Hoseya 3:1-5
3 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Pita ukayambenso kukonda mkazi amene akukondedwa ndi mwamuna wina ndipo akuchita chigololo.+ Ukamukonde ngati mmene Yehova amakondera Aisiraeli,+ ngakhale kuti iwo amalambira milungu ina+ komanso amakonda makeke a mphesa.”*
2 Choncho ndinagula mkaziyo ndi ndalama zasiliva 15 ndiponso balere wokwana muyezo umodzi ndi hafu wa homeri.*
3 Ndiyeno ndinamuuza kuti: “Ukhala wanga masiku ambiri. Usachite uhule* ndipo usagone ndi mwamuna wina. Inenso sindigona nawe.”
4 Ziyenera kukhala choncho chifukwa chakuti kwa nthawi yaitali Aisiraeli adzakhala opanda mfumu,+ kalonga, nsembe, chipilala chopatulika, efodi+ ndi zifaniziro za aterafi.*+
5 Kenako Aisiraeli adzabwerera nʼkuyamba kufunafuna Yehova Mulungu wawo+ ndi Davide mfumu yawo.+ Iwo adzabwera kwa Yehova akunjenjemera ndipo adzafunafuna ubwino wake mʼmasiku otsiriza.+
Mawu a M'munsi
^ Amenewa ndi makeke amene ankawagwiritsa ntchito polambira milungu yabodza.
^ Homeri imodzi inali yofanana ndi malita 220. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “chiwerewere.”
^ Kapena kuti, “milungu ya banja; mafano.”