Levitiko 11:1-47

  • Nyama zosadetsedwa ndi zodetsedwa (1-47)

11  Kenako Yehova analankhula ndi Mose komanso Aroni kuti: 2  “Uzani Aisiraeli kuti, ‘Zamoyo zapadziko lapansi* zimene mungadye+ ndi izi: 3  Mungadye nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogawanika zokhala ndi mpata pakati, yomwenso imabzikula. 4  Koma musamadye nyama zotsatirazi zimene zimabzikula kapena zili ndi ziboda zogawanika: Ngamila, chifukwa imabzikula koma ziboda zake nʼzosagawanika. Nyama imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu.+ 5  Ndiponso mbira,+ chifukwa imabzikula koma ziboda zake nʼzosagawanika. Ndi yodetsedwa kwa inu. 6  Chimodzimodzinso kalulu, chifukwa amabzikula koma ziboda zake nʼzosagawanika. Ndi wodetsedwa kwa inu. 7  Komanso nkhumba,+ chifukwa ziboda zake nʼzogawanika ndipo zili ndi mpata pakati, koma siibzikula. Ndi yodetsedwa kwa inu. 8  Musamadye nyama iliyonse ya zimenezi, ndipo nyamazi zikafa musamazikhudze. Ndi zodetsedwa kwa inu.+ 9  Zimene mungadye pa zonse zamʼmadzi ndi izi: Chilichonse chamʼmadzi chimene chili ndi zipsepse ndi mamba, kaya chimapezeka mʼnyanja kapena mʼmitsinje mungadye.+ 10  Koma chilichonse chopezeka mʼnyanja ndi mʼmitsinje chimene chilibe zipsepse ndi mamba, pa zamoyo zopezeka zambiri ndi pa zamoyo zina zonse zamʼmadzi, ndi zonyansa kwa inu. 11  Zinthu zimenezi zikhale zonyansa kwa inu. Musamadye nyama yake iliyonse,+ ndipo zikafa zizikhalabe zonyansa kwa inu. 12  Chamoyo chilichonse chamʼmadzi chimene chilibe zipsepse ndi mamba, ndi chonyansa kwa inu. 13  Izi ndi zamoyo zouluka zimene muyenera kuziona kuti ndi zonyansa. Sizikuyenera kudyedwa chifukwa ndi zonyansa: chiwombankhanga,+ nkhwazi, muimba wakuda,+ 14  mphamba wofiira, mtundu uliwonse wa mphamba wakuda, 15  mtundu uliwonse wa khwangwala, 16  nthiwatiwa, kadzidzi, kakowa, mtundu uliwonse wa kabawi, 17  nkhwezule, chiswankhono, mantchichi, 18  tsekwe, vuwo, muimba, 19  dokowe, mtundu uliwonse wa chimeza, sadzu ndi mleme. 20  Tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso tamiyendo 4, ndi tonyansa kwa inu. 21  Pa tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso timayenda ndi miyendo yonse 4, mungathe kudya tizilombo tokhato timene tili ndi miyendo iwiri italiitali yolumphira. 22  Tizilombo timene mungadye ndi iti: mitundu yosiyanasiyana ya dzombe loyenda mitunda italiitali, mitundu ina ya dzombe lodyedwa,+ nkhululu ndi ziwala. 23  Koma tizilombo tina tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso tamiyendo 4, ndi tonyansa kwa inu. 24  Zamoyo zimenezi nʼzimene mungadzidetse nazo. Aliyense wokhudza zamoyo zimenezi zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 25  Aliyense wonyamula chilichonse mwa zamoyo zimenezi chitafa, azichapa zovala zake,+ ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 26  Nyama iliyonse imene ili ndi chiboda chogawanika koma chopanda mpata pakati, imenenso siibzikula, ndi yodetsedwa kwa inu. Aliyense wokhudza nyama imeneyi adzakhala wodetsedwa.+ 27  Chamoyo chilichonse chokhala ndi mapazi a zikhadabo pa zamoyo zonse zimene zimayenda ndi miyendo yonse 4, nʼchodetsedwa kwa inu. Aliyense wokhudza chamoyo chimenechi chitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 28  Munthu wonyamula iliyonse ya nyama zimenezi itafa, azichapa zovala zake+ ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ Nyama zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu. 29  Izi ndi zamoyo zapadziko lapansi zomwe ndi zodetsedwa kwa inu: Mfuko, mbewa+ ndi mtundu uliwonse wa buluzi. 30  Ndiponso nalimata, buluzi wamkulu, dududu, buluzi wamumchenga ndi bilimankhwe. 31  Zamoyo zimenezi, zomwe zimapezeka zambiri, ndi zodetsedwa kwa inu.+ Aliyense wozikhudza zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 32  Ndiye chilichonse cha zamoyo zimenezi chikafa nʼkugwera pa chinthu china chilichonse, chinthucho chidzakhala chodetsedwa, kaya ndi chiwiya chamtengo, chovala, chikopa kapena chiguduli. Chiwiya chilichonse chimene chimagwiritsidwa ntchito chiziviikidwa mʼmadzi, ndipo chizikhala chodetsedwa mpaka madzulo, kenako chidzakhala choyera. 33  Ngati chamoyocho chagwera mʼchiwiya chadothi, muzichiswa, ndipo chilichonse chimene chinali mmenemo chidzakhala chodetsedwa.+ 34  Madzi a mʼchiwiya chimenecho akagwera pachakudya chilichonse, chakudyacho chizikhala chodetsedwa. Ndipo chakumwa chilichonse chimene chili mʼchiwiya chimenecho, chidzakhala chodetsedwa. 35  Chilichonse mwa zamoyo zimenezi chikafa nʼkugwera pachinthu chilichonse, kaya ndi uvuni kapena mbaula, chinthucho chidzakhala chodetsedwa ndipo muzichiswa. Zinthu zimenezi zadetsedwa ndipo zidzapitiriza kukhala zodetsedwa kwa inu. 36  Kasupe ndiponso thanki yosungiramo madzi ndi zokhazo zimene zidzakhalabe zoyera, koma aliyense wokhudza chinthu chakufacho adzakhala wodetsedwa. 37  Ngati chinthu chakufacho chagwera pambewu iliyonse imene mukufuna kudzala, mbewuyo izikhalabe yoyera. 38  Koma mbewuyo ikathiridwa madzi ndipo chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo nʼkugwerapo, mbewuyo izikhala yodetsedwa kwa inu. 39  Nyama iliyonse imene mwaloledwa kudya ikapezeka itafa, aliyense wokhudza nyama yakufayo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 40  Aliyense amene angadye nyama yakufayo azichapa zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ Aliyense amene anganyamule nyama yakufayo azichapa zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 41  Zamoyo zonse zimene zimapezeka zambiri padziko lapansi ndi zonyansa.+ Simukuyenera kudya zimenezi. 42  Musamadye chamoyo chilichonse chokwawa, chamoyo chilichonse chimene chimayenda ndi miyendo yonse 4 kapena zamoyo zonse zimene zimapezeka zambiri padziko lapansi, zokhala ndi miyendo yambiri, chifukwa zimenezi ndi zonyansa.+ 43  Musamadziipitse ndi zamoyo zilizonse zimene zimapezeka zambirizi ndipo musamadzidetse nazo nʼkukhala odetsedwa.+ 44  Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Mudzipatule ndi kukhala oyera,+ chifukwa ine ndine woyera.+ Choncho musamadzidetse ndi chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi. 45  Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu.+ Muzikhala oyera,+ chifukwa ine ndine woyera.+ 46  Limeneli ndi lamulo lokhudza nyama, zamoyo zouluka, zamoyo zonse zamʼmadzi ndi zamoyo zonse zapamtunda, 47  kuti muzisiyanitsa chodetsedwa ndi choyera komanso zamoyo zimene muyenera kudya ndi zimene simukuyenera kudya.’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Nyama zapamtunda.”