Esitere 3:1-15
3 Kenako Mfumu Ahasiwero anakweza pa udindo Hamani+ mwana wa Hamedata mbadwa ya Agagi,+ ndipo anamupatsa mpando wapamwamba kuposa akalonga ena onse a mfumuyo.+
2 Choncho atumiki onse a mfumu amene ankakhala pageti la mfumu ankaweramira Hamani ndiponso kumugwadira chifukwa mfumu ndi imene inalamula kuti azimuchitira zimenezi. Koma Moredikayi ankakana kumuweramira kapena kumugwadira.
3 Choncho atumiki a mfumu amene ankakhala pagetiwo anafunsa Moredikayi kuti: “Nʼchifukwa chiyani sukutsatira lamulo la mfumu?”
4 Ankamufunsa zimenezi tsiku ndi tsiku koma iye sankawamvera. Kenako anthuwo anauza Hamani kuti aone ngati khalidwe la Moredikayi lingalekereredwe+ popeza iye anali atawauza kuti anali Myuda.+
5 Hamani ataona kuti Moredikayi sankamuweramira ndiponso kumugwadira, anakwiya kwambiri.+
6 Koma Hamani anaona kuti nʼzosakwanira kupha Moredikayi yekha chifukwa anthu anali atamuuza za anthu a mtundu wa Moredikayi. Choncho Hamani anaganiza zoti aphe Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredikayi mʼmadera onse amene Ahasiwero ankalamulira.
7 Ndiyeno mʼmwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani,* mʼchaka cha 12+ cha Mfumu Ahasiwero, anthu anachita Puri+ kapena kuti maere pamaso pa Hamani kuti adziwe tsiku ndi mwezi woyenerera. Maerewo anagwera mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+
8 Kenako Hamani anauza Mfumu Ahasiwero kuti: “Pali mtundu wina wa anthu+ umene ukupezeka paliponse mʼzigawo zonse za ufumu wanu.+ Malamulo awo ndi osiyana ndi malamulo a anthu ena onse ndipo sakutsatira malamulo anu. Choncho ngati mungawasiye anthu amenewa, zinthu sizikuyenderani bwino mfumu.
9 Ngati mungakonde mfumu, palembedwe lamulo loti anthu amenewa aphedwe. Ine ndidzapereka ndalama zokwana matalente* 10,000 asiliva kwa akuluakulu ogwira ntchito kunyumba ya mfumu kuti akaziike mosungiramo chuma cha mfumu.”*
10 Zitatero mfumu inavula mphete yake yodindira+ nʼkuipereka kwa Hamani+ mwana wa Hamedata, mbadwa ya Agagi,+ yemwe ankadana kwambiri ndi Ayuda.
11 Ndiyeno mfumu inauza Hamani kuti: “Siliva* komanso anthuwo ndakupatsa ndipo uchite nawo zilizonse zimene ukufuna.”
12 Kenako pa tsiku la 13 la mwezi woyamba, alembi a mfumu+ anaitanidwa. Ndipo alembiwo analemba+ zonse zimene Hamani analamula masatarapi* a mfumu, abwanamkubwa a mʼzigawo zosiyanasiyana ndiponso akalonga a anthu osiyanasiyana. Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu a kumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Makalatawa anawalemba mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndipo anawadinda ndi mphete yodindira ya mfumuyo.+
13 Makalatawo anawatumiza kuzigawo zonse za mfumu kudzera mwa anthu operekera makalata. Anachita izi kuti tsiku limodzi, tsiku la 13 la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara,+ aphe Ayuda onse, kaya ndi achinyamata, amuna achikulire, ana ndiponso akazi nʼkutenga zinthu zawo.+
14 Lamulo lopita kuzigawo zonse, limene analilemba mʼmakalatawo, linafalitsidwa kwa anthu a mitundu yonse kuti akonzekere tsiku limeneli.
15 Mfumu inalamula kuti operekera makalatawo apite mwamsanga.+ Lamuloli linaperekedwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Susani*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako mfumu ndi Hamani, anakhala pansi nʼkumamwa vinyo, koma mumzinda wa Susani munali chipwirikiti.
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto B15.
^ Onani Zakumapeto B15.
^ Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
^ Mabaibulo ena amati, “Ine ndidzapereka ndalama zokwana matalente 10,000 asiliva kuti akaziike mosungiramo chuma cha mfumu zoti zipite kwa anthu amene adzagwire ntchitoyi.”
^ Nʼkutheka kuti amanena za siliva amene akatenge akakapha Ayuda.
^ Limeneli ndi dzina laudindo la anthu oteteza ufumu.
^ Kapena kuti, “Susa.”