Genesis 24:1-67
24 Tsopano Abulahamu anali atakalamba ndipo anali ndi zaka zambiri. Yehova anali atamudalitsa mʼchilichonse.+
2 Ndiyeno Abulahamu anauza mtumiki wake, yemwe anali wamkulu kwambiri mʼnyumba yake komanso woyangʼanira zinthu zake zonse+ kuti: “Chonde, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.
3 Ndikufuna ulumbire pali Yehova, Mulungu wakumwamba ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti sutengera mwana wanga mkazi pakati pa ana aakazi a Akanani, amene ndikukhala mʼdziko lawo.+
4 Mʼmalomwake, upite kudziko lakwathu kwa abale anga,+ ndipo kumeneko ukamutengere mkazi Isaki mwana wanga.”
5 Koma mtumikiyo anamufunsa kuti: “Bwanji ngati mkaziyo atakana kubwera nane kuno? Kodi ndidzatenge mwana wanuyu nʼkumubwezera kudziko limene munachokera?”+
6 Pamenepo Abulahamu anayankha kuti: “Ayi, usadzatenge mwana wanga nʼkupita naye kumeneko.+
7 Yehova Mulungu wakumwamba, amene ananditenga kunyumba kwa bambo anga ndi kudziko la abale anga,+ amenenso analankhula nane nʼkulumbira kwa ine+ kuti: ‘Ndidzapereka dziko+ ili kwa mbadwa* zako,’+ ameneyo atumiza mngelo wake kuti akutsogolere,+ ndipo ndithu ukamʼtengere mkazi mwana wanga kumeneko.+
8 Koma ngati mkaziyo angakakane kubwera nawe, iweyo udzamasuka pa lumbiro limeneli. Koma sindikufuna kuti udzatenge mwana wanga nʼkupita naye kumeneko.”
9 Atatero, mtumikiyo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu ya Abulahamu mbuye wake nʼkulumbira kwa iye pa nkhani imeneyi.+
10 Choncho mtumikiyo anatenga ngamila 10 pa ngamila za mbuye wake. Anatenganso zinthu zabwino zosiyanasiyana kwa mbuye wake. Kenako ananyamuka ulendo wopita ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
11 Atafika, anagwaditsa pansi ngamilazo pachitsime cha madzi chimene chinali kunja kwa mzindawo. Anafika chakumadzulo, nthawi imene akazi ankatuluka mumzindamo kukatunga madzi.
12 Ndiyeno mtumikiyo anati: “Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abulahamu, chonde ndithandizeni kuti lero zinthu zindiyendere bwino, ndipo musonyeze chikondi chanu chokhulupirika kwa mbuye wanga Abulahamu.
13 Ndaima pano pakasupe wa madzi, ndipo ana aakazi amumzindawu akubwera kudzatunga madzi.
14 Zichitike kuti, mtsikana amene ndimuuze kuti, ‘Chonde tula pansi mtsuko wako wa madzi kuti ndimweko,’ ndipo iye nʼkundiyankha kuti, ‘Imwani, ndiponso nditungira madzi ngamila zanu kuti zimwe,’ ameneyo akhale amene mwasankhira mtumiki wanu Isaki. Mukachita zimenezo, ndidziwa kuti mwasonyeza chikondi chokhulupirika kwa mbuye wanga.”
15 Asanamalize nʼkomwe kulankhula, anangoona Rabeka mwana wa Betuele+ akutuluka mumzindawo. Betuele anali mwana wa Milika,+ ndipo Milika anali mkazi wa Nahori,+ mchimwene wake wa Abulahamu. Rabekayo anali atanyamula mtsuko paphewa pake.
16 Mtsikanayo anali wokongola mochititsa kaso, ndipo anali namwali amene anali asanagonepo ndi mwamuna. Iye analowa mʼchitsimemo nʼkutungira madzi mumtsuko wake, kenako anatulukamo.
17 Nthawi yomweyo mtumiki wa Abulahamuyo anamuthamangira nʼkumuuza kuti: “Chonde ndipatse madzi amumtsuko wako ndimweko pangʼono.”
18 Rabekayo anayankha kuti: “Eni, imwani mbuyanga.” Atatero anatula mtsuko wake mwamsanga nʼkuupendeketsa kuti mtumikiyo amwe.
19 Atamaliza kupereka madzi akumwawo, anati: “Nditungiranso madzi ngamila zanu mpaka zitamwa mokwanira.”
20 Choncho, iye mwamsanga anakhuthulira madzi amene anali mumtsuko aja muchomweramo ziweto. Kenako anayamba kuthamanga mobwerezabwereza kukatunga madzi ena pachitsimepo mpaka ngamila zonse za mlendoyo zitamwa mokwanira.
21 Nthawi yonseyi nʼkuti munthu uja akungomuyangʼana modabwa osanena chilichonse, kuti aone ngati Yehova wapangitsadi kuti pa ulendo wakewo, zinthu ziyende bwino kapena ayi.
22 Ngamila zija zitamaliza kumwa, mlendoyo anatenga ndolo yagolide yovala pamphuno yolemera hafu ya sekeli,* ndi zibangili ziwiri zagolide zolemera masekeli 10 nʼkumupatsa Rabeka.
23 Kenako anamufunsa kuti: “Chonde ndiuze, kodi ndiwe mwana wa ndani? Kodi kunyumba kwa bambo ako kuli malo oti tikhoza kugonako?”
24 Iye anayankha kuti: “Ine ndine mwana wa Betuele.+ Bambo angawo mayi awo ndi Milika, bambo awo ndi Nahori.”+
25 Ananenanso kuti: “Chakudya cha ziweto tili nacho chambiri, komanso malo ogona alipo.”
26 Kenako mwamunayo anagwada pansi nʼkuwerama pamaso pa Yehova
27 nʼkunena kuti: “Atamandike Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abulahamu, chifukwa sanasiye kusonyeza mbuye wanga chikondi chokhulupirika komanso nthawi zonse amakwaniritsa zimene wamulonjeza. Yehova wanditsogolera kunyumba kwa abale a mbuye wanga.”
28 Ndiyeno mtsikanayo anathamangira kunyumba kwa mayi ake nʼkufotokozera onse zimenezi.
29 Rabeka anali ndi mchimwene wake dzina lake Labani.+ Choncho Labani anathamanga kupita kwa munthu uja, yemwe anali kuchitsime, kunja kwa mzinda.
30 Labani ataona ndolo ya pamphuno ndi zibangili pamikono ya mchemwali wake, ndiponso atamva mawu a mchemwali wake Rabeka akuti: “Munthuyo anandiuza zakutizakuti,” Labaniyo anapita kwa munthuyo ndipo anamupeza ataima pafupi ndi ngamila zija pachitsimepo.
31 Atangomuona anamuuza kuti: “Tabwerani, inu wodalitsika wa Yehova. Bwanji mwangoima kunja kuno? Inetu ndakonza kale malo kunyumbaku, a inu ndi a ngamilazi.”
32 Munthuyo atamva zimenezo, anapita nʼkukalowa mʼnyumbamo. Kenako Labani anamasula ngamila nʼkuzipatsa chakudya. Anatenganso madzi nʼkusambitsa mapazi a mlendoyo ndi mapazi a anyamata omwe anali nawo.
33 Kenako anamubweretsera chakudya, koma iye anati: “Sindidya pokhapokha nditanena chimene ndabwerera.” Choncho Labani anati: “Ndiye lankhulanitu!”
34 Iye anati: “Ine ndine mtumiki wa Abulahamu.+
35 Yehova wamudalitsa kwambiri mbuye wanga ndipo wamupatsa chuma chambiri moti ali ndi nkhosa, ngʼombe, siliva, golide, antchito aamuna ndi aakazi komanso ngamila ndi abulu.+
36 Ndiponso Sara mkazi wake anamuberekera mbuye wangayo mwana wamwamuna, Sarayo atakalamba.+ Mbuye wanga adzamupatsa mwanayo zonse zimene ali nazo.+
37 Choncho mbuye wangayo anandilumbiritsa kuti, ‘Usatengere mwana wanga mkazi pakati pa ana aakazi a Chikananiwa amene ndikukhala mʼdziko lawo.+
38 Usachite zimenezo, koma upite kubanja la bambo anga, kwa abale anga,+ ukamʼtengere mkazi mwana wanga.’+
39 Koma ineyo ndinafunsa mbuye wanga kuti, ‘Bwanji ngati mkaziyo atakana kubwera nane?’+
40 Iye anandiyankha kuti: ‘Yehova, amene ndakhala ndikuyenda pamaso pake+ movomerezeka, atumiza mngelo+ wake kuti apite nawe limodzi, ndipo akakuthandiza kuti zimene ukuyenderazo zikatheke. Kumeneko, ukamʼtengere mkazi mwana wanga, kwa abale anga, kubanja la bambo anga.+
41 Udzamasuka ku lumbiro limene wachitali ngati utapita kwa abale anga koma iwo nʼkukana kukupatsa mkazi. Zikatero udzamasuka ku lumbiro limene wachitali.’+
42 Nditafika kuchitsime lero, ndinati: ‘Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abulahamu, ngati mundithandizedi kuti zimene ndayendera zitheke, pachitike zinthu izi:
43 Mtsikana+ amene abwere pachitsime ndaima pano kuchokera mumzindawu kudzatunga madzi, ine nʼkumuuza kuti, “Chonde, ndimweko pangʼono madzi amumtsuko wakowo,”
44 iye nʼkundiyankha kuti, “Imwani, ndiponso nditungira madzi ngamila zanu kuti zimwe.” Ameneyo akhale mkazi amene Yehova wasankhira mwana wa mbuye wanga.’+
45 Ndisanamalize nʼkomwe kulankhula mumtima mwanga, ndinangoona Rabeka akutuluka mumzindawu, atanyamula mtsuko wake paphewa. Iye analowa mʼchitsime nʼkuyamba kutunga madzi. Kenako ndinamupempha kuti, ‘Chonde undigaireko madzi ndimwe.’+
46 Mwamsanga iye anatula mtsuko wake umene unali paphewa lake nʼkundiuza kuti: ‘Imwani,+ ndipo nditungiranso ngamila zanu kuti zimwe.’ Choncho ndinamwa madziwo, ndipo anatungiranso ngamila kuti zimwe.
47 Atachita zimenezi ndinamufunsa kuti, ‘Kodi ndiwe mwana wa ndani?’ Iye anandiyankha kuti, ‘Ine bambo anga ndi a Betuele. Bambo awo ndi a Nahori, ndipo mayi awo ndi a Milika.’ Ndiyeno ndinamuveka ndolo pamphuno ndi zibangili mʼmikono yake.+
48 Kenako ndinagwada nʼkuwerama pamaso pa Yehova. Ndinatamanda Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abulahamu,+ amene wanditsogolera panjira yoyenera, kuti ndidzatengere mkazi mwana wa mbuye wanga kwa mʼbale wake.
49 Tsopano ndiuzeni ngati mukufuna kusonyeza mbuye wanga chikondi komanso kukhala okhulupirika kwa iye. Koma ngati simukufuna, mundiuzenso kuti ndikayangʼane kwina.”*+
50 Ndiyeno Labani ndi Betuele anamuyankha kuti: “Zimenezi zachokera kwa Yehova. Ife sitingathe kukuvomerani kapena kukukanizani.*
51 Rabeka ndi ameneyu. Mʼtengeni muzipita naye, ndipo akakhale mkazi wa mwana wa mbuye wanu mogwirizana ndi zimene Yehova wanena.”
52 Mtumiki wa Abulahamu atamva zimenezi, nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa Yehova.
53 Kenako mtumikiyo anayamba kutulutsa zinthu zasiliva, zagolide ndi zovala nʼkupatsa Rabeka. Anaperekanso zinthu zamtengo wapatali kwa mchimwene wake wa Rabeka ndi kwa mayi ake.
54 Pambuyo pake, iye limodzi ndi anyamata ake anadya ndi kumwa, ndipo anagona komweko.
Atadzuka mʼmawa, mtumiki wa Abulahamu uja anati: “Ndiloleni ndizipita kwa mbuye wanga.”
55 Koma mchimwene wa mtsikanayo ndi mayi ake anati: “Bwanji mtsikanayu akhalebe nafe masiku 10 okha, kenako akhoza kupita.”
56 Iye anawauza kuti: “Musandichedwetse, chifukwa Yehova wandithandiza kukwaniritsa zimene ndayendera. Ndiloleni ndizipita kwa mbuye wanga.”
57 Choncho iwo anati: “Tiyeni timuitane mtsikanayo kuti timve maganizo ake.”
58 Ndiyeno anaitana Rabekayo nʼkumufunsa kuti: “Kodi upita naye limodzi munthuyu?” Iye anayankha kuti: “Eya ndipita.”
59 Choncho iwo analola kuti mchemwali wawo Rabeka+ ndi mlezi* wake,+ apite limodzi ndi mtumiki wa Abulahamuyo ndi anyamata ake.
60 Ndiyeno iwo anadalitsa Rabeka kuti: “Iwe mchemwali wathu, ukakhale mayi wa anthu masauzande kuchulukitsa ndi masauzande 10, ndipo mbadwa* zako zikalande mizinda ya adani awo.”+
61 Kenako Rabeka ndi atumiki ake aakazi ananyamuka nʼkukwera ngamila kumapita limodzi ndi mtumiki wa Abulahamu uja. Choncho mtumikiyo anatenga Rabeka nʼkupita naye.
62 Isaki ankakhala mʼdziko la Negebu.+ Ndiye tsiku lina, akuyenda panjira yochokera ku Beere-lahai-roi,+
63 analowa patchire madzulo kuti akasinkhesinkhe.+ Atakweza maso, anaona ngamila zikubwera poteropo!
64 Nayenso Rabeka atakweza maso anaona Isaki, ndipo mwamsanga anatsika pangamila.
65 Ndiye anafunsa mtumiki uja kuti: “Kodi munthu akubwera apoyo kuchokera mʼtchire kudzakumana nafe ndi ndani?” Mtumikiyo anayankha kuti: “Ameneyo ndi mbuye wanga.” Choncho iye anatenga nsalu yophimba kumutu nʼkudziphimba nayo.
66 Kenako mtumikiyo anafotokozera Isaki zonse zimene anachita.
67 Ndiyeno Isaki analowa ndi mkaziyo mutenti ya Sara, mayi ake.+ Choncho Isaki anatenga Rabeka kukhala mkazi wake. Iye anamʼkonda kwambiri,+ ndipo zimenezi zinamutonthoza pambuyo pa imfa ya mayi ake.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti nditembenukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.”
^ Kapena kuti, “sitingathe kulankhula zoipa kapena zabwino kwa inu.”
^ Mlezi ndi wantchito wamkazi amene amalera mwana. Choncho mlezi wa Rabekayu anamulera ali mwana, ndipo atakula mleziyu anakhala mtumiki wake.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”