Ekisodo 40:1-38

  • Kumanga chihema (1-33)

  • Ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihema (34-38)

40  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 2  “Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, udzamange chihema kapena kuti chihema chokumanako.+ 3  Mkati mwake udzaikemo likasa la Umboni+ ndipo udzatchinge kumene kuli Likasalo ndi katani.+ 4  Mʼchihemacho udzaikemonso tebulo+ ndipo udzaikepo zinthu zake mwadongosolo. Kenako udzaikemo choikapo nyale+ nʼkuyatsa nyale zake.+ 5  Ndiyeno udzaike guwa lansembe zofukiza lagolide+ patsogolo pa likasa la Umboni, nʼkuika nsalu yotchinga pakhomo la chihema.+ 6  Udzaike guwa lansembe zopsereza+ patsogolo pa khomo la chihema kapena kuti chihema chokumanako. 7  Ndipo udzaike beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe nʼkuthiramo madzi.+ 8  Kenako udzatchinge bwalo la chihema+ ndi mpanda ndipo pakhomo pa bwalolo udzaikepo nsalu yake yotchinga.+ 9  Kenako udzatenge mafuta odzozera+ nʼkudzoza chihema ndi zonse zimene zili mkati mwake+ ndipo udzachiyeretse pamodzi ndi ziwiya zake zonse kuti chikhale chopatulika. 10  Udzadzozenso guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse nʼkuliyeretsa, kuti guwalo lidzakhale lopatulika kwambiri.+ 11  Ndiponso udzadzoze beseni ndi choikapo chake nʼkuliyeretsa. 12  Kenako udzabweretse Aroni ndi ana ake pafupi ndi khomo la chihema chokumanako ndipo udzawasambitse ndi madzi.+ 13  Ukatero udzaveke Aroni zovala zopatulika+ kenako nʼkumudzoza+ komanso kumuyeretsa ndipo adzatumikira monga wansembe wanga. 14  Kenako udzatenge ana ake nʼkuwaveka mikanjo.+ 15  Udzawadzoze ngati mmene unadzozera bambo awo+ kuti atumikire monga ansembe anga. Iwo akadzadzozedwa adzapitiriza kutumikira monga ansembe mʼmibadwo yawo yonse.”+ 16  Mose anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula.+ Anachitadi zomwezo. 17  Choncho mʼmwezi woyamba wa chaka chachiwiri, pa tsiku loyamba la mweziwo, anamanga chihema.+ 18  Pamene Mose ankamanga chihemacho, anayala pansi zitsulo zake+ nʼkukhazikamo mafelemu.+ Ndiyeno analowetsa ndodo zake+ nʼkuimika zipilala pamalo ake. 19  Atatero anayala nsalu+ yophimba pachihemacho ndi inanso yophimba+ pamwamba pake, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 20  Kenako anatenga Umboni+ ndi kuuika mu Likasa,+ ndipo analowetsa ndodo zonyamulira+ mʼmbali mwa Likasalo nʼkuika chivundikiro+ pamwamba pa Likasa.+ 21  Atatero analowetsa Likasa mʼchihema nʼkuika katani+ pamalo ake ndipo inatchinga likasa la Umboni,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 22  Ndiyeno analowetsa tebulo+ mʼchihema chokumanako nʼkuliika kumbali yakumpoto ya chihemacho, kunja kwa katani. 23  Kenako anaika mkate+ pamalo ake pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 24  Anaika choikapo nyale+ mʼchihema chokumanako patsogolo pa tebulo, kumbali yakumʼmwera ya chihemacho. 25  Ndipo anayatsa nyalezo+ pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 26  Kenako anaika guwa lansembe lagolide+ mʼchihema chokumanako patsogolo pa katani, 27  kuti azifukizirapo zofukiza+ zonunkhira,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 28  Atatero anaika nsalu yotchinga+ pakhomo la chihema. 29  Ndiyeno anaika guwa lansembe zopsereza+ pakhomo la chihema kapena kuti chihema chokumanako, kuti aziperekerapo nsembe yopsereza+ ndi nsembe yambewu, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 30  Kenako anaika beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe nʼkuthiramo madzi osamba.+ 31  Mose, Aroni ndi ana ake ankasamba mʼmanja ndi mapazi awo pamenepo. 32  Akamalowa mʼchihema chokumanako ndiponso akamapita kuguwa lansembe ankasamba,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 33  Pomaliza anamanga mpanda kuzungulira bwalo+ la chihema ndi guwa lansembe ndipo anaika nsalu yotchinga pakhomo la bwalolo.+ Choncho Mose anamaliza ntchitoyo. 34  Kenako mtambo unayamba kuphimba chihema chokumanako ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.+ 35  Mose sanathenso kulowa mʼchihema chokumanako, chifukwa mtambo unali utaphimba chihemacho ndipo munadzaza ulemerero wa Yehova.+ 36  Mʼzigawo zonse za ulendo wawo, mtambowo ukachoka pamwamba pa chihemacho nʼkukwera mʼmwamba, Aisiraeli ankanyamuka nʼkuyamba ulendo.+ 37  Koma ukapanda kukwera mʼmwamba, iwo sankanyamuka mpaka tsiku limene udzakwere.+ 38  Mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema masana ndipo usiku pankakhala moto. Nyumba yonse ya Isiraeli inkaona zimenezi mʼzigawo zonse za ulendo wawo.+

Mawu a M'munsi