Genesis 31:1-55

  • Yakobo anachoka ku Kanani mozemba (1-18)

  • Labani anapezana ndi Yakobo (19-35)

  • Pangano la Yakobo ndi Labani (36-55)

31  Patapita nthawi, Yakobo anamva zimene ana aamuna a Labani ankanena kuti: “Yakobo watenga zinthu zonse za bambo athu, ndipo chuma chonse chimene ali nachochi chachokera kwa bambo athu.”+ 2  Yakobo akayangʼana nkhope ya Labani ankaona kuti sakumuyangʼana ndi diso labwino ngati poyamba.+ 3  Kenako Yehova anauza Yakobo kuti: “Bwerera kudziko la makolo ako ndi kwa abale ako,+ ndipo ine ndidzapitiriza kukuthandiza.” 4  Ndiyeno Yakobo anaitanitsa Rakele ndi Leya kuti abwere kubusa kumene iye anali ndi nkhosa zake. 5  Iye anawauza kuti: “Ndikuona kuti bambo anu sakundiyangʼana ndi diso labwino ngati poyamba,+ koma Mulungu wa bambo anga sanandisiye.+ 6  Inunso mukudziwa bwino kuti bambo anu ndawagwirira ntchito ndi mphamvu zanga zonse.+ 7  Koma bambo anu akhala akundipusitsa, ndipo asintha malipiro anga maulendo 10. Ngakhale zili choncho, Mulungu sanawalole kuti andichitire zoipa. 8  Nthawi zonse akanena kuti, ‘Zamawangamawanga ndi zimene zidzakhale malipiro ako,’ ziweto zonse zinkabereka zamawangamawanga. Akanena kuti, ‘Zamizeremizere ndi zimene zidzakhale malipiro ako,’ ziweto zonse zinkabereka zamizeremizere.+ 9  Choncho Mulungu ankachotsa ziweto kwa bambo anu nʼkuzipereka kwa ine. 10  Pa nthawi imene ziweto zinali zokonzeka kutenga bere, ndinalota maloto ndipo ndinaona mbuzi zamphongo zikukwera zazikazi. Mbuzi zamphongozo zinali zamizeremizere, zamawangamawanga ndi zamathothomathotho.+ 11  Kenako, mngelo wa Mulungu woona anandiitana mʼmalotowo kuti, ‘Yakobo!’ Ine ndinayankha kuti, ‘Ine Ambuye.’ 12  Iye anapitiriza kuti, ‘Kweza maso ako ndipo uona kuti mbuzi zonse zamphongo zimene zikukwera zazikazizi ndi zamizeremizere, zamawangamawanga ndiponso zamathothomathotho. Ndachita zimenezi chifukwa ndaona zonse zimene Labani akukuchitira.+ 13  Ndine Mulungu woona wa ku Beteli+ kumene unadzoza mwala wachikumbutso kuja, kumenenso unachita lonjezo kwa ine.+ Tsopano nyamuka, uchoke kudziko lino, ubwerere kudziko limene unabadwira.’”+ 14  Pamenepo Rakele ndi Leya anamuyankha kuti: “Kodi ifeyo tatsala ndi cholowa chilichonse mʼnyumba ya bambo athu ngati? 15  Kodi iwowa ife sakutiona ngati alendo? Bambowa anatigulitsa kwa inu ndipo akupitiriza kudya ndalama zimene inu munapereka.+ 16  Chuma chonse chimene Mulungu watenga kwa bambo athuwo ndi chathu ndi cha ana athu.+ Ndiye chilichonse chimene Mulungu wakuuzani, chitani.”+ 17  Kenako Yakobo anakweza ana ake ndi akazi ake pangamila.+ 18  Atatero anayamba kutenga ziweto zake zonse ndi katundu wake yense amene anapeza+ ku Padani-aramu, nʼkunyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani kwa Isaki bambo ake.+ 19  Labani atapita kukameta ubweya wa nkhosa zake, Rakele anaba aterafi*+ a bambo akewo.+ 20  Yakobo anachita zinthu mochenjera chifukwa anachoka kwa Labani wa Chiaramu uja, osamuuza kuti akuchoka. 21  Yakobo anathawa nʼkuwoloka Mtsinje*+ limodzi ndi anthu komanso katundu amene anali naye. Atatero analowera kudera la mapiri la Giliyadi.+ 22  Pa tsiku lachitatu, Labani anauzidwa kuti Yakobo wathawa. 23  Atamva zimenezo, anatenga abale ake* nʼkuyamba kuthamangira Yakobo. Iwo anayenda ulendo wa masiku 7, ndipo anamupeza mʼdera la mapiri la Giliyadi. 24  Koma usiku mʼmaloto,+ Mulungu anafikira Labani wa Chiaramuyo+ nʼkumuuza kuti: “Usamale ndi zimene ukalankhule ndi Yakobo, kaya zabwino kapena zoipa.”+ 25  Kenako Labani anapita kwa Yakobo. Pa nthawiyi nʼkuti Yakobo atamanga tenti yake mʼdera la mapiri la Giliyadi, ndipo Labani ndi abale ake anamanganso tenti yawo mʼdera lomwelo. 26  Ndiyeno Labani anafunsa Yakobo kuti: “Nʼchiyani wachitachi? Nʼchifukwa chiyani wandipusitsa nʼkutenga ana anga aakazi ngati akapolo ogwidwa kunkhondo? 27  Nʼchifukwa chiyani unachoka mozemba osandiuza? Ukanandiuza ndikanatsanzikana nawe mosangalala, tikuimba nyimbo, maseche ndi azeze. 28  Sunandipatse mpata woti ndikise* zidzukulu zanga* ndi ana anga. Zimene wachitazi nʼzopusa. 29  Ndikanatha kukuchitirani zoipa, koma Mulungu wa bambo anu analankhula nane usiku wapitawu kuti, ‘Usamale ndi zimene ukalankhule ndi Yakobo, kaya zabwino kapena zoipa.’+ 30  Wachoka chifukwa umafunitsitsa kubwerera kunyumba kwa bambo ako, koma nʼchifukwa chiyani waba milungu yanga?”+ 31  Yakobo anayankha Labani kuti: “Ndinachoka mozemba chifukwa ndimaopa kuti mundilanda ana anuwa. 32  Aliyense amene mumʼpeze ndi milungu yanu aphedwe. Pamaso pa abale athuwa, fufuzani milungu yanuyo pakatundu amene ndili naye. Mukaipeza muitenge.” Koma Yakobo sanadziwe kuti Rakele anali ataba milunguyo. 33  Choncho Labani anakalowa mutenti ya Yakobo ndi mutenti ya Leya, ndiponso mutenti ya akapolo aakazi awiri aja,+ koma sanaipeze. Potsirizira pake, anatuluka mutenti ya Leya nʼkukalowa mutenti ya Rakele. 34  Rakele anali atatenga aterafi aja nʼkuwabisa mʼchishalo choika pangamila, nʼkuchikhalira. Labani anafunafuna mutenti monsemo koma sanawapeze aterafiwo. 35  Kenako Rakele anauza bambo ake kuti: “Musandikwiyire mbuyanga chifukwa sinditha kunyamuka pano. Kungoti sindili bwino malinga ndi chikhalidwe chathu akazife.”+ Labani anapitiriza kufunafuna mosamala koma sanawapeze aterafiwo.+ 36  Ndiyeno Yakobo anapsa mtima nʼkuyamba kukalipira Labani. Iye anafunsa Labani kuti: “Kodi ndakulakwirani chiyani? Ndipo ndakuchimwirani chiyani kuti muchite kundilondola mokwiya chonchi? 37  Popeza mwafufuza katundu wanga yense, kodi mwapezapo chiyani chamʼnyumba mwanu? Chiikeni apa pamaso pa abale anga ndi abale anu kuti atiweruze. 38  Pa zaka 20 zonsezi zimene ndakhala nanu, nkhosa zanu ndi mbuzi zanu sizinaberekepo mwana wakufa.+ Ndiponso chiyambire sindinadyepo nkhosa yanu yamphongo ngakhale imodzi. 39  Sindinakubweretserenipo nyama iliyonse imene inaphedwa ndi chilombo+ koma ndinkaitenga kuti ikhale yanga. Nyama ikabedwa masana kapena usiku, munkandiuza kuti ndikulipireni. 40  Ndinkangokhalira kupsa ndi dzuwa masana komanso kuzizidwa ndi mphepo usiku, ndipo tulo sindinkationa.+ 41  Ndakhala mʼnyumba mwanu zaka 20. Ndakugwirirani ntchito zaka 14 kuti mundipatse ana anu aakazi awiriwa. Ndinagwiranso ntchito zaka zina 6 kuti mundipatse ziwetozi. Koma inu munkangosintha malipiro anga mpaka maulendo 10.+ 42  Mulungu wa bambo anga,+ Mulungu wa Abulahamu amenenso Isaki ankamuopa,+ akanapanda kukhala kumbali yanga, bwenzi mutandibweza kwathu chimanjamanja. Koma Mulungu waona kusautsika kwanga ndi ntchito zimene ndagwira molimbika, nʼchifukwa chake anakudzudzulani usiku wapitawu.”+ 43  Ndiyeno Labani anamuyankha Yakobo kuti: “Akaziwa ndi ana anga, ana awo ndi ana anga, ziwetozi ndi ziweto zanga, ndipo chilichonse chimene ukuchiona ndi cha ine ndi ana anga aakaziwa. Ndiye kodi lero iwowa kapena ana awo amene anabereka, ndingawachitire choipa? 44  Tiye tichite pangano iwe ndi ine, kuti likhale umboni pakati pa ine ndi iwe.” 45  Choncho Yakobo anatenga mwala nʼkuuimika ngati mwala wachikumbutso.+ 46  Kenako Yakobo anauza abale ake kuti: “Tengani miyala!” Iwo anatenga miyala nʼkuiunjika mulu. Atatero, anadyera chakudya pamulu wamiyalawo. 47  Labani anatchula mulu wamiyalawo kuti Yegara-sahaduta,* koma Yakobo anautchula kuti Galeeda.* 48  Kenako Labani ananena kuti: “Mulu wamiyalawu ndi umboni wathu lero pakati pa ine ndi iwe.” Nʼchifukwa chake anaupatsa dzina lakuti Galeeda,+ 49  ndiponso lakuti Nsanja ya Mlonda, chifukwa Labani ananena kuti: “Yehova apitirize kuyangʼanira iwe ndi ine tikasiyana pano. 50  Ukamakazunza ana angawa ndiponso ukakatenga akazi ena kuwonjezera pa ana angawa, ngakhale kuti palibe munthu amene adzaone,* kumbukira kuti Mulungu ndi mboni pakati pa ine ndi iwe.” 51  Labani anauzanso Yakobo kuti: “Ona mulu wamiyala ndiponso mwala wachikumbutso umene ndaimika monga chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi iwe. 52  Muluwu ndiponso mwala wachikumbutsowu ndi umboni+ pakati pa ine ndi iwe, kuti wina sadzadutsa muluwu ndi mwala wachikumbutsowu kukachitira mnzake zoipa. 53  Mulungu wa Abulahamu+ ndi Mulungu wa Nahori, yemwe ndi Mulungu wa bambo awo, atiweruze.” Ndipo Yakobo analumbira mʼdzina la Mulungu amene bambo ake Isaki ankamuopa.+ 54  Pambuyo pake, Yakobo anapereka nsembe mʼphirimo nʼkuitana abale ake kuti adye chakudya. Choncho iwo anadya chakudya nʼkugona mʼphirimo usiku umenewo. 55  Ndiyeno Labani anadzuka mʼmamawa nʼkukisa zidzukulu*+ zake ndi ana ake aakazi ndipo anawadalitsa.+ Atatero, ananyamuka nʼkubwerera kwawo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “milungu ya banja ya; mafano.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti, “achibale ake.”
Kapena kuti, “ndipsompsone.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anga aamuna.”
Mawu a Chiaramu otanthauza, “Mulu wa Umboni.”
Mawu a Chiheberi otanthauza, “Mulu wa Umboni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngakhale kuti palibe munthu pano.”
Kutanthauza, “ana aamuna.”