Wolembedwa ndi Luka 10:1-42

  • Yesu anatumiza ophunzira 70 (1-12)

  • Tsoka mizinda yosalapa (13-16)

  • Ophunzira 70 aja anabwerera (17-20)

  • Yesu anatamanda Atate wake chifukwa chokomera mtima anthu odzichepetsa (21-24)

  • Fanizo la Msamariya wachifundo (25-37)

  • Yesu anapita kwa Marita ndi Mariya (38-42)

10  Pambuyo pa zimenezi, Ambuye anasankha anthu ena 70 nʼkuwatumiza awiriawiri+ kuti atsogole kupita mumzinda ndi malo alionse kumene iye ankafunika kudzapitako. 2  Kenako anawauza kuti: “Inde, pali zinthu zambiri zofunika kukolola, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwiniwake wa munda kuti atumize antchito kukakolola.+ 3  Pitani! Inetu ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu.+ 4  Musatenge chikwama cha ndalama, thumba la chakudya, kapena nsapato,+ ndipo musamapereke moni kwa wina aliyense* panjira. 5  Mukafika panyumba, choyamba muzinena kuti: ‘Mtendere ukhale panyumba pano.’+ 6  Ndipo ngati pakhomopo pali munthu wokonda mtendere, mtendere wanu udzakhala pa iye. Koma ngati palibe, udzabwerera kwa inu. 7  Choncho muzikhala mʼnyumba imeneyo+ ndipo muzidya ndi kumwa zimene angakupatseni,+ chifukwa wantchito ayenera kulandira malipiro ake.+ Musamachoke kumene mwafikirako nʼkupita kunyumba zina. 8  Komanso mukalowa mumzinda ndipo iwo nʼkukulandirani, muzidya zimene akukonzerani, 9  muzichiritsanso odwala amene ali mmenemo komanso muziwauza kuti: ‘Ufumu wa Mulungu wakuyandikirani.’+ 10  Koma mukalowa mumzinda umene sanakulandireni bwino, muzichokamo nʼkupita mʼmisewu yawo nʼkunena kuti: 11  ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi lamumzinda wanu uno,+ limene lamatirira kumapazi kwathu. Komabe dziwani kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 12  Ndikukuuzani, chilango cha mzinda umenewo chidzakhala chopweteka kwambiri pa tsiku limenelo kuposa cha Sodomu.+ 13  Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida! Chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanakhala kuti zinachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu akanakhala atalapa kalekale, atavala ziguduli nʼkukhala paphulusa.+ 14  Choncho chilango chanu pachiweruzo chidzakhala chopweteka kwambiri kuposa cha Turo ndi Sidoni. 15  Iwenso Kaperenao, kodi mwina udzakwezedwa kumwamba? Ayi, koma udzatsikira ku Manda.* 16  Amene akukumverani, akumveranso ine.+ Amene akunyalanyaza inu, akunyalanyazanso ine ndipo amene akunyalanyaza ine, akunyalanyazanso Mulungu amene anandituma.”+ 17  Kenako anthu okwana 70 aja anabwerera akusangalala ndipo anauza Yesu kuti: “Ambuye, ngakhale ziwanda zimatigonjera tikagwiritsa ntchito dzina lanu.”+ 18  Atamva zimenezo iye anawauza kuti: “Ndayamba kuona Satana atagwa kale+ ngati mmene mphezi imachitira kuchokera kumwamba. 19  Taonani! Inetu ndakupatsani ulamuliro kuti muzitha kupondaponda njoka ndi zinkhanira. Komanso ndakupatsani ulamuliro kuti mugonjetse mphamvu zonse za mdani,+ ndipo palibe chimene chidzakuvulazeni. 20  Komano musasangalale chifukwa choti mizimu yakugonjerani, koma sangalalani chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.”+ 21  Pa nthawi imeneyo Yesu anasangalala kwambiri mwa mzimu woyera nʼkunena kuti: “Ndikukutamandani inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa anthu anzeru ndi ozindikira mwawabisira mosamala zinthu zimenezi+ ndipo mwaziulula kwa ana aangʼono. Inde Atate, chifukwa inu munavomereza kuti zimenezi zichitike.+ 22  Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine ndipo palibe amene akumudziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha+ ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.”+ 23  Ndiyeno Yesu ndi ophunzira akewo ali kwaokha, anawauza kuti: “Osangalala ndi anthu amene akuona zimene inu mukuonazi.+ 24  Chifukwa ndithu ndikukuuzani, aneneri ambiri komanso mafumu ankalakalaka kuti aone zinthu zimene mukuziona inuzi koma sanazione,+ komanso kuti amve zimene mukumva inuzi koma sanazimve.” 25  Kenako munthu wina wodziwa Chilamulo anaimirira kuti amuyese ndipo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, ndizichita chiyani kuti ndidzapeze moyo wosatha?”+ 26  Yesu anamufunsa kuti: “Kodi mʼChilamulo analembamo chiyani? Umawerengamo zotani?” 27  Iye anayankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.’+ Komanso ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+ 28  Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola. Uzichita zimenezo ndipo udzapeza moyo.”+ 29  Koma pofuna kudzionetsera kuti ndi wolungama,+ munthuyo anafunsa Yesu kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndi ndani kwenikweni?” 30  Poyankha Yesu ananena kuti: “Munthu wina ankayenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko ndipo anakumana ndi achifwamba amene anamuvula nʼkumumenya koopsa. Kenako anachoka, nʼkumusiya atatsala pangʼono kufa. 31  Ndiye zinangochitika kuti wansembe wina ankadutsa mumsewu womwewo, koma atamuona, anangomulambalala. 32  Chimodzimodzinso Mlevi, atafika pamalowo nʼkumuona, anangomulambalala. 33  Koma panafika Msamariya wina+ amene ankadutsanso mumsewu womwewo. Ndipo atamuona, anamva chisoni. 34  Choncho anafika pamene panali munthuyo ndipo anathira mafuta komanso vinyo mʼmabala ake nʼkuwamanga. Kenako anamukweza pabulu wake nʼkupita naye kunyumba ya alendo kumene anamusamalira. 35  Tsiku lotsatira anatulutsa madinari* awiri nʼkupereka kwa mwini nyumba ya alendoyo ndipo anamuuza kuti: ‘Musamalireni bwino, mukawononga ndalama zina zowonjezera, ndidzakubwezerani ndikadzabwera.’ 36  Ndi ndani pa anthu atatuwa amene iweyo ukuona kuti anakonda+ munthu amene anakumana ndi achifwambayu?” 37  Iye anayankha kuti: “Ndi amene anamuchitira chifundoyo.”+ Ndiye Yesu anamuuza kuti: “Pita, iwenso uzikachita zomwezo.”+ 38  Ndiyeno iwo anapitiriza ulendo wawo ndipo analowa mʼmudzi wina. Kumeneko mayi wina dzina lake Marita+ anamulandira mʼnyumba mwake monga mlendo. 39  Iye anali ndi mchemwali wake dzina lake Mariya, amene anakhala pansi pafupi ndi Ambuye nʼkumamvetsera zimene ankanena.* 40  Koma Marita anatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho anafika kwa Yesu nʼkunena kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti mchemwali wangayu wandisiyira ndekha ntchito? Tamuuzeni kuti abwere adzandithandize.” 41  Poyankha Ambuye anamuuza kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri. 42  Komatu zinthu zofunika kwenikweni ndi zochepa, mwinanso nʼchimodzi chokha basi. Kumbali yake, Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri+ ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndipo musamachedwe ndi kupereka moni.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mawu awo.”