Hoseya 4:1-19
4 Tamverani mawu a Yehova inu Aisiraeli.Yehova ali ndi mlandu ndi anthu amʼdzikoli,+Chifukwa mʼdzikoli mulibe choonadi, chikondi chokhulupirika ndipo anthu ake sadziwa Mulungu.+
2 Kulumbira monama, bodza,+ kuphana,+Kuba ndi chigololo+ zafala mʼdzikoli.Ndipo kukhetsa magazi kukuchitika pafupipafupi.+
3 Nʼchifukwa chake dzikoli lidzalira maliro,+Ndipo aliyense wokhala mmenemo adzalefukiratu.Nyama zakutchire ndi mbalame zamumlengalenga,Ngakhalenso nsomba zamʼnyanja, zidzafa.
4 “Komabe, munthu asakutsutseni kapena kukudzudzulani,+Chifukwa muli ngati anthu otsutsana ndi wansembe.+
5 Choncho mudzapunthwa masanasana.Ndipo mneneri adzapunthwa nanu limodzi ngati kuti ndi usiku.
Komanso mayi anu ndidzawakhalitsa chete.*
6 Anthu anga adzakhalitsidwa chete* chifukwa cha kusadziwa.
Popeza iwo akana kundidziwa,+Inenso ndidzawakana kuti asamanditumikire ngati wansembe wanga.Komanso chifukwa chakuti iwo aiwala lamulo* la ine Mulungu wawo,+Inenso ndidzaiwala ana awo.
7 Pamene akuchuluka, mʼpamenenso akundichimwira kwambiri.+
Ndidzasintha ulemerero wawo nʼkukhala kunyozeka.*
8 Iwo akupindula mwadyera ndi machimo a anthu anga,Ndipo amalakalaka mwadyera machimo a anthuwo.
9 Zimene zidzachitikire anthuwo zidzachitikiranso ansembe.Onse ndidzawaimba mlandu chifukwa cha njira zawo,Ndipo ndidzachititsa kuti zotsatira za zochita zawo ziwabwerere.+
10 Iwo adzadya, koma sadzakhuta.+
Adzachita zachiwerewere, koma sadzachulukana,+Chifukwa chakuti sakumvera Yehova.
11 Chiwerewere, vinyo wakale ndiponso vinyo watsopanoZimalepheretsa munthu kuchita zoyenera.+
12 Anthu anga amafunsira kwa mafano awo amtengo,Ndipo amachita zimene ndodo yawo* yawauza.Chifukwa chakuti mtima wachiwerewere umawasocheretsa,Ndiponso chifukwa cha chiwerewere chawocho, amakana kugonjera Mulungu wawo.
13 Iwo amapereka nsembe pamwamba pa mapiri akuluakulu,+Ndipo amapereka nsembe zautsi pamapiri angʼonoangʼono.Amachitanso zimenezi pansi pa mitengo yokhala ndi nthambi zambiri ndi masamba ambiri, pansi pa mitengo ya mlanje ndiponso pa mtengo uliwonse waukulu,+
Chifukwa mitengo imeneyi imakhala ndi mthunzi wabwino.Nʼchifukwa chake ana anu aakazi amachita uhule
Ndipo akazi a ana anu amachita chigololo.
14 Sindidzaimba mlandu ana anu aakazi chifukwa cha chiwerewere chawo,Komanso akazi a ana anu chifukwa cha chigololo chawo.
Chifukwa amuna akuyenda ndi mahuleNdipo amapereka nsembe limodzi ndi mahule apakachisi.Anthu osamvetsa zinthu amenewa+ adzawonongedwa.
15 Ngakhale kuti inu Aisiraeli mukuchita chiwerewere,+Yuda asakhale ndi mlandu.+
Musabwere ku Giligala+ kapena ku Beti-aveni,+Ndipo musalumbire kuti, ‘Mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo!’+
16 Isiraeli wakhala wamakani ngati ngʼombe yomwe ikuchita makani.+
Ndiye kodi Yehova adzawaweta ngati nkhosa yamphongo yaingʼono pamalo odyetsera ziweto?
17 Efuraimu wagwirizana ndi mafano.+
Musiyeni aona!
18 Mowa* wawo ukatha,Amayamba kuchita zachiwerewere.
Ndipo atsogoleri awo amakonda kwambiri zinthu zochititsa manyazi.+
19 Mphepo idzawakulunga mʼmapiko ake,Ndipo adzachita manyazi ndi nsembe zawo.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “ndidzawawononga.”
^ Kapena kuti, “adzawonongedwa.”
^ Kapena kuti, “malangizo.”
^ Mabaibulo ena amati, “Asintha ulemerero wanga nʼkukhala kunyozeka.”
^ Kapena kuti, “ndodo ya munthu wamatsenga.”
^ Kapena kuti, “Mowa wamasese.”