Hoseya 6:1-11
6 “Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova,Chifukwa iye watikhadzulakhadzula,+ koma adzatichiritsa.
Wativulaza, koma adzamanga mabala athu.
2 Iye adzatithandiza kuti titsitsimuke pakatha masiku awiri.
Pa tsiku lachitatu adzatidzutsa,Ndipo tidzakhalanso ndi moyo pamaso pake.
3 Ife tidzamudziwa Yehova ndipo tidzayesetsa kuti timudziwe bwino.
Nʼzosakayikitsa kuti adzatulukira ngati mmene mʼbandakucha umafikira.Adzabwera kwa ife ngati mvula yambiri,Ngati mvula yomalizira imene imanyowetsa kwambiri nthaka.”
4 “Kodi ndikuchite chiyani iwe Efuraimu?
Nanga iwe Yuda, ndikuchite chiyani?
Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika chili ngati mitambo yamʼmawa,Ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma.
5 Nʼchifukwa chake anthu amenewa ndidzawadula pogwiritsa ntchito aneneri.+Ndidzawapha ndi mawu amʼkamwa mwanga.+
Chiweruzo chimene mudzalandire chidzakhala ngati kuwala.+
6 Chifukwa ndimakondwera ndi chikondi chokhulupirika,* osati nsembe.Ndimakondweranso ndi kudziwa Mulungu, osati nsembe zopsereza zathunthu.+
7 Koma iwo, mofanana ndi anthu wamba, aphwanya pangano.+
Kumeneko andichitira zosakhulupirika.
8 Giliyadi ndi tauni ya anthu ochita zoipa,+Yodzaza ndi zidindo za mapazi amagazi.+
9 Gulu la ansembe lili ngati gulu la achifwamba lobisalira munthu panjira.
Amapha anthu mumsewu ku Sekemu+Chifukwa khalidwe lawo ndi lochititsa manyazi.
10 Ndaona zinthu zonyansa kwambiri mʼnyumba ya Isiraeli.
Efuraimu akuchita zachiwerewere mmenemo.+Isiraeli wadziipitsa.+
11 Komanso, inu anthu a ku Yuda, nthawi yoti mukololedwe yakhazikitsidwa.Ine ndidzasonkhanitsanso anthu anga amene anatengedwa kupita kudziko lina.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “chifundo.”