Ekisodo 37:1-29
37 Kenako Bezaleli+ anapanga Likasa+ la mtengo wa mthethe masentimita 110* mulitali, masentimita 70 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi kupita mʼmwamba.+
2 Analikuta ndi golide woyenga bwino mkati ndi kunja komwe ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+
3 Ndiyeno analipangira mphete 4 zagolide zoika pamwamba pa miyendo yake 4. Mphete ziwiri zinali mbali imodzi ndipo mphete zina ziwiri zinali mbali inayo.
4 Anapanganso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide.+
5 Kenako analowetsa ndodo zonyamulirazo mumphete zamʼmbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo.+
6 Anapanga chivundikiro chagolide woyenga bwino+ masentimita 110 mulitali ndi masentimita 70 mulifupi.+
7 Anapanganso akerubi awiri+ agolide. Anali osula ndipo anawaika kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+
8 Kerubi mmodzi anamuika kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina anamuika kumbali inayo. Akerubiwo anawapanga kumapeto onse awiri a chivundikirocho.
9 Mapiko a akerubi awiriwo anawakweza mʼmwamba nʼkuwatambasula ndipo anaphimba chivundikirocho ndi mapiko awo.+ Akerubiwo anakhala moyangʼanizana ndipo nkhope zawo zinaweramira pachivundikirocho.+
10 Ndiyeno anapanga tebulo la mtengo wa mthethe+ masentimita 90 mulitali, masentimita 45 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi mpaka mʼmwamba.+
11 Analikuta ndi golide woyenga bwino ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo.
12 Analipangiranso felemu kuzungulira tebulo lonse muyezo wake masentimita 7* mulifupi mwake ndipo anapanga mkombero wagolide pafelemulo.
13 Kuwonjezera pamenepo, analipangira mphete 4 zagolide nʼkuziika mʼmakona ake 4 mmene munali miyendo yake 4.
14 Mphetezo zinali pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa ndodo zonyamulira tebulolo.
15 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe nʼkuzikuta ndi golide. Ndodo zimenezi zinali zonyamulira tebulolo.
16 Atatero anapanga ziwiya zapatebulolo, mbale zake, makapu, mitsuko ndi mbale zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Anazipanga ndi golide woyenga bwino.+
17 Kenako anapanga choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino ndipo chinali chosula. Choikapo nyalecho chinali chinthu chimodzi ndipo chinali ndi tsinde, thunthu, timasamba tamʼmunsi mwa duwa, mphindi ndi maluwa.+
18 Choikapo nyalecho chinali ndi nthambi 6. Kumbali ina kunali nthambi zitatu ndipo kumbali inayo kunalinso nthambi zitatu.
19 Panthambi za mbali imodzi, iliyonse inali ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. Panthambi za mbali inayo, iliyonse inalinso ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyalecho anazipanga choncho.
20 Pathunthu la choikapo nyalecho panali timasamba 4 tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa.
21 Mphindi imodzi inali pansi pa nthambi zake ziwiri zoyambirira. Mphindi ina inalinso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mphindi inanso inali pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zinali choncho ndi nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyale.
22 Choikapo nyale chonsecho kuphatikizapo mphindi ndi nthambi zake chinali chimodzi ndipo anachisula ndi golide woyenga bwino.
23 Kenako anachipangira nyale 7,+ zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino.
24 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi anazipanga pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente imodzi.*
25 Kenako anapanga guwa lansembe zofukiza+ la matabwa a mthethe. Mulitali mwake linali masentimita 45, mulifupi mwake masentimita 45. Mbali zake zonse 4 zinali zofanana, ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 90. Nyanga zake anazipangira kumodzi ndi guwalo.*+
26 Analikuta ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi mʼmbali mwake kuzungulira guwalo komanso nyanga zake. Ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo.
27 Anapanga mphete ziwiri zagolide mʼmunsi mwa mkombero kumbali zake ziwiri zoyangʼanizana kuti muzilowa ndodo zonyamulira guwalo.
28 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide.
29 Anapanganso mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika+ ndi mafuta onunkhira abwino kwambiri,+ osakanizidwa mwaluso.*
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono iwiri ndi hafu.” Onani Zakumapeto B14.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhatho chimodzi.” Onani Zakumapeto B14.
^ Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
^ Kutanthauza kuti nyanga zimenezi sanazipangire padera nʼkuchita kuzilumikiza kuguwalo.
^ Kapena kuti, “ngati opangidwa ndi anthu ogwira ntchito yosakaniza mafuta.”