Hoseya 1:1-11
1 Yehova analankhula ndi Hoseya* mwana wa Beeri mʼmasiku a Uziya,+ Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya+ mafumu a Yuda,+ ndiponso mʼmasiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi+ mfumu ya Isiraeli.
2 Yehova atayamba kulankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anauza Hoseya kuti: “Pita ukakwatire mkazi amene azidzachita uhule* ndipo ukakhale ndi ana ochokera kwa hule. Chifukwa dzikoli lasiyiratu kutsatira Yehova chifukwa cha uhule.”+
3 Choncho Hoseya anapita nʼkukakwatira Gomeri, mwana wa Dibulaimu. Kenako Gomeri anakhala ndi pakati ndipo anamuberekera mwana wamwamuna.
4 Ndiyeno Yehova anauza Hoseya kuti: “Mwanayo umupatse dzina lakuti Yezereeli,* popeza kwatsala nthawi yochepa kuti ndiimbe mlandu nyumba ya Yehu+ chifukwa cha magazi amene Yezereeli anakhetsa. Ndipo ndidzathetsa ufumu wa nyumba ya Isiraeli.+
5 Mʼmasiku amenewo ndidzathyola uta wa Isiraeli mʼchigwa cha Yezereeli.”
6 Kenako Gomeri anakhalanso ndi pakati nʼkubereka mwana wamkazi. Ndiyeno Mulungu anauza Hoseya kuti: “Mwanayo umupatse dzina lakuti Lo-ruhama,* chifukwa sindidzachitiranso chifundo+ anthu a mʼnyumba ya Isiraeli, chifukwa ndidzawathamangitsa.+
7 Koma ndidzachitira chifundo anthu a mʼnyumba ya Yuda+ ndipo Ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.+ Sindidzawapulumutsa ndi nkhondo, uta, lupanga, mahatchi* kapenanso amuna okwera pamahatchi.”+
8 Gomeri atamusiyitsa mwana wake Lo-ruhama kuyamwa, anakhalanso ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna.
9 Ndiyeno Mulungu anati: “Mwanayo umupatse dzina lakuti Lo-ami,* chifukwa inu siinu anthu anga ndipo ine sindidzakhala Mulungu wanu.
10 Ndipo Aisiraeli* adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene munthu sangathe kuuyeza kapena kuuwerenga.+ Ndipo kumene ankauzidwa kuti, ‘Siinu anthu anga,’+ adzauzidwa kuti, ‘Ndinu ana a Mulungu wamoyo.’+
11 Ayuda ndi Aisiraeli adzasonkhanitsidwa pamodzi ndipo adzakhala ogwirizana.+ Iwo adzasankha mtsogoleri mmodzi nʼkutuluka mʼdzikolo chifukwa tsiku limeneli lidzakhala lofunika kwambiri kwa Yezereeli.”+
Mawu a M'munsi
^ Chidule cha dzina lakuti Hoshaiya limene limatanthauza, “Wopulumutsidwa ndi Ya; Ya Wapulumutsa.”
^ Kapena kuti, “chiwerewere.”
^ Kutanthauza “Mulungu Adzadzala Mbewu.”
^ Kutanthauza “Wosasonyezedwa Chifundo.”
^ Ena amati “mahosi.”
^ Kutanthauza, “Si Anthu Anga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”