Deuteronomo 6:1-25

  • Muzikonda Yehova ndi mtima wanu wonse (1-9)

    • “Tamverani Aisiraeli inu” (4)

    • Makolo aziphunzitsa ana (6, 7)

  • Musaiwale Yehova (10-15)

  • Musamamuyese Yehova (16-19)

  • Mudzafotokozere mʼbadwo wotsatira (20-25)

6  “Tsopano amenewa ndi malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wanu wandipatsa kuti ndikuphunzitseni, kuti muzikazitsatira mukawoloka mtsinje wa Yorodano nʼkupita mʼdziko limene mukukalitenga kuti likhale lanu, 2  kuti muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira malangizo ake komanso malamulo ake amene ndikukuuzani, inuyo, ana anu ndi zidzukulu zanu,+ masiku onse a moyo wanu, nʼcholinga choti mukhale ndi moyo nthawi yaitali.+ 3  Ndipo inu Aisiraeli, muzimvetsera ndi kutsatira malangizo ndi malamulo akewo mosamala, kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi, mogwirizana ndi zimene Yehova, Mulungu wa makolo anu anakulonjezani. 4  Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.+ 5  Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse+ ndi mphamvu zanu zonse.+ 6  Mawu awa amene ndikukulamulani lerowa azikhala pamtima panu, 7  ndipo muziwakhomereza* mumtima mwa ana anu.+ Muzilankhula nawo mawuwo mukakhala pansi mʼnyumba mwanu, mukamayenda pamsewu, mukamagona komanso mukadzuka.+ 8  Muwamange padzanja lanu kuti muziwakumbukira, ndipo azikhala ngati chomanga pachipumi panu.*+ 9  Muwalembe pamafelemu a nyumba zanu komanso pamageti a mzinda wanu. 10  Ndiyeno Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene analumbira kwa makolo anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsani,+ dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yabwino imene simunamange ndinu,+ 11  yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zosiyanasiyana zabwino zimene simunagwirire ntchito, zitsime zimene simunakumbe ndinu komanso minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale ndinu, ndiye mukakadya nʼkukhuta,+ 12  mukasamale kuti musakaiwale Yehova+ amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo. 13  Muziopa Yehova Mulungu wanu+ nʼkumamutumikira,+ ndipo muzilumbira pa dzina lake.+ 14  Musatsatire milungu ina, milungu iliyonse ya anthu amene akuzungulirani,+ 15  chifukwa Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.+ Mukatsatira milungu ina, mkwiyo wa Yehova Mulungu wanu udzakuyakirani+ ndipo adzakufafanizani padziko lapansi.+ 16  Yehova Mulungu wanu musamamuyese+ ngati mmene munamuyesera ku Masa.+ 17  Muzionetsetsa kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, zikumbutso zake ndi malangizo ake amene wakulamulani kuti muziwatsatira. 18  Muzichita zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova kuti zikuyendereni bwino komanso kuti mukalowe mʼdziko labwino limene Yehova analumbira kwa makolo anu, nʼkulitenga kuti likhale lanu,+ 19  pothamangitsa adani anu onse mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza.+ 20  Mʼtsogolo mwana wanu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi zikumbutso, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wathu anakupatsani zimatanthauza chiyani?’ 21  mwana wanuyo mudzamuyankhe kuti, ‘Tinali akapolo a Farao ku Iguputo, koma Yehova anatitulutsa ku Iguputoko ndi dzanja lamphamvu. 22  Choncho Yehova anapitiriza kuchita zizindikiro ndi zodabwitsa zazikulu ndiponso zowononga mu Iguputo monse,+ kwa Farao ndi kwa anthu onse amʼnyumba mwake, ife tikuona.+ 23  Ndipo anatitulutsa kumeneko kuti atibweretse kuno kudzatipatsa dziko limene analumbira kwa makolo athu.+ 24  Ndiyeno Yehova anatilamula kuti tizitsatira malangizo onsewa komanso kuti tiziopa Yehova Mulungu wathu kuti zinthu zizitiyendera bwino nthawi zonse,+ komanso kuti tikhale ndi moyo+ ngati mmene zilili lero. 25  Ndipo tikamatsatira malamulo onsewa mosamala kwambiri pomvera* Yehova Mulungu wathu mogwirizana ndi zimene anatilamula, ndiye kuti tikuchita chilungamo pamaso pake.’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “muziwaphunzitsa mobwerezabwereza kuti akhazikike.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa maso anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pamaso pa.”