Wolembedwa ndi Luka 7:1-50

  • Chikhulupiriro cha mtsogoleri wa asilikali (1-10)

  • Yesu anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye ku Naini (11-17)

  • Yohane Mʼbatizi anatamandidwa (18-30)

  • Anadzudzula mʼbadwo wosamvera (31-35)

  • Mkazi wochimwa anakhululukidwa (36-50)

    • Fanizo la anthu amene anatenga ngongole (41-43)

7  Yesu atamaliza kunena zonse zimene ankafuna kuuza anthu, analowa mumzinda wa Kaperenao. 2  Kumeneko kapolo wa mtsogoleri wina wa asilikali, amene mtsogoleriyo ankamukonda kwambiri, ankadwala ndipo anali atatsala pangʼono kumwalira.+ 3  Mtsogoleriyo atamva za Yesu, anatumiza akulu ena a Ayuda kwa iye kukamupempha kuti abwere kudzachiritsa kapolo wakeyo. 4  Anthuwo atafika kwa Yesu anayamba kumuchonderera ndi mtima wonse kuti: “Ameneyu ndi woyenereradi kuti mumuthandize, 5  chifukwa amakonda anthu amtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge.” 6  Choncho Yesu ananyamuka nawo limodzi. Koma atatsala pangʼono kufika kunyumbako, anakumana ndi anzake a mtsogoleri wa asilikali uja, amene anawatuma kuti adzamuuze kuti: “Ambuye musavutike ndi kubwera, sindine munthu woyenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga.+ 7  Nʼchifukwa chake inenso sindinadzione kuti ndine woyenera kubwera kwa inu. Koma mungonena mawu okha ndipo wantchito wangayo achira. 8  Chifukwa inenso ndili ndi akuluakulu amene anaikidwa kuti azindiyangʼanira komanso ndili ndi asilikali amene ndimawayangʼanira. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’ amapita, wina ndikamuuza kuti, ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.” 9  Yesu atamva zimenezi anadabwa ndi munthu ameneyu. Kenako anatembenukira gulu la anthu omwe ankamutsatira nʼkuwauza kuti: “Kunena zoona, ngakhale mu Isiraeli sindinapezemo aliyense wachikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.”+ 10  Koma anthu amene anatumidwa aja atabwerera kunyumba, anakapeza kapolo uja ali bwinobwino.+ 11  Patangopita kanthawi pangʼono, ananyamuka kupita kumzinda wina wotchedwa Naini. Ophunzira ake ndiponso gulu lalikulu la anthu linkayenda naye limodzi. 12  Atayandikira pageti la mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula maliro. Munthu amene anamwalirayo anali mwana wamwamuna yekhayo kwa mayi ake.+ Komanso mayi akewo anali mkazi wamasiye. Gulu lalikulu ndithu la anthu ochokera mumzindawo linali limodzi ndi mayiwo. 13  Ambuye ataona mayiwo anawamvera chisoni,+ ndipo anawauza kuti: “Tontholani mayi.”+ 14  Atatero anayandikira nʼkugwira chithathacho ndipo amene ananyamulawo anangoima. Kenako iye ananena kuti: “Mnyamata iwe, ndikunena ndi iwe, dzuka!”+ 15  Zitatero mnyamata amene anamwalirayo anadzuka nʼkuyamba kulankhula ndipo Yesu anamupereka kwa mayi ake.+ 16  Ataona zimenezi anthu onse anachita mantha ndipo anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu.”+ Ananenanso kuti, “Mulungu wakumbukira anthu ake.”+ 17  Nkhani imeneyi, yonena za Yesu, inafala paliponse mu Yudeya monse ndi mʼmadera onse ozungulira. 18  Ndiyeno ophunzira a Yohane anamuuza zinthu zonsezi.+ 19  Choncho Yohane anaitanitsa ophunzira ake awiri nʼkuwatuma kwa Ambuye kukafunsa kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja* ndinu+ kapena tiyembekezere wina?” 20  Atafika kwa iye amunawo ananena kuti: “Yohane Mʼbatizi watituma kudzakufunsani kuti: ‘Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndi inu kapena tiyembekezere wina?’” 21  Mu ola limenelo iye anachiritsa anthu ambiri amene ankavutika ndi matenda osiyanasiyana+ komanso amene ankadwala mwakayakaya ndi kutulutsa mizimu yoipa. Anathandizanso anthu ambiri amene anali ndi vuto losaona kuti ayambe kuona. 22  Choncho poyankha anauza amuna awiri aja kuti: “Pitani mukauze Yohane zimene mwaona ndi kumva: Amene anali ndi vuto losaona akuona,+ olumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa ndipo amene anali ndi vuto losamva akumva.+ Akufa akuukitsidwa ndipo osauka akuuzidwa uthenga wabwino.+ 23  Wosangalala ndi amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.”+ 24  Anthu amene Yohane anawatuma aja atachoka, Yesu anayamba kuuza gulu la anthu za Yohane kuti: “Kodi munapita mʼchipululu kukaona chiyani? Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+ 25  Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena?+ Ayi, paja amene amavala zovala zapamwamba ndiponso anthu amene amakhala moyo wamwanaalirenji amapezeka mʼnyumba zachifumu. 26  Nangano munapita kukaona chiyani makamaka? Mneneri kapena? Inde, ndikukuuzani, Yohane ndi mneneri komanso ndi wofunika kwambiri kuposa aneneri.+ 27  Malemba amanena za iyeyu kuti: ‘Taona! Inetu ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole kukakukonzera njira.’+ 28  Ndithudi ndikukuuzani, pa anthu onse,* palibe wamkulu kuposa Yohane. Koma munthu amene ali wocheperapo mu Ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iyeyu.”+ 29  (Anthu onse komanso okhometsa msonkho atamva zimenezi, analengeza kuti Mulungu ndi wolungama, chifukwa iwo anali atabatizidwa ndi Yohane.+ 30  Koma Afarisi ndi anthu odziwa Chilamulo ananyalanyaza malangizo amene Mulungu anawapatsa.+ Choncho Yohane sanawabatize.) 31  “Kodi anthu a mʼbadwo uwu ndiwayerekeze ndi ndani ndipo kodi akufanana ndi ndani?+ 32  Iwo ali ngati ana aangʼono amene akhala pansi mumsika nʼkumafuulirana kuti: ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunalire.’ 33  Mofanana ndi zimenezi, Yohane Mʼbatizi anabwera ndipo sakudya chakudya kapena kumwa vinyo,+ koma inu mukunena kuti: ‘Ali ndi chiwanda.’ 34  Mwana wa munthu wabwera ndipo iye akudya ndi kumwa, koma inu mukunena kuti: ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa!’+ 35  Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha zotsatira zake.”+ 36  Ndiyeno Mfarisi wina anaumiriza Yesu kuti akadye naye. Choncho anapita kunyumba ya Mfarisiyo ndipo anamupatsa chakudya. 37  Koma mayi wina amene anali wodziwika mumzindawo kuti ndi wochimwa, anamva kuti Yesu akudya chakudya mʼnyumba ya Mfarisiyo. Choncho anapita komweko ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala, muli mafuta onunkhira.+ 38  Atafika anagwada kumapazi ake nʼkuyamba kulira, moti anayamba kunyowetsa mapaziwo ndi misozi, kwinaku akupukuta mapaziwo ndi tsitsi lamʼmutu mwake. Komanso anakisa mapazi akewo mwachikondi nʼkuwapaka mafuta onunkhirawo. 39  Mfarisi amene anamuitana uja ataona zimenezi, mumtima mwake ananena kuti: “Munthuyu akanakhala kuti ndi mneneridi, akanadziwa kuti mkazi amene akumugwirayu ndi ndani, ndiponso kuti ndi wotani. Akanadziwa kuti ndi wochimwa.”+ 40  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Simoni, ndikufuna ndikuuze kanthu kena.” Iye anati: “Ndiuzeni Mphunzitsi!” 41  “Amuna awiri anatenga ngongole kwa munthu wina wokongoza ndalama. Mmodzi anatenga ngongole ya madinari* 500, koma winayo anatenga ngongole ya madinari 50. 42  Atalephera kubweza ngongolezo, mwiniwake uja anawakhululukira ndi mtima wonse. Kodi ndi ndani mwa awiriwo amene angakonde kwambiri wokongozayo?” 43  Poyankha Simoni anati: “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira zambiriyo.” Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola.” 44  Atatero anacheukira mayi uja nʼkuuza Simoni kuti: “Wamuona mayiyu? Ngakhale kuti ndalowa mʼnyumba yako, sunandipatse madzi otsukira mapazi anga. Koma mayiyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake nʼkuwapukuta ndi tsitsi lake. 45  Iwe sunandikise, koma chilowereni muno, mayiyu sanasiye kukisa mapazi anga mwachikondi. 46  Iwe sunathire mafuta mʼmutu mwanga, koma mayiyu wapaka mapazi anga mafuta onunkhira. 47  Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuza kuti, machimo ake akhululukidwa, ngakhale kuti ndi ochuluka.+ Nʼchifukwa chake akusonyeza chikondi chochuluka. Koma amene wakhululukidwa machimo ochepa amasonyezanso chikondi chochepa.” 48  Kenako anauza mayiyo kuti: “Machimo ako akhululukidwa.”+ 49  Anthu onse amene anakhala naye patebulopo anayamba kudzifunsa mumtima mwawo kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani amene amathanso ngakhale kukhululukira machimo?”+ 50  Koma iye anauza mayiyo kuti: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa.+ Pita mu mtendere.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Kodi Wobwerayo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwa onse amene anabadwa kwa akazi.”