Levitiko 27:1-34
27 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu akapanga lonjezo lapadera+ lopereka munthu mnzake kwa Yehova pa mtengo womwe unaikidwa,
3 ndipo ngati munthu amene akuperekedwayo ndi wamwamuna, wazaka zapakati pa 20 ndi 60, mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli* asiliva 50, pamuyezo wofanana ndi sekeli yakumalo oyera.*
4 Koma ngati munthuyo ndi wamkazi, mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli 30.
5 Ndipo ngati munthu amene akuperekedwayo ndi wazaka zapakati pa 5 ndi 20, akakhala wamwamuna mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli 20, koma akakhala wamkazi mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli 10.
6 Ngati munthuyo ndi woyambira mwezi umodzi kufika zaka 5, akakhala wamwamuna mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli asiliva 5, ndipo akakhala wamkazi ndi masekeli asiliva atatu.
7 Ndiyeno ngati zaka za munthu amene akuperekedwayo ndi zoyambira pa 60 kupita mʼtsogolo, akakhala wamwamuna, mtengo wake womwe unaikidwa ndi masekeli 15, ndipo akakhala wamkazi ndi masekeli 10.
8 Koma ngati munthu amene akulonjezayo ndi wosauka moti sangakwanitse mtengo womwe unaikidwawo,+ azikaonetsa munthuyo kwa wansembe, ndipo wansembe azinena mtengo wake. Wansembe adzanena mtengo umene munthu amene analonjezayo angakwanitse.+
9 Koma ngati walonjeza kupereka nyama yomwe ndi yoyenera kuperekedwa nsembe kwa Yehova, nyama iliyonse imene angapereke kwa Yehova izikhala yopatulika.
10 Asaichotse nʼkuikapo ina, ndipo asasinthanitse yabwino ndi yoipa kapena yoipa ndi yabwino. Koma ngati waisinthanitsa ndi nyama ina, zonse ziwiri, yoyambayo ndiponso imene waisinthanitsayo, zizikhala zopatulika.
11 Koma ngati akupereka nyama yodetsedwa+ imene sikuyenera kuperekedwa nsembe kwa Yehova, azikaonetsa nyamayo kwa wansembe.
12 Wansembe azinena mtengo wake mogwirizana ndi mmene nyamayo ilili, kaya ndi yabwino kapena yoipa. Mtengo umene wansembe wanena uzikhala womwewo.
13 Koma ngati akufuna kuiwombola, azipereka mtengo wa nyamayo womwe unaikidwa nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo.+
14 Munthu akapereka nyumba yake kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, wansembe aziiona nʼkunena mtengo wake. Mtengowo uzidalira mmene nyumbayo ilili, kaya ndi yabwino kapena ayi. Mtengo umene wansembe wanena uzikhala womwewo.+
15 Koma amene wapereka nyumbayo akafuna kuiwombola, azipereka mtengo wa nyumbayo womwe unaikidwa nʼkuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo. Akatero nyumbayo izikhala yake.
16 Ngati munthu wapereka mbali ina ya munda wake kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, mtengo wa malowo uzikhala wogwirizana ndi mbewu zimene angadzalepo. Ngati angadzalepo balere wokwanira muyezo umodzi wa homeri,* ndiye kuti mtengo wa malowo ndi masekeli asiliva 50.
17 Ngati wapereka mundawo kuyambira mʼChaka cha Ufulu+ kupita mʼtsogolo, mtengo wake womwe unaikidwa uzikhala womwewo.
18 Koma ngati akupereka mundawo Chaka cha Ufulu chitadutsa, wansembe azimuwerengera mtengo wake mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kukafika mʼChaka cha Ufulu chotsatira, ndipo azichotsera pa mtengo wake womwe unaikidwa.+
19 Koma ngati munthu amene anapereka mundayo akufuna kuuwombola, azipereka mtengo wake womwe unaikidwa nʼkuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo ake 5, akatero mundawo uzikhala wake.
20 Ngati mundawo sanauwombole ndipo wagulitsidwa kwa munthu wina, sangathenso kuuwombola.
21 Mundawo ukamadzabwezedwa mʼChaka cha Ufulu, udzakhala wopatulika kwa Yehova monga munda umene waperekedwa kwa iye. Mundawo udzakhala wa ansembe.+
22 Ngati munthu wapereka munda kwa Yehova kuti ukhale wopatulika, koma mundawo anachita kugula ndipo sunali mbali ya cholowa chake,+
23 wansembe azimuwerengera mtengo wake, mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kuti Chaka cha Ufulu chifike, ndipo tsiku lomwelo azipereka mtengo umene wansembe wawerengerawo.+ Ndalamazo ndi zopatulika kwa Yehova.
24 MʼChaka cha Ufulu mundawo udzabwezedwa kwa mwiniwake weniweni amene anaugulitsa.+
25 Mtengo uliwonse womwe unaikidwa uzikhala wofanana ndi sekeli yakumalo oyera. Sekeli imodzi izikwana magera* 20.
26 Koma munthu asapereke nyama iliyonse yoyamba kubadwa kuti ikhale yopatulika, chifukwa iliyonse yoyamba kubadwa ndi ya Yehova.+ Kaya ndi ngʼombe kapena nkhosa, ndi za Yehova.+
27 Koma ngati ndi nyama yodetsedwa ndipo waiwombola mogwirizana ndi mtengo womwe unaikidwa, azipereka mtengo wa nyamayo nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo.+ Koma ngati sangaiwombole izigulitsidwa pa mtengo womwe unaikidwa.
28 Koma zinthu zimene munthu wapereka kwa Yehova monga zinthu zoyenera kuwonongedwa, kuchokera pa katundu wake, sizikuyenera kugulitsidwa kapena kuwomboledwa, kaya ndi munthu, nyama kapena munda. Chinthu chilichonse chimene munthu wapereka kwa Yehova ndi chopatulika koposa.+
29 Kuwonjezera pamenepa, munthu aliyense amene waperekedwa kwa Mulungu kuti awonongedwe sangathe kuwomboledwa.+ Ameneyo aziphedwa ndithu.+
30 Chakhumi chilichonse+ cha zinthu zamʼdzikolo, kaya ndi zokolola zamʼmunda kapena zipatso zamʼmitengo, ndi za Yehova. Chakhumi chimenechi ndi chopatulika kwa Yehova.
31 Ngati munthu akufuna kuwombola chakhumi chake chilichonse, azipereka mtengo wa chakhumicho nʼkuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo 5 a mtengowo.
32 Ngʼombe kapena nkhosa iliyonse ya 10, pa nyama zonse zodutsa pansi pa ndodo ya mʼbusa, nyama iliyonse ya 10 izikhala yopatulika kwa Yehova.
33 Asaifufuze ngati ili yabwino kapena yoipa, ndiponso asaisinthanitse ndi ina. Koma ngati waisinthanitsa ndi nyama ina, zonse ziwiri, yoyambayo ndi imene waisinthanitsayo, zizikhala zopatulika.+ Sangathe kuiwombola.’”
34 Amenewa ndi malamulo amene Yehova anapatsa Mose paphiri la Sinai+ kuti apereke kwa Aisiraeli.
Mawu a M'munsi
^ Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
^ Homeri imodzi inali yofanana ndi malita 220. Onani Zakumapeto B14.
^ Gera limodzi linali lofanana ndi magalamu 0.57. Onani Zakumapeto B14.