Ezara 2:1-70
2 Awa ndi anthu amʼchigawo* amene anatuluka mu ukapolo+ pa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+
2 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,*+ Nehemiya, Seraya, Reelaya, Moredikayi, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Bana.
Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:+
3 Ana a Parosi, 2,172.
4 Ana a Sefatiya, 372.
5 Ana a Ara,+ 775.
6 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu, 2,812.
7 Ana a Elamu,+ 1,254.
8 Ana a Zatu,+ 945.
9 Ana a Zakai, 760.
10 Ana a Bani, 642.
11 Ana a Bebai, 623.
12 Ana a Azigadi, 1,222.
13 Ana a Adonikamu, 666.
14 Ana a Bigivai, 2,056.
15 Ana a Adini, 454.
16 Ana a Ateri, a mʼbanja la Hezekiya, 98.
17 Ana a Bezai, 323.
18 Ana a Yora, 112.
19 Ana a Hasumu,+ 223.
20 Ana a Gibara, 95.
21 Ana a Betelehemu, 123.
22 Amuna a ku Netofa, 56.
23 Amuna a ku Anatoti,+ 128.
24 Ana a Azimaveti, 42.
25 Ana a Kiriyati-yearimu, Kefira ndi Beeroti, 743.
26 Ana a Rama+ ndi Geba,+ 621.
27 Amuna a ku Mikemasi, 122.
28 Amuna a ku Beteli ndi a ku Ai,+ 223.
29 Ana a Nebo,+ 52.
30 Ana a Magabisi, 156.
31 Ana a Elamu wina, 1,254.
32 Ana a Harimu, 320.
33 Ana a Lodi, Hadidi ndi Ono, 725.
34 Ana a Yeriko, 345.
35 Ana a Senaya, 3,630.
36 Ansembe:+ Ana a Yedaya,+ a mʼbanja la Yesuwa,+ 973.
37 Ana a Imeri,+ 1,052.
38 Ana a Pasuri,+ 1,247.
39 Ana a Harimu,+ 1,017.
40 Alevi:+ Ana a Yesuwa, a mʼbanja la Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodaviya, 74.
41 Oimba,+ ana a Asafu,+ 128.
42 Ana a alonda apageti:+ ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita ndi ana a Sobai, onse analipo 139.
43 Atumiki apakachisi:*+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,
44 ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni,
45 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu,
46 ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani,
47 ana a Gideli, ana a Gahara, ana a Reyaya,
48 ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu,
49 ana a Uziza, ana a Paseya, ana a Besai,
50 ana a Asena, ana a Meyuni, ana a Nefusimu,
51 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,
52 ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa,
53 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,
54 ana a Neziya ndi ana a Hatifa.
55 Ana a atumiki a Solomo: Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,+
56 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,
57 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu ndi ana a Ami.
58 Atumiki onse apakachisi* pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392.
59 Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi, ndi awa:+
60 ana a Delaya, ana a Tobia ndi ana a Nekoda, 652.
61 Ana a ansembe anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi,+ ana a Barizilai amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ wa ku Giliyadi nʼkuyamba kutchedwa ndi dzina lawo.
62 Amenewa ndi amene mayina awo anawayangʼana mʼkaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Choncho anawaletsa kuti asatumikire ngati ansembe.*+
63 Choncho, bwanamkubwa* anawauza kuti asamadye zinthu zopatulika koposa,+ mpaka patakhala wansembe amene angagwiritse ntchito Urimu ndi Tumimu.+
64 Anthu onse analipo 42,360.+
65 Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi aakazi amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi okwana 200.
66 Anali ndi mahatchi* 736 ndi nyulu* 245.
67 Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720.
68 Atsogoleri ena a nyumba za makolo awo atafika kunyumba ya Yehova imene inali ku Yerusalemu, anapereka zopereka zaufulu+ kunyumba ya Mulungu woona kuti imangidwenso pamalo ake.+
69 Mogwirizana ndi chuma chawo, anapereka zinthu zoti zithandize pa ntchitoyo. Anapereka madalakima* agolide 61,000, ma mina*+ asiliva 5,000 ndi mikanjo 100 ya ansembe.
70 Ndiyeno ansembe, Alevi, anthu ena, oimba, alonda apageti, atumiki apakachisi* ndi Aisiraeli onse anayamba kukhala mʼmizinda yawo.+
Mawu a M'munsi
^ Nʼkutheka kuti chinali chigawo cha ku Babulo kapena cha ku Yuda.
^ Nʼkutheka kuti akunena za “Yoswa” yemwe akutchulidwa pa Hag 1:1 ndi Zek 3:1.
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “anawachotsa pa udindo wokhala ansembe chifukwa anali odetsedwa.”
^ Kapena kuti, “Tirisata.” Dzinali ndi la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.
^ Ena amati “mahosi.”
^ “Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
^ “Dalakima” imeneyi inali yofanana ndi ndalama yagolide ya ku Perisiya yotchedwa dariki, yomwe inkalemera magalamu 8.4. Koma si yofanana ndi dalakima yomwe imatchulidwa mʼMalemba a Chigiriki. Onani Zakumapeto B14.
^ “Mina” yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi inkalemera magalamu 570. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”