwambiri,*Komanso nkhosa zamphongo za ku Basana ndi mbuzi zamphongo,Pamodzi ndi tirigu wabwino koposa.*+Ndipo munamwa vinyo wochokera mʼmagazi a mphesa.*
15 Yesuruni* atanenepa, anapandukira mbuye wake.
Iwe wanenepa, wakula thupi, wakhuta mopitirira muyezo.+
Choncho iye anasiya Mulungu amene anamupanga,+Ndipo ananyoza Thanthwe la chipulumutso chake.
16 Anamukwiyitsa ndi milungu yachilendo.+Ankamukhumudwitsa ndi zinthu zonyansa.+
17 Iwo ankapereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+Anapereka nsembe kwa milungu imene sankaidziwa,Kwa milungu yatsopano yongobwera kumene,Komanso kwa milungu imene makolo anu sankaidziwa.
18 Munaiwala Thanthwe+ limene linakuberekani,Ndipo simunakumbukire Mulungu amene anakuberekani.+
19 Yehova ataona zimenezi anawakana+Chifukwa chakuti ana ake aamuna ndi aakazi anamukhumudwitsa.
20 Choncho iye anati, ‘Ndiwabisira nkhope yanga,+Ndione kuti ziwathera bwanji.
Chifukwa iwo ndi mʼbadwo wokonda zoipa,+Ana osakhulupirika.+
21 Iwo andikwiyitsa* ndi milungu yabodza.+Andikhumudwitsa ndi mafano awo opanda pake.+
Choncho ine ndiwachititsa nsanje ndi anthu opanda pake,+Ndiwakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+
22 Mkwiyo wanga wayatsa moto+Umene udzayaka mpaka kukafika pansi penipeni pa Manda,*+Ndipo udzapsereza dziko lapansi ndi zokolola zake,Komanso udzayatsa maziko a mapiri.
23 Ndidzawonjezera masoka awo,Mivi yanga yonse ndidzaigwiritsa ntchito pa iwo.
24 Adzalefuka ndi njala+Ndipo adzavutika ndi kutentha thupi koopsa komanso adzawonongedwa nʼkutheratu.+
Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali+Komanso njoka zapoizoni za mʼfumbi.
25 Kunja, lupanga lidzawasandutsa anamfedwa.+Mʼnyumba, anthu adzagwidwa ndi mantha+Zimenezi zidzachitikira mnyamata, namwali,Mwana wamngʼono ndi munthu wa imvi.+
26 Ndikanatha kunena kuti: “Ndidzawabalalitsa,Ndidzachititsa kuti anthu asakumbukirenso za iwo,”
27 Koma ndinkaopa zimene mdani anganene,+Chifukwa adaniwo angaganize molakwika.+
Iwo anganene kuti: “Tapambana chifukwa cha mphamvu zathu,+Si Yehova amene wachita zonsezi.”
28 Chifukwa iwo ndi mtundu wopanda nzeru,*Ndipo ndi osazindikira.+
29 Zikanakhala bwino ngati akanakhala anzeru,+ chifukwa akanaganizira mozama zimenezi.+
Akanaganizira kuti ziwathera bwanji.+
30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,Kapena anthu awiri angathamangitse bwanji anthu 10,000?+
Nʼzosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+Komanso ngati Yehova atawapereka.
31 Chifukwa thanthwe lawo si lofanana ndi Thanthwe lathu,+Ndipo adani athu akudziwa bwino zimenezi.+
32 Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,Ndi kuminda ya mʼmapiri a ku Gomora.+
Zipatso zawo za mphesa ndi zapoizoniNdipo ndi zowawa.+
33 Vinyo wawo ndi poizoni wa njoka,Ndi poizoni woopsa wa mamba.
34 Kodi ine sindinasunge zimenezi,Nʼkuziikira chidindo mʼnyumba yanga yosungira zinthu?+
35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+Zimenezi zidzachitika pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo likadzaterereka,+Chifukwa tsiku la tsoka lawo layandikira,Ndipo zowagwera zifika mofulumira.’
36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake+Akadzaona kuti mphamvu zawo zatha,Komanso kuti kwangotsala anthu ovutika ndi ofooka.
37 Ndiyeno iye adzanena kuti, ‘Ili kuti milungu yawo,+Thanthwe limene anathawirako,
38 Milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo,*Ndi kumwa vinyo wa nsembe zawo zachakumwa?+
Ibwere kudzakuthandizani.
Ikhale malo anu othawirako.
39 Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+Ndipo palibe Mulungu wina koma ine ndekha.+
Ndimapha komanso ndimapereka moyo.+
Ndimavulaza,+ ndipo ndidzachiritsa,+Palibe aliyense amene angapulumutse munthu mʼdzanja langa.+
40 Ndakweza dzanja langa kumwambaNdipo ndikulumbira kuti: “Ine, Mulungu wamuyaya, ndikulumbira pa dzina langa,”+
41 Ndikanola lupanga langa lonyezimira,Nʼkukonzekeretsa dzanja langa kuti lipereke chiweruzo,+Ndidzabwezera adani anga,+Ndipo ndidzapereka chilango kwa amene amadana nane.
42 Ndidzaledzeretsa mivi yanga ndi magazi,Ndipo lupanga langa lidzadya nyama,Ndi magazi a anthu ophedwa komanso ogwidwa,Ndiponso mitu ya atsogoleri a adani.’
43 Inu anthu a mitundu ina, sangalalani limodzi ndi anthu ake,+Chifukwa adzabwezera magazi a atumiki ake,+Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+Komanso adzaphimba machimo a dziko la anthu ake.”*
44 Ndiyeno Mose anabwera nʼkulankhula mawu onse a nyimbo iyi anthu onse akumva,+ iye pamodzi ndi Hoshiya*+ mwana wa Nuni.
45 Mose atamaliza kulankhula mawu onsewa kwa Aisiraeli onse,
46 anawauza kuti: “Ganizirani mofatsa mawu onse okuchenjezani amene ndikulankhula nanu lero,+ kuti muuze ana anu kuti azionetsetsa kuti akuchita zimene mawu onse a Chilamulo ichi akunena.+
47 Chifukwa amenewa si mawu opanda pake kwa inu, koma angakuthandizeni kukhala ndi moyo.+ Mukamatsatira mawu amenewa mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukuwoloka Yorodano kuti mukalitenge kukhala lanu.”
48 Yehova analankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti:
49 “Kwera mʼphiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili mʼdziko la Mowabu, moyangʼanizana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa Aisiraeli kuti likhale lawo.+
50 Kenako ukafera paphiri limene ukufuna kukwerali nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako,* mofanana ndi Aroni mʼbale wako amene anafera paphiri la Hora+ nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.
51 Izi zili choncho chifukwa awirinu simunakhale okhulupirika kwa ine pakati pa Aisiraeli kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini, chifukwa simunandilemekeze pamaso pa Aisiraeli.+
52 Iwe udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa mʼdziko limene ndikupereka kwa Aisiraeli.”+
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “mitundu ya anthu.”
^ Apa akunena Yakobo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mafuta a nkhosa zamphongo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mafuta apaimpso a tirigu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “madzi a zipatso za mphesa.”
^ Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.
^ Kapena kuti, “anandichititsa nsanje.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “wosafuna kumva malangizo.”
^ Kapena kuti, “imene inkadya nsembe zawo zabwino kwambiri.”
^ Kapena kuti, “adzayeretsa dziko la anthu ake.”
^ Dzina lakale la Yoswa. Hoshiya ndi chidule cha dzina lakuti Hoshaiya limene limatanthauza kuti, “Wopulumutsidwa ndi Ya; Ya Wapulumutsa.”
^ Awa ndi mawu okuluwika otanthauza imfa.