Machitidwe a Atumwi 11:1-30

  • Petulo anakapereka lipoti kwa atumwi (1-18)

  • Baranaba ndi Saulo anapita ku Antiokeya wa ku Siriya (19-26)

    • Ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu (26)

  • Agabo analosera za njala (27-30)

11  Tsopano atumwi ndi abale amene anali ku Yudeya anamva kuti anthu a mitundu ina nawonso alandira mawu a Mulungu. 2  Koma Petulo atapita ku Yerusalemu, anthu olimbikitsa mdulidwe+ anayamba kumuimba mlandu. 3  Iwo ankamunena kuti: “Iwe unakalowa mʼnyumba ya anthu osadulidwa ndipo unadya nawo.” 4  Ndiyeno Petulo anayamba kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene zinachitika kuti: 5  “Ine ndikupemphera mumzinda wa Yopa, ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chooneka ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba. Chinthucho anachigwira mʼmakona onse 4 nʼkuchitsitsira pamene ndinali.+ 6  Nditachiyangʼanitsitsa, ndinaonamo nyama za miyendo 4 zapadziko lapansi, nyama zakutchire, nyama zokwawa komanso mbalame zamumlengalenga. 7  Ndinamvanso mawu akuti: ‘Petulo, nyamuka ndipo uphe zinthu zimenezi nʼkudya.’ 8  Koma ine ndinati, ‘Ayi Ambuye, mʼkamwa mwanga simunalowepo chinthu chilichonse chodetsedwa ndiponso chonyansa.’ 9  Koma ndinamvanso mawu aja kachiwiri kuti: ‘Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa, usiyiretu kunena kuti nʼzodetsedwa.’ 10  Mawuwo anamvekanso kachitatu, ndipo kenako zonse zija zinatengedwa kupita kumwamba. 11  Nthawi yomweyo, anthu atatu amene anatumidwa kwa ine kuchokera ku Kaisareya anaima panyumba imene tinkakhala.+ 12  Kenako mzimu unandiuza kuti ndipite nawo, ndisakayikire ngakhale pangʼono. Abale 6 awa anapita nane limodzi ndipo tinakalowa mʼnyumba ya munthuyo. 13  Iye anatiuza kuti ali mʼnyumba mwake anaona mngelo ataimirira ndipo anamuuza kuti, ‘Tuma anthu kuti apite ku Yopa akaitane Simoni wotchedwanso Petulo.+ 14  Iye adzakuuza zinthu zimene zidzathandize iweyo ndi anthu onse a mʼbanja lako kupulumuka.’ 15  Koma nditangoyamba kulankhula, iwo analandira mzimu woyera ngati mmene zinalilinso ndi ifeyo poyamba paja.+ 16  Zitatero ndinakumbukira mawu amene Ambuye ankakonda kunena aja akuti, ‘Yohane ankabatiza ndi madzi,+ koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.’+ 17  Choncho ngati Mulungu anawapatsa mphatso yaulere yomwenso anatipatsa ifeyo amene tinakhulupirira mwa Ambuye Yesu Khristu, ndine ndani kuti ndiletse Mulungu?”+ 18  Atamva zimenezi, anasiya kumutsutsa,* ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Ndiye kuti Mulungu waperekanso mwayi kwa anthu a mitundu ina kuti nawonso alape nʼkudzapeza moyo.”+ 19  Anthu amene anabalalika+ chifukwa cha mavuto amene anayamba chifukwa cha zimene zinachitikira Sitefano, anakafika mpaka ku Foinike, ku Kupuro ndi ku Antiokeya. Ndipo ankangolalikira kwa Ayuda okha.+ 20  Koma ena mwa anthuwa anali a ku Kupuro ndi ku Kurene. Iwowa atafika ku Antiokeya anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ambuye Yesu kwa anthu olankhula Chigiriki. 21  Dzanja la Yehova* linkawathandiza ndipo anthu ambiri anakhulupirira nʼkuyamba kutsatira Ambuye.+ 22  Mpingo wa ku Yerusalemu unamva za anthuwa ndipo unatumiza Baranaba+ kuti apite ku Antiokeya. 23  Atafika kumeneko nʼkuona kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, anasangalala ndipo anayamba kulimbikitsa onse kuti apitirize ndi mtima wonse kukhala okhulupirika kwa Ambuye.+ 24  Baranaba anali munthu wabwino komanso wa chikhulupiriro cholimba. Iye ankatsogoleredwa kwambiri ndi mzimu woyera ndipo anthu enanso ambiri anakhulupirira Ambuye.+ 25  Kenako Baranaba anapita ku Tariso kukafufuza Saulo.+ 26  Atamupeza anabwera naye ku Antiokeya. Iwo anasonkhana ndi mpingo kumeneko kwa chaka chathunthu ndipo anaphunzitsa anthu ambiri. Ku Antiokeya nʼkumene ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.+ 27  Pa nthawiyi, aneneri+ ochokera ku Yerusalemu anapita ku Antiokeya. 28  Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, mmodzi wa iwo dzina lake Agabo,+ analosera kuti padziko lonse lapansi+ padzagwa njala yaikulu. Izi zinachitikadi mʼnthawi ya Kalaudiyo. 29  Choncho ophunzirawo anatsimikiza mtima kutumiza thandizo+ kwa abale a ku Yudeya, aliyense mogwirizana ndi zimene akanakwanitsa.+ 30  Ndipo anachitadi zimenezo moti thandizolo anapatsira Baranaba ndi Saulo kuti akapereke kwa akulu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anangoti kukamwa yasaa.”