Deuteronomo 8:1-20
8 “Muonetsetse kuti mukusunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ komanso kuti muchuluke, nʼkupita kukatenga dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu.+
2 Muzikumbukira njira yaitali imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani mʼchipululu zaka 40 zonsezi.+ Iye anakuyendetsani mʼchipululu kuti akuphunzitseni kudzichepetsa komanso kukuyesani+ pofuna kudziwa zimene zinali mumtima mwanu,+ kuti aone ngati mungasunge malamulo ake kapena ayi.
3 Anakuphunzitsani kudzichepetsa pokulolani kuti mukhale ndi njala+ nʼkukudyetsani mana,+ amene inu kapena makolo anu sankawadziwa. Anachita zimenezi kuti mudziwe kuti munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.+
4 Zovala zimene munavala sizinathe ndipo mapazi anu sanatupe pa zaka 40 zimenezi.+
5 Inu mukudziwa bwino mumtima mwanu kuti Yehova Mulungu wanu ankakulangizani, ngati mmene bambo amalangizira mwana wake.+
6 Tsopano muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu poyenda mʼnjira zake ndi kumuopa.
7 Chifukwa Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino,+ dziko la mitsinje ya madzi,* akasupe ndi madzi ochuluka amene akuyenda mʼzigwa ndi mʼdera lamapiri,
8 dziko la tirigu, balere, mphesa, mitengo ya mkuyu ndi makangaza,*+ dziko la maolivi opangira mafuta ndiponso la uchi,+
9 mʼdziko limene simudzasowa chakudya komanso simudzasowa chilichonse, dziko limene miyala yake amapangira zitsulo, limenenso mʼmapiri ake mudzakumbamo kopa.*
10 Mukadzadya nʼkukhuta, mudzatamande Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.+
11 Samalani kuti musaiwale Yehova Mulungu wanu polephera kusunga malamulo, zigamulo ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero.
12 Mukadzadya nʼkukhuta, kumanga nyumba zabwino nʼkukhalamo,+
13 ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu nʼkuchuluka, siliva ndi golide wanu nʼkuwonjezeka ndiponso nʼkukhala ndi zinthu zochuluka,
14 musakalole kuti mtima wanu ukayambe kunyada+ nʼkukuchititsani kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo,+
15 amene anakuyendetsani mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni, zinkhanira ndiponso nthaka youma yopanda madzi. Iye anachititsa kuti madzi atuluke pamwala wolimba,+
16 anakudyetsani mana+ mʼchipululu, chakudya chimene makolo anu sankachidziwa, kuti akuphunzitseni kudzichepetsa+ komanso kukuyesani kuti mʼtsogolo zinthu zidzakuyendereni bwino.+
17 Ngati mumtima mwanu munganene kuti, ‘Chuma ichi ndachipeza chifukwa cha ntchito ya manja anga komanso mphamvu zanga,’+
18 muzikumbukira kuti ndi Yehova Mulungu wanu amene amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbira kwa makolo anu, ngati mmene zilili lero.+
19 Koma mukadzaiwala Yehova Mulungu wanu nʼkutsatira milungu ina, kuitumikira ndiponso kuigwadira, ndikukuchenjezani lero kuti anthu inu mudzatha ndithu.+
20 Mudzatheratu mofanana ndi mitundu imene Yehova akuiwononga pamaso panu, chifukwa simunamvere mawu a Yehova Mulungu wanu.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “makhwawa a madzi.”
^ “Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
^ Kapena kuti, “mkuwa.”