Machitidwe a Atumwi 20:1-38

  • Paulo ku Makedoniya ndi ku Girisi (1-6)

  • Utiko anaukitsidwa ku Torowa (7-12)

  • Kuchoka ku Torowa kupita ku Mileto (13-16)

  • Paulo anakumana ndi akulu a ku Efeso (17-38)

    • Ankaphunzitsa kunyumba ndi nyumba (20)

    • “Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri” (35)

20  Chipolowe chija chitatha, Paulo anaitanitsa ophunzira. Atawalimbikitsa nʼkutsanzikana nawo, ananyamuka ulendo wopita ku Makedoniya. 2  Iye anayendayenda mʼmadera akumeneko nʼkumalimbikitsa ophunzira ndi mawu ambiri, kenako anafika ku Girisi. 3  Atakhala kumeneko miyezi itatu, anaganiza zobwerera ku Makedoniya, chifukwa chakuti Ayuda+ anamukonzera chiwembu. Chiwembuchi anachikonza Paulo atangotsala pangʼono kuyamba ulendo wapamadzi wopita ku Siriya. 4  Pa ulendowu anali limodzi ndi Sopaturo mwana wa Puro wa ku Bereya, Arisitako+ ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Debe ndi Timoteyo,+ koma ochokera mʼchigawo cha Asia anali Tukiko+ ndi Terofimo.+ 5  Anthu amenewa anatsogola ndipo ankatiyembekezera ku Torowa. 6  Koma tinayamba ulendo wapanyanja ku Filipi masiku a Mkate Wopanda Zofufumitsa+ atatha. Ndipo tinawapeza ku Torowa patapita masiku 5. Kumeneko tinakhalako masiku 7. 7  Pa tsiku loyamba la mlungu, titasonkhana pamodzi kuti tidye chakudya, Paulo anayamba kuwakambira nkhani, chifukwa kunali koti anyamuka tsiku lotsatira. Ndipo analankhula kwa nthawi yaitali mpaka pakati pa usiku. 8  Mʼchipinda chamʼmwamba mmene tinasonkhanamo, munali nyale zambiri ndithu. 9  Paulo ali mkati mokamba nkhani, mnyamata wina dzina lake Utiko amene anakhala pawindo, anagona tulo tofa nato. Ali mʼtulo choncho, anagwa pansi kuchokera panyumba yachitatu yosanja, ndipo anamupeza atafa. 10  Koma Paulo anatsika pansi, ndipo anafika pamene iye anali nʼkumukumbatira.+ Kenako ananena kuti: “Khalani chete, chifukwa ali moyo tsopano.”+ 11  Atatero Paulo anapitanso mʼchipinda chamʼmwamba chija ndipo anatenga mkate nʼkuyamba kudya.* Anakambirana nawo kwa nthawi yaitali mpaka mʼbandakucha ndipo kenako ananyamuka nʼkumapita. 12  Choncho iwo anatenga mnyamata uja ali wamoyo ndipo anatonthozedwa kwambiri. 13  Tsopano ife tinatsogola kukakwera ngalawa nʼkuyamba ulendo wopita ku Aso. Iye anatiuza kuti titsogole ndipo tikamutengere ku Aso chifukwa ankafuna kuyenda wapansi. 14  Choncho atatipeza ku Aso, tinamukweza mʼngalawa nʼkupita ku Mitilene. 15  Mʼmawa wake titachoka kumeneko, tinafika pafupi ndi Kiyo. Koma tsiku lotsatira tinaima kwa kanthawi ku Samo, ndipo mʼmawa wake tinafika ku Mileto. 16  Paulo anaganiza zongolambalala Efeso,+ kuti asataye nthawi mʼchigawo cha Asia. Anachita zimenezi chifukwa ankafulumira kuti ngati nʼkotheka, pa tsiku la Chikondwerero cha Pentekosite akakhale ali ku Yerusalemu.+ 17  Komabe ali ku Mileto anatumiza uthenga woti akulu a mpingo wa ku Efeso abwere. 18  Akuluwo atafika, iye anawauza kuti: “Inu mukudziwa bwino mmene ndinkachitira zinthu pa nthawi yomwe ndinali nanu, kuchokera tsiku limene ndinafika mʼchigawo cha Asia.+ 19  Ndinkatumikira Ambuye ngati kapolo modzichepetsa kwambiri,+ ndi misozi komanso ndi mayesero amene ndinakumana nawo chifukwa cha ziwembu za Ayuda. 20  Komatu sindinakubisireni chilichonse chothandiza ndipo sindinasiye kukuphunzitsani pagulu+ komanso kunyumba ndi nyumba.+ 21  Koma ndachitira umboni mokwanira kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, kuti alape+ nʼkubwerera kwa Mulungu komanso kuti ayambe kukhulupirira Ambuye wathu Yesu.+ 22  Ndipo tsopano, motsogoleredwa ndi mzimu, ndikupita ku Yerusalemu ngakhale kuti sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko. 23  Koma chinthu chimodzi chokha chimene ndikudziwa nʼchakuti mumzinda ndi mzinda, mzimu woyera wandichitira umboni mobwerezabwereza kuti ndikuyembekezera kumangidwa komanso kuzunzidwa.+ 24  Komabe, moyo wanga sindikuuona ngati wofunika* kwa ine. Chimene ndikungofuna nʼchakuti ndimalize kuthamanga mpikisanowu, komanso kuti ndimalize+ utumiki umene ndinalandira kwa Ambuye Yesu. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. 25  Ndipo tamverani tsopano. Ndikudziwa kuti nonsenu amene ndinakulalikirani za Ufumu, simudzaonanso nkhope yanga. 26  Choncho mukhale mboni lero, kuti ine ndilibe mlandu wa magazi a anthu onse+ 27  chifukwa ndinakuuzani malangizo onse a Mulungu.*+ 28  Muzidziyangʼanira nokha+ komanso kusamalira gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani kuti muziliyangʼanira,+ kuti muwete mpingo wa Mulungu,+ umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.+ 29  Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzafika pakati panu+ ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. 30  Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.+ 31  Choncho khalani maso, ndipo muzikumbukira kuti kwa zaka zitatu+ masana ndi usiku, sindinasiye kuchenjeza aliyense wa inu ndikutulutsa misozi. 32  Koma tsopano ndikukusiyani kuti mutetezedwe ndi Mulungu ndiponso mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu. Mawu amenewo angakulimbikitseni ndi kukupatsani cholowa pakati pa oyera onse.+ 33  Sindinasirire siliva, golide kapena chovala cha munthu.+ 34  Inunso mukudziwa bwino kuti manja awa anagwira ntchito kuti ndipeze zofunika pa moyo wanga+ ndi za amene ndinali nawo. 35  Pa zinthu zonse ndakusonyezani kuti pogwira ntchito molimbikira chonchi,+ muzithandiza ofooka ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Paja iye anati, ‘Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri+ kuposa kulandira.’” 36  Atanena zimenezi, iyeyo ndi akulu onsewo anagwada nʼkupemphera. 37  Zitatero onse analira kwambiri. Kenako anamuhaga* Paulo nʼkumukisa mwachikondi. 38  Iwo anamva chisoni kwambiri, makamaka chifukwa cha mawu amene iye ananena akuti sadzaonanso nkhope yake.+ Kenako anamʼperekeza kukakwera ngalawa.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ananyemanyema mkate ndipo anayamba kudya.”
Kapena kuti, “wamtengo wapatali.”
Kapena kuti, “zonse zimene Mulungu akufuna kuchita.”
Kapena kuti, “anamukumbatira.”