Hoseya 12:1-14
12 “Efuraimu akudya mphepo.
Akuthamangitsa mphepo yakumʼmawa tsiku lonse.
Iye akuchulukitsa mabodza ndi chiwawa.
Wachita pangano ndi Asuri+ ndipo wapititsa mafuta ku Iguputo.+
2 Pali mlandu umene Yehova akufuna kuimba Yuda.+Adzalanga Yakobo mogwirizana ndi njira zake.Ndipo adzamubwezera mogwirizana ndi zochita zake.+
3 Pamene Yakobo anali mʼmimba anagwira chidendene cha mʼbale wake.+Iye analimbana ndi Mulungu ndi mphamvu zake zonse.+
4 Anapitiriza kulimbana ndi mngelo ndipo anapambana.
Analira komanso anachonderera kuti amudalitse.”+
Mulungu anamupeza ku Beteli ndipo kumeneko Mulungu analankhula nafe.*+
5 Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,+Amakumbukiridwa ndi dzina lakuti Yehova.+
6 “Choncho bwerera kwa Mulungu wako.+Uzisonyeza chikondi chokhulupirika ndi chilungamo,+Ndipo nthawi zonse uziyembekezera Mulungu wako.
7 Koma mʼmanja mwa wamalonda muli masikelo achinyengo.Iye amakonda kuba mwachinyengo.+
8 Efuraimu akupitiriza kunena kuti, ‘Inetu ndalemeradi,+Ndapeza chuma.+
Pa ntchito zanga zonse, palibe amene angapeze cholakwa kapena tchimo.’
9 Koma ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+
Ndidzakuchititsa kukhalanso mʼmatenti,Ngati pa masiku achikondwerero.
10 Ndinalankhula ndi aneneri,+Ndipo ndinawaonetsa masomphenya ambiri.Ndinalankhula mafanizo kudzera mwa aneneri.
11 Ku Giliyadi anthu akuchita zachinyengo*+ ndiponso akulankhula mabodza.
Ku Giligala, akupereka nsembe ngʼombe zamphongo.+Ndipo maguwa awo ansembe ali ngati milu yamiyala mʼmunda.+
12 Yakobo anathawira mʼdera la Aramu.*+Ndipo Isiraeli+ ankagwira ntchito kumeneko kuti apeze mkazi,+Ankalondera nkhosa kuti apeze mkazi.+
13 Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kutulutsa Aisiraeli ku Iguputo,+Ndipo mneneri ankalondera Aisiraeli.+
14 Efuraimu wakhumudwitsa kwambiri Mulungu.+Mlandu wake wamagazi uli pa iyeyo,Ndipo Ambuye adzamubwezera kunyoza kwake.”+
Mawu a M'munsi
^ Ayenera kuti akutanthauza mbadwa za Yakobo.
^ Kapena kuti, “zamatsenga.”
^ Kapena kuti, “Siriya.”