Machitidwe a Atumwi 26:1-32

  • Paulo anadziteteza pamaso pa Agiripa (1-11)

  • Paulo anafotokoza mmene anakhalira Mkhristu (12-23)

  • Zimene Fesito ndi Agiripa anachita (24-32)

26  Agiripa+ anauza Paulo kuti: “Ukhoza kulankhula mbali yako.” Ndiyeno Paulo anakweza dzanja nʼkuyamba kulankhula modziteteza kuti: 2  “Inu Mfumu Agiripa, ndine wosangalala kuti lero ndidziteteza pamaso panu, pa zinthu zonse zimene Ayuda akundineneza.+ 3  Makamaka chifukwa chakuti ndinu katswiri pa miyambo yonse komanso pa zimene Ayuda amakangana. Choncho ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima. 4  Ndithudi, moyo umene ndakhala kuyambira ndili mnyamata, pakati pa anthu a mtundu wanga ndiponso mu Yerusalemu, ndi wodziwika bwino kwa Ayuda onse+ 5  amene akundidziwa kuyambira kale. Atafuna, angandichitire umboni kuti ndinalidi Mfarisi+ wa mʼgulu limene limalambira mokhwimitsa zinthu kwambiri.+ 6  Koma tsopano ndikuimbidwa mlandu chifukwa cha chiyembekezo cha zimene Mulungu analonjeza makolo athu.+ 7  Mafuko athu 12 akuyembekezera kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli ndipo akumuchitira Mulunguyo utumiki wopatulika mosalekeza masana ndi usiku. Choncho Mfumu, Ayuda akundiimba mlandu chifukwa cha chiyembekezo chimenechi.+ 8  Nʼchifukwa chiyani anthu inu mukuona kuti nʼzosatheka kuti Mulungu aukitse akufa? 9  Inetu ndinkaganiza kuti ndiyenera kuchita zambiri zotsutsana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti. 10  Ndipo izi ndi zimene ndinachitadi ku Yerusalemu. Ndinkatsekera mʼndende oyera ambiri+ nditapatsidwa mphamvu ndi ansembe aakulu.+ Akaweruzidwa kuti aphedwe, ine ndinkavomereza. 11  Nthawi zambiri ndinkawapatsa chilango mʼmasunagoge onse, pofuna kuwakakamiza kuti asiye zimene amakhulupirira. Popeza ndinali nditakwiya nawo kwambiri, ndinafika powazunza ngakhale mʼmizinda yakunja. 12  Ndili ndi zolinga zimenezi, ndinanyamuka ulendo wopita ku Damasiko nditapatsidwa mphamvu komanso chilolezo ndi ansembe aakulu. 13  Koma ndili mʼnjira dzuwa lili pamutu, inu mfumu, ndinaona kuwala kochokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa ndipo kunandizungulira ineyo ndiponso anthu amene ndinali nawo pa ulendowu.+ 14  Ndiyeno tonse titagwa pansi, ndinamva mawu akundiuza mʼChiheberi kuti, ‘Saulo! Saulo! Nʼchifukwa chiyani ukundizunza? Ukungovutika popitiriza kuchita ngati nyama imene ikuponya miyendo yake nʼkumamenya zisonga zotosera.’* 15  Koma ine ndinati: ‘Ambuye, ndinu ndani kodi?’ Ndipo Ambuye anati: ‘Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza. 16  Komabe dzuka ndipo uimirire. Ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki komanso mboni ya zinthu zonse zokhudza ine, zomwe waona ndiponso zimene ndidzakuonetsa.+ 17  Ndipo ndidzakupulumutsa kwa anthu awa komanso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutumiza+ 18  kuti ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mumdima+ nʼkuwapititsa kowala+ ndiponso kuwachotsa mʼmanja mwa Satana+ nʼkuwapititsa kwa Mulungu. Ukachite zimenezi kuti machimo awo akhululukidwe+ nʼkulandira cholowa pamodzi ndi oyeretsedwa chifukwa chondikhulupirira.’ 19  Choncho, Mfumu Agiripa, ine ndinaona kuti ndimvere zimene ndinaona mʼmasomphenya akumwambawo. 20  Kuyambira kwa anthu a ku Damasiko,+ kenako a ku Yerusalemu+ ndipo kenako mʼdziko lonse la Yudeya ndi anthu a mitundu ina, ndinafikitsa uthenga wakuti alape nʼkuyamba kulambira Mulungu pochita zinthu zosonyeza kulapa.+ 21  Nʼchifukwa chake Ayuda anandigwira mʼkachisi nʼkumafuna kundipha.+ 22  Komabe, popeza ndinaona Mulungu akundithandiza, ndikuchitirabe umboni kwa anthu otchuka ndiponso anthu wamba mpaka lero. Sindikunena chilichonse, koma zokhazo zimene aneneri ndi Mose ananena kuti zichitika.+ 23  Zoti Khristu adzavutika,+ ndipo monga woyamba kuukitsidwa,+ adzalalikira kwa anthu awa ndiponso kwa anthu a mitundu ina zokhudza kuwala.”+ 24  Pamene Paulo ankanena zimenezi podziteteza, Fesito ananena mokweza mawu kuti: “Wachita misala iwe Paulo! Kuphunzira kwambiri kwakupengetsa!” 25  Koma Paulo anati: “Wolemekezeka a Fesito, inetu sindinachite misala, koma ndikulankhula mawu a choonadi ndipo ndili bwinobwino. 26  Kunena zoona, ndikulankhula momasuka chifukwa mfumu imene ndikulankhula nayo ikudziwa bwino zimenezi. Sindikukayikira kuti palibe ngakhale chimodzi mwa zinthu zimenezi, chimene simukuchidziwa chifukwa zimenezi sizinachitike mwamseri.+ 27  Kodi inuyo, Mfumu Agiripa, mumakhulupirira zimene aneneri analemba? Ndikudziwa kuti mumazikhulupirira.” 28  Koma Agiripa anauza Paulo kuti: “Pa nthawi yochepa ukhoza kundikopa kuti ndikhale Mkhristu.” 29  Ndiyeno Paulo anati: “Kaya pa nthawi yochepa kapena yaitali, pemphero langa kwa Mulungu ndi lakuti, onse amene andimvetsera lero, osati inu nokha, akhale ngati ine kupatulapo maunyolo okhawa.” 30  Kenako mfumu inaimirira. Bwanamkubwa, Berenike ndiponso amuna amene anakhala nawo pamodzi nawonso anaimirira. 31  Koma pochoka anayamba kukambirana kuti: “Munthu uyu sanachite chilichonse choyenera kuphedwa kapena kumangidwa.”+ 32  Ndipo Agiripa anauza Fesito kuti: “Akanakhala kuti sanapemphe kukaonekera kwa Kaisara, munthu ameneyu akanamasulidwa.”+

Mawu a M'munsi

Zimenezi zinali ndodo zosongola zimene ankatosera nyama zapagoli kuti ziziyenda mofulumira.