Ezekieli 20:1-49

  • Mbiri ya kupanduka kwa Isiraeli (1-32)

  • Aisiraeli analonjezedwa kuti adzabwerera kwawo (33-44)

  • Ulosi wokhudza mbali yakumʼmwera (45-49)

20  Mʼchaka cha 7, mʼmwezi wa 5, pa tsiku la 10 la mweziwo, akuluakulu ena a Isiraeli anabwera nʼkudzakhala pansi pafupi ndi ine kuti adzafunsire kwa Yehova. 2  Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: 3  “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi akuluakulu a Isiraeliwo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi mwabwera kudzafunsira kwa ine? ‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindikuyankhani,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’ 4  Kodi wakonzeka kuti uwaweruze? Kodi wakonzeka kuwaweruza, iwe mwana wa munthu? Auze zinthu zonyansa zimene makolo awo anachita.+ 5  Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pa tsiku limene ndinasankha Isiraeli,+ ndinalumbiranso* kwa ana* a Yakobo ndipo ndinawachititsa kuti andidziwe mʼdziko la Iguputo.+ Inde, ndinalumbira kwa iwo nʼkunena kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ 6  Pa tsiku limenelo ndinalumbira kuti ndidzawatulutsa mʼdziko la Iguputo nʼkupita nawo kudziko limene ndinawasankhira,* dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Linali dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse. 7  Kenako ndinawauza kuti, ‘Aliyense wa inu ataye zinthu zonyansa zimene akuzitumikira. Musadziipitse ndi mafano onyansa* a ku Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+ 8  Koma iwo anandipandukira ndipo sanafune kundimvera. Iwo sanataye zinthu zonyansa zimene ankazitumikira ndipo sanasiye kulambira mafano onyansa a ku Iguputo.+ Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuti ndiwatsanulire mkwiyo wanga komanso kuwaonetsa ukali wanga wonse mʼdziko la Iguputo. 9  Koma ndinachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina kumene ankakhalako.+ Chifukwa ndinachititsa kuti iwo* andidziwe pamaso pa anthu a mitundu inawo pamene ndinawatulutsa* mʼdziko la Iguputo.+ 10  Choncho ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo nʼkuwalowetsa mʼchipululu.+ 11  Kenako ndinawapatsa malamulo anga ndi kuwadziwitsa zigamulo zanga+ kuti munthu amene akuzitsatira akhale ndi moyo.+ 12  Ndinawapatsanso sabata langa+ kuti likhale chizindikiro pakati pa ine ndi iwowo.+ Ndinachita zimenezi nʼcholinga choti adziwe kuti ine Yehova, ndi amene ndikuwachititsa kuti akhale opatulika. 13  Koma a nyumba ya Isiraeli anandipandukira mʼchipululu.+ Iwo sanatsatire malamulo anga ndipo anakana zigamulo zanga zimene munthu akamazitsatira, zimamuthandiza kuti akhale ndi moyo. Sabata langa analidetsa kwambiri. Choncho ndinatsimikiza mtima kuti ndiwatsanulire mkwiyo wanga mʼchipululu kuti onse ndiwawonongeretu.+ 14  Ndinachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo.+ 15  Ndinalumbiranso kwa iwo mʼchipululu kuti sindidzawalowetsa mʼdziko limene ndinawapatsa,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi+ komanso lokongola kwambiri kuposa mayiko onse. 16  Ndinachita zimenezi chifukwa anakana zigamulo zanga, sanatsatire malamulo anga ndipo anadetsa sabata langa popeza anatsimikiza mtima kuti azilambira mafano awo onyansa.+ 17  Koma ndinawamvera chisoni ndipo sindinawawononge. Sindinawaphe onse mʼchipululu. 18  Ndinauza ana awo mʼchipululu+ kuti, ‘Musamatsatire malamulo a makolo anu+ kapena kusunga zigamulo zawo kapenanso kudziipitsa ndi mafano awo onyansa. 19  Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Muzitsatira malamulo anga ndipo muzisunga zigamulo zanga komanso kuzitsatira.+ 20  Muzisunga sabata langa kuti likhale lopatulika+ ndipo lidzakhala chizindikiro pakati pa ine ndi inu, kuti mudziwe kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+ 21  Koma anawo anayamba kundipandukira.+ Sanatsatire malamulo anga ndipo sanasunge komanso kutsatira zigamulo zanga, zimene ngati munthu atazitsatira zingamuthandize kuti akhale ndi moyo. Iwo anadetsa sabata langa. Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuti ndiwatsanulire mkwiyo wanga komanso kuwaonetsa ukali wanga wonse mʼchipululu.+ 22  Koma sindinatero+ ndipo ndinachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa+ kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo. 23  Komanso ndinalumbira kwa iwo mʼchipululu kuti ndidzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndiponso kuwamwaza mʼmayiko osiyanasiyana,+ 24  chifukwa sanatsatire zigamulo zanga, anakana malamulo anga,+ anadetsa sabata langa ndiponso ankalambira mafano onyansa a makolo awo.+ 25  Komanso ndinawasiya kuti azitsatira malamulo oipa ndi zigamulo zimene sizikanawathandiza kuti akhale ndi moyo.+ 26  Ndinawasiya kuti adziipitse ndi nsembe zawo pamene ankaponya pamoto mwana aliyense woyamba kubadwa.+ Ndinachita zimenezi kuti ndiwawononge nʼcholinga choti adziwe kuti ine ndine Yehova.”’ 27  Choncho iwe mwana wa munthu, lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Makolo anu nawonso anandinyoza pondichitira zinthu mosakhulupirika. 28  Ine ndinawalowetsa mʼdziko limene ndinalumbira kuti ndidzawapatsa.+ Koma ataona mapiri onse ataliatali ndi mitengo ya masamba ambiri,+ anayamba kupereka nsembe zawo ndi zopereka zawo zimene sizinkandisangalatsa. Anapereka kafungo kosangalatsa* ka nsembe zawo ndiponso kuthira nsembe zawo zachakumwa pamalo amenewo. 29  Choncho ndinawafunsa kuti, ‘Kodi mumakachita chiyani kumalo okwezeka kumene mumapitako? (Malowo akudziwikabe kuti Malo Okwezeka mpaka lero.)’”’+ 30  Tsopano uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu mukudziipitsa ngati mmene makolo anu anachitira potumikira mafano awo onyansa komanso kuwalambira.*+ 31  Ndipo mukupitiriza kudziipitsa mpaka lero popereka nsembe kwa mafano anu onse onyansa nʼkumawotcha ana anu pamoto.+ Ndiye kodi pa nthawi imodzimodziyo ndiyankhe zimene mukufunsa, inu a nyumba ya Isiraeli?”’+ ‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindiyankha zimene mukufunsazo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 32  ‘Ndipo zimene mukuganiza zakuti: “Tiyeni tikhale ngati anthu a mitundu ina. Tikhale ngati mabanja amʼmayiko ena amene amalambira* mitengo ndi miyala,”+ sizichitika.’ 33  ‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘Ine ndidzakulamulirani monga mfumu yanu. Ndidzakulamulirani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi mkwiyo wosefukira.+ 34  Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ya anthu ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumayiko amene munabalalikirako. Ndidzakusonkhanitsani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi mkwiyo wosefukira.+ 35  Ndidzakulowetsani mʼchipululu cha mitundu ya anthu ndipo kumeneko ndidzakuimbani mlandu pamasomʼpamaso.+ 36  Ndidzakuimbani mlandu mofanana ndi mmene ndinaimbira mlandu makolo anu mʼchipululu chamʼdziko la Iguputo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 37  ‘Ndidzakudutsitsani pansi pa ndodo ya mʼbusa+ ndipo ndidzachititsa kuti musunge pangano. 38  Koma ndidzachotsa anthu opanduka komanso amene akundichimwira pakati panu.+ Chifukwa ndidzawatulutsa mʼdziko limene akukhalamo monga alendo, koma sadzalowa mʼdziko la Isiraeli,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’ 39  Inu a nyumba ya Isiraeli, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Pitani, aliyense wa inu akatumikire mafano ake onyansa.+ Koma mudziwe kuti ngati simuyamba kundimvera, nthawi idzafika ndipo simudzathanso kudetsa dzina langa loyera popereka nsembe zanu ndiponso polambira mafano anu onyansa.’+ 40  ‘Nyumba yonse ya Isiraeli idzanditumikira mʼphiri langa loyera,+ phiri lalitali lamʼdziko la Isiraeli,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Kumeneko ndidzasangalala nanu ndipo ndidzafuna kuti mundibweretsere zopereka zanu komanso nsembe zanu zabwino kwambiri za zinthu zanu zonse zopatulika.+ 41  Chifukwa cha kafungo kosangalatsa,* ndidzasangalala nanu ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina nʼkukusonkhanitsani pamodzi kuchokera mʼmayiko osiyanasiyana kumene munabalalikira.+ Komanso ndidzakusonyezani kuti ndine woyera ndipo anthu a mitundu ina adzaona zimenezi.+ 42  Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ ndikadzakulowetsani mʼdziko la Isiraeli+ limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu. 43  Kumeneko mudzakumbukira khalidwe lanu ndi zonse zomwe munkachita nʼkudziipitsa nazo+ ndipo mudzanyansidwa chifukwa cha zoipa zonse zimene munachita.+ 44  Kenako mudzadziwa kuti ine ndine Yehova ndikadzakuchitirani zimenezi chifukwa cha dzina langa+ osati mogwirizana ndi khalidwe lanu loipa kapena zinthu zoipa zimene munkachita, inu a nyumba ya Isiraeli,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 45  Ndiyeno Yehova anandiuzanso kuti: 46  “Iwe mwana wa munthu, yangʼana mbali yakumʼmwera ndipo ulankhule zokhudza kumeneko. Ulosere zokhudza nkhalango ya dziko lakumʼmwera. 47  Uuze nkhalango yakumʼmwerayo kuti, ‘Imva mawu a Yehova. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikukuyatsa ndi moto.+ Motowo udzawotcha mtengo uliwonse wauwisi ndi mtengo uliwonse wouma umene uli mwa iwe. Malawi a motowo sadzazimitsidwa+ ndipo nkhope iliyonse, kuchokera kumʼmwera mpaka kumpoto idzapsa ndi moto. 48  Anthu onse adzaona kuti ine Yehova ndayatsa nkhalangoyo ndi moto ndipo sudzazimitsidwa.”’”+ 49  Ine ndinanena kuti: “Mayo ine, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Iwo akundinena kuti, ‘Kodi si miyambi imene akunenayi?’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinakweza dzanja langa.”
Kapena kuti, “ndinaliyendera kuti iwo akakhalemo.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kutanthauza Aisiraeli.
Kutanthauza Aisiraeli.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “kuchita uhule ndi mafanowo.”
Kapena kuti, “amatumikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”