Ekisodo 1:1-22

  • Aisiraeli anachulukana ku Iguputo (1-7)

  • Farao anazunza Aisiraeli (8-14)

  • Azamba oopa Mulungu anapulumutsa ana (15-22)

1  Ndiyeno awa ndi mayina a ana a Isiraeli kapena kuti Yakobo, amene anapita nawo ku Iguputo. Mwana wamwamuna aliyense anapita limodzi ndi banja lake:+  Rubeni, Simiyoni, Levi, Yuda,+  Isakara, Zebuloni, Benjamini,  Dani, Nafitali, Gadi ndi Aseri.+  Ana onse a Yakobo komanso zidzukulu zake* analipo 70, koma Yosefe anali kale ku Iguputo.+  Patapita nthawi Yosefe anamwalira,+ chimodzimodzinso abale ake onse ndi anthu a mʼbadwo wonsewo.  Aisiraeli* anaberekana ndipo anachuluka kwambiri mʼdzikomo. Iwo anapitiriza kukhala amphamvu komanso anachulukana mofulumira kwambiri, moti anadzaza mʼdzikomo.+  Patapita nthawi, mfumu ina yomwe sinkamudziwa Yosefe inayamba kulamulira ku Iguputo.  Mfumuyo inauza anthu ake kuti: “Taonani! Aisiraeli achuluka kwambiri ndipo ndi amphamvu kuposa ife.+ 10  Tiyeni tiwachenjerere anthu amenewa kuti asapitirize kuchulukana, kuopera kuti pa nthawi ya nkhondo angadzagwirizane ndi adani athu nʼkumenyana nafe kenako nʼkuchoka mʼdziko muno.” 11  Choncho anaika akapitawo oti aziwayangʼanira pa ntchito yawo yaukapolo kuti aziwazunza powagwiritsa ntchito mwankhanza.+ Ndipo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramese+ kuti ikhale mosungiramo zinthu.* 12  Koma pamene ankawazunza kwambiri mʼpamenenso ankawonjezeka komanso kufalikira kwambiri, moti Aiguputo anachita mantha kwambiri chifukwa cha Aisiraeliwo.+ 13  Choncho Aiguputo anakakamiza Aisiraeli kuti azigwira ntchito yaukapolo mwankhanza.+ 14  Iwo anasautsa moyo wa Aisiraeliwo powagwiritsa ntchito yowawa, yomwe inali yoponda matope ndi kuumba njerwa. Anawagwiritsa ntchito yaukapolo wa mtundu uliwonse mʼmunda. Ankawazunza komanso kuwagwiritsa ntchito ya mtundu uliwonse wa ukapolo.+ 15  Kenako mfumu ya Iguputo inalankhula ndi azamba* a Chiheberi, amene mayina awo anali Sifira ndi Puwa. 16  Iye anawauza kuti: “Mukamathandiza amayi a Chiheberi kubereka+ ndipo mwaona kuti mwana amene akubadwayo ndi wamwamuna muzimupha, koma ngati ndi wamkazi muzimusiya wamoyo.” 17  Koma azambawo ankaopa Mulungu woona, ndipo sanachite zimene mfumu ya Iguputo inawauza. Mʼmalomwake, ana aamuna ankawasiya amoyo.+ 18  Patapita nthawi, mfumu ya Iguputo inaitana azamba aja nʼkuwafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ana aamuna mwakhala mukuwasiya amoyo?” 19  Azambawo anauza Farao kuti: “Akazi a Chiheberi sali ngati akazi a ku Iguputo kuno. Akazi a Chiheberi ndi amphamvu, moti mzamba asanafike iwo amakhala atabereka kale.” 20  Choncho Mulungu anawadalitsa azambawo, ndipo Aisiraeli anapitiriza kuwonjezeka nʼkukhala amphamvu kwambiri. 21  Chifukwa chakuti azambawo anaopa Mulungu woona, patapita nthawi iye anawadalitsa powapatsa ana awoawo. 22  Kenako Farao analamula anthu ake onse kuti: “Mwana aliyense wamwamuna wobadwa kumene wa Aheberi muzimuponya mumtsinje wa Nailo, koma mwana aliyense wamkazi muzimusiya wamoyo.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene anatuluka pantchafu ya Yakobo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana a Isiraeli.”
Mʼmizinda imeneyi anamangamo nkhokwe ndi nyumba zina zosungiramo chakudya ndi zinthu zina.
“Mzamba” ndi munthu amene amathandiza amayi pobereka. Ena amamutcha “namwino.”