Hoseya 14:1-9
14 “Inu Aisiraeli, bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,+Popeza mwapunthwa chifukwa cha zolakwa zanu.
2 Bwererani kwa Yehova ndi mawu amenewa.Uzani Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni zolakwa zathu.+ Landirani zinthu zathu zabwino,Ndipo tidzakutamandani ndi pakamwa pathu+ ngati mmene tingaperekere nsembe kwa inu ana a ngʼombe amphongo.
3 Dziko la Asuri silidzatipulumutsa.+
Ife sitidzakwera pamahatchi.+Ndipo sitidzauzanso ntchito ya manja athu kuti: “Inu Mulungu wathu!”Chifukwa inu ndi amene mumachitira chifundo mwana wamasiye.’+
4 Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo.+
Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga,+Chifukwa ndasiya kuwakwiyira.+
5 Ine ndidzakhala ngati mame kwa Isiraeli,Ndipo iye adzaphuka ngati maluwa okongola.Mizu yake idzazama ngati mitengo ya ku Lebanoni.
6 Nthambi zake zidzatambalala,Ulemerero wake udzakhala ngati wa mtengo wa maolivi.Ndipo fungo lake lonunkhira lidzakhala ngati la mtengo wa ku Lebanoni.
7 Iwo adzakhalanso mumthunzi wake.
Adzadzala mbewu ndipo adzaphuka ngati mpesa.+
Adzatchuka* ngati vinyo wa ku Lebanoni.
8 Efuraimu adzanena kuti, ‘Mafano alibenso ntchito kwa ine.’+
Ine ndidzamva ndipo ndidzamuyangʼanira.+
Ndidzakhala ngati mtengo wa mkungudza wobiriwira bwino.
Ndipo mudzapeza zipatso kwa ine.”
9 Ndani ali ndi nzeru? Amvetse zinthu zimenezi.
Wochenjera ndani? Adziwe zimenezi.
Njira za Yehova ndi zowongoka.+Ndipo anthu olungama adzayendamo,Koma olakwa adzapunthwa mʼnjira zimenezo.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Adzakumbukiridwa.”