Genesis 3:1-24

  • Kuchimwa kwa munthu (1-13)

  • Chiweruzo chimene Yehova anapereka kwa opanduka (14-24)

    • Ananeneratu za mbadwa ya mkazi  (15)

    • Anathamangitsidwa mu Edeni (23, 24)

3  Tsopano njoka+ inali yochenjera kwambiri kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: “Eti nʼzoona kuti Mulungu ananena kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse wamʼmundamu?”+ 2  Mkaziyo anayankha njokayo kuti: “Anatiuza kuti tingathe kudya zipatso za mitengo yamʼmundamu.+ 3  Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda,+ Mulungu ananena kuti: ‘Musadye zipatso zake, ndipo musayerekeze kuukhudza, chifukwa mukatero mudzafa.’” 4  Kenako njokayo inauza mkaziyo kuti: “Si zoona zimenezo, simudzafa ayi.+ 5  Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”+ 6  Mkaziyo atamva zimenezo, anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo nʼzokoma kudya, zosiririka komanso zooneka bwino. Choncho anathyola chipatso cha mtengowo nʼkudya.+ Kenako anatenga zina nʼkukapatsa mwamuna wake pa nthawi imene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.+ 7  Atatero onse maso awo anatseguka ndipo anazindikira kuti ali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nʼkuwamangirira mʼchiuno mwawo.+ 8  Pambuyo pake, iwo anamva mawu a Yehova Mulungu pamene iye ankayendayenda mʼmundamo pa nthawi imene kamphepo kayeziyezi kankaomba. Mwamuna ndi mkaziyo atamva, anabisala pakati pa mitengo ya mʼmundamo kuti Yehova Mulungu asawaone. 9  Koma Yehova Mulungu anapitiriza kuitana mwamunayo kuti: “Kodi uli kuti?” 10  Kenako mwamunayo anayankha kuti: “Ndinamva kuitana kwanu mʼmunda muno, koma ndinachita mantha poona kuti ndili maliseche. Choncho ndinabisala.” 11  Ndiyeno Mulungu anati: “Wakuuza ndi ndani kuti uli maliseche?+ Kodi wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti usadzadye uja?”+ 12  Mwamunayo anayankha kuti: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.” 13  Ndiyeno Yehova Mulungu anafunsa mkaziyo kuti: “Ndiye chiyani wachitachi?” Mkaziyo anayankha kuti: “Njoka ndi imene yandipusitsa, ndipo ine ndadya.”+ 14  Zitatero Yehova Mulungu anauza njokayo kuti:+ “Chifukwa cha zimene wachitazi, ukhala wotembereredwa pa nyama zonse zoweta ndi zakutchire. Udzakwawa ndi mimba yako ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako. 15  Ndidzaika chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ komanso pakati pa mbadwa* yako+ ndi mbadwa yake.+ Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”+ 16  Ndiyeno Mulungu anauza mkaziyo kuti: “Ndidzawonjezera kwambiri kuvutika kwako pa nthawi imene uli woyembekezera. Ndipo pobereka ana udzamva ululu. Uzidzafunitsitsa kukhala ndi mwamuna wako, ndipo iye azidzakulamulira.” 17  Kenako Mulungu anauza Adamu* kuti: “Popeza wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti,+ ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi.+ Udzavutika kulima nthakayo masiku onse a moyo wako+ kuti upeze chakudya. 18  Minga ndi zitsamba zobaya zidzamera panthaka, ndipo chakudya chako chidzakhala zomera zamʼnthaka. 19  Udzadya chakudya kuchokera mʼthukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, chifukwa nʼkumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+ 20  Pambuyo pa zimenezi, Adamu anapatsa mkazi wake dzina lakuti Hava,* chifukwa anali woti adzakhala mayi wa anthu onse.+ 21  Kenako Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zazitali zachikopa, nʼkuwaveka.+ 22  Ndiyeno Yehova Mulungu anati: “Tsopano munthu wakhala ngati ife chifukwa wadziwa zabwino ndi zoipa.+ Choncho kuti asathyolenso ndi kudya chipatso cha mtengo wa moyo,+ nʼkukhala ndi moyo mpaka kalekale,—”* 23  Atatero Yehova Mulungu anatulutsa munthuyo mʼmunda wa Edeni,+ kuti akalime nthaka imene anatengedwako.+ 24  Choncho anathamangitsa munthuyo mʼmundamo, nʼkuika akerubi+ kumʼmawa kwa munda wa Edeniwo. Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linkazungulira nthawi zonse, kutchinga njira yopita kumtengo wa moyo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.” Mawuwa mʼChiheberi angatanthauze mbewu zambiri kapena imodzi.
Kutanthauza kuti “Munthu Wochokera Kufumbi; Mtundu wa Anthu.”
Dzina limeneli limatanthauza “Wamoyo.”
Kamzere kameneka kakusonyeza kuti mawuwa anathera mʼmalere.