Hoseya 5:1-15

  • Chiweruzo cha Efuraimu ndi Yuda (1-15)

5  “Tamvani izi inu ansembe,+Ndipo mvetserani inu a mʼnyumba ya Isiraeli.Inunso a mʼnyumba ya mfumu mvetserani,Popeza chiweruzochi chikukhudza inuyo,Chifukwa mwakhala msampha ku MizipaNdiponso ngati ukonde paphiri la Tabori.+  2  Anthu amene andipandukira apha anthu ambiri,Ndipo ine ndikuwachenjeza onsewo.  3  Inetu ndimamudziwa bwino Efuraimu,Ndipo Isiraeli si wobisika kwa ine. Iwe Efuraimu wachita zachiwerewere,Ndipo Isiraeli wadziipitsa.+  4  Zochita zawo zikuwalepheretsa kubwerera kwa Mulungu wawo,Chifukwa iwo ali ndi mtima wachiwerewere+Ndipo akana kuzindikira kuti ine Yehova ndine Mulungu wawo.  5  Kunyada kwa Isiraeli kwakhala umboni womutsutsa,+Ndipo Isiraeli ndi Efuraimu apunthwa ndi zolakwa zawo.Nayenso Yuda wapunthwa nawo limodzi.+  6  Iwo anapita kukafunafuna Yehova ali ndi nkhosa ndiponso ngʼombe zawo,Koma sanamupeze. Chifukwa anali atawachokera.+  7  Akhala osakhulupirika kwa Yehova,+Chifukwa abereka ana achilendo. Tsopano mwezi udzawadya* limodzi ndi zinthu zawo.*  8  Lizani lipenga la nyanga ya nkhosa+ ku Gibeya ndi lipenga ku Rama!+ Fuulani mfuu ya nkhondo ku Beti-aveni:+ Tsogola iwe Benjamini!  9  Iwe Efuraimu, udzakhala chinthu choopsa pa tsiku limene udzalangidwe.+ Inetu ndauza mafuko a Isiraeli zinthu zimene zidzawachitikiredi. 10  Akalonga a Yuda ali ngati anthu osuntha malire.+ Ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ngati madzi. 11  Efuraimu waponderezedwa ndi chiweruzo,Chifukwa anatsimikiza mtima kutsatira mdani wake.+ 12  Choncho ndinali ngati njenjete* kwa Efuraimu,Ndipo ndinachititsa kuti nyumba ya Yuda iwole. 13  Efuraimu ataona matenda ake ndiponso Yuda ataona chilonda chake,Efuraimu anapita ku Asuri+ komanso anatumiza anthu kwa mfumu yaikulu. Koma mfumuyo sinathe kukuchiritsani.Ndipo sinathe kupoletsa chilonda chanu. 14  Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa Efuraimu,Ndiponso ngati mkango wamphamvu kwa anthu a mʼnyumba ya Yuda. Ineyo ndidzawakhadzulakhadzula nʼkuchoka.+Ndidzawatenga nʼkukawataya ndipo palibe adzawalanditse.+ 15  Kenako ndidzabwerera kumalo anga mpaka iwo atakumana ndi zotsatira za zolakwa zawo,Ndipo adzayamba kundifunafuna kuti ndiwakomere mtima.+ Akadzakumana ndi mavuto, adzandifuna.”+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Pasanathe mwezi, adzadyedwa.”
Kapena kuti, “minda yawo.”
Mawu amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.