Genesis 6:1-22

  • Ana a Mulungu anakwatira akazi padziko lapansi (1-3)

  • Kubadwa kwa Anefili (4)

  • Yehova anamva chisoni chifukwa cha kuipa kwa anthu (5-8)

  • Nowa anapatsidwa ntchito yopanga chingalawa (9-16)

  • Mulungu ananena kuti adzabweretsa chigumula (17-22)

6  Anthu atayamba kuchuluka padziko lapansi, kunabadwa ana ambiri aakazi. 2  Ndiyeno ana a Mulungu woona*+ anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Choncho anayamba kutenga akazi alionse amene ankawafuna nʼkuwakwatira. 3  Kenako Yehova anati: “Ine sindipitiriza* kulezera mtima anthu mpaka kalekale,+ chifukwa ndi ochimwa. Choncho adzangokhala ndi moyo zaka 120 zokha.”*+ 4  Kuyambira masiku amenewo kupita mʼtsogolo, padziko lapansi panali Anefili.* Pa nthawi imeneyo, ana a Mulungu woona anapitiriza kugona ndi ana aakazi a anthu ndipo anawaberekera ana. Anawo anali zianthu zamphamvu zimene zinalipo kalelo, amuna otchuka. 5  Choncho Yehova anaona kuti anthu aipa kwambiri padziko lapansi. Anaona kuti maganizo a anthu komanso zofuna za mtima wawo zinali zoipa zokhazokha nthawi zonse.+ 6  Yehova anamva chisoni kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinamupweteka kwambiri mumtima.+ 7  Choncho Yehova anati: “Ndidzaseseratu padziko lapansi anthu amene ndinawalenga. Ndidzaseseratu anthu, nyama zoweta, nyama zokwawa komanso zamoyo zouluka mumlengalenga, chifukwa ndikumva chisoni kuti ndinazipanga.” 8  Koma Yehova ankasangalala ndi Nowa. 9  Iyi ndi mbiri ya Nowa. Nowa anali munthu wolungama.+ Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a mʼnthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.+ 10  Patapita nthawi, Nowa anabereka ana aamuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.+ 11  Koma dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona, ndipo linadzaza ndi chiwawa. 12  Mulungu anayangʼana dziko lapansi ndipo anaona kuti laipa.+ Anthu onse padziko lapansi ankachita zinthu zoipa.+ 13  Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Ndaganiza zowononga anthu onse, chifukwa apangitsa kuti dziko lapansi lidzaze ndi chiwawa. Choncho ndiwawononga limodzi ndi zonse zimene zili padziko lapansi.+ 14  Upange chingalawa pogwiritsa ntchito matabwa a mtengo wa mnjale.+ Uchigawe zipindazipinda ndipo uchimate ndi phula+ mkati ndi kunja komwe. 15  Uchipange chonchi: Mulitali chikhale mamita 134,* mulifupi mamita 22, ndipo kutalika kwake kuyambira pansi mpaka pamwamba chikhale mamita 13. 16  Chingalawacho uchiikire windo* kuti mkatimo muziwala. Kuchokera kudenga kufika pamene pali windolo pakhale mpata wa masentimita 44 ndi hafu. Khomo la chingalawacho uliike mʼmbali mwake.+ Chikhale ndi zipinda zosanjikiza zitatu, chapansi, chapakati ndi chapamwamba. 17  Ine ndidzabweretsa chigumula+ padziko lapansi kuti chiwononge chamoyo chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mpweya wa moyo* mʼthupi lake. Chilichonse chimene chili padziko lapansi chidzawonongedwa.+ 18  Ndikuchita pangano ndi iwe. Iweyo udzalowe mʼchingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako ndi akazi a ana ako.+ 19  Mʼchingalawacho udzalowetsemo chamoyo cha mtundu uliwonse.+ Udzazilowetse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi,+ kuti zidzasungike zamoyo limodzi ndi iwe. 20  Udzalowe nazo ziwiriziwiri za mtundu uliwonse. Zolengedwa zouluka monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo, nyama zonse zokwawa panthaka monga mwa mitundu yawo, kuti zidzasungike zamoyo.+ 21  Udzasonkhanitse chakudya+ cha mtundu uliwonse nʼkuchilowetsa mʼchingalawamo kuti chidzakhale chakudya chanu ndi cha zinyama.” 22  Ndipo Nowa anachita zonse mogwirizana ndi zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi zomwezo.+

Mawu a M'munsi

Mawu okuluwika a Chiheberi amene akunena za angelo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mzimu wanga supitiriza.”
Zaka 120 zimenezi zinkaimira zaka zimene zinatsala kuti anthu oipa awonongedwe ndi chigumula.
Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Ogwetsa” kutanthauza amene amagwetsa anthu ena. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 300.” Onani Zakumapeto B14.
Mawu a Chiheberi ndi “tsoʹhar.” Anthu ena amaona kuti mawuwa akutanthauza denga lokhala ndi mpata wa masentimita 44 ndi hafu, osati bowo kapena windo loti kuwala kuzilowa.
Kapena kuti, “mzimu wa moyo.”