Machitidwe a Atumwi 6:1-15
6 Pa nthawi imeneyo, pamene ophunzirawo ankapitiriza kuwonjezeka, Ayuda olankhula Chigiriki anayamba kudandaula za Ayuda olankhula Chiheberi. Ankadandaula chifukwa akazi amasiye a Chigiriki ankanyalanyazidwa pa nkhani yogawa chakudya cha tsiku ndi tsiku.+
2 Choncho atumwi 12 aja anaitana gulu la ophunzira nʼkunena kuti: “Nʼzosayenera kuti ife tisiye ntchito yophunzitsa mawu a Mulungu nʼkuyamba kugawa chakudya.+
3 Ndiye abale, fufuzani amuna 7 pagulu lanuli a mbiri yabwino,+ amene ali ndi mzimu komanso nzeru,+ kuti ife tiwapatse udindo woyangʼanira ntchito yofunikayi.+
4 Koma ife tidzipereka pa nkhani yokhudza kupemphera ndiponso kuphunzitsa mawu a Mulungu.”
5 Anthu onsewo anasangalala ndi mawu amenewa moti anasankha Sitefano, munthu wa chikhulupiriro cholimba ndiponso wodzaza ndi mzimu woyera. Anasankhanso Filipo,+ Purokoro, Nikanora, Timoni, Paremena ndi Nikolao wa ku Antiokeya amene analowa Chiyuda.
6 Ndiyeno anawabweretsa kwa atumwi, ndipo atapemphera, atumwiwo anawagwira pamutu* posonyeza kuti awapatsa udindo.+
7 Zitatero mawu a Mulungu anapitiriza kufalikira.+ Chiwerengero cha ophunzira chinkawonjezeka kwambiri+ mu Yerusalemu. Ndipo ansembe ambiri anakhala okhulupirira.+
8 Sitefano anali ndi mphamvu ndipo ankachita kuonekeratu kuti Mulungu ali naye. Iye ankachita zinthu zodabwitsa ndi zizindikiro zazikulu pakati pa anthu.
9 Koma anthu ena a mʼgulu lotchedwa Sunagoge wa Omasulidwa anafika limodzi ndi anthu ena a ku Kurene, a ku Alekizandiriya, ku Kilikiya ndiponso a ku Asia kudzatsutsana ndi Sitefano.
10 Koma iwo sanathe kulimbana ndi nzeru zake komanso mzimu woyera umene unkamutsogolera akamalankhula.+
11 Kenako ananyengerera amuna ena mwamseri kuti anene kuti: “Tamumva ife ameneyu akulankhula zinthu zonyoza Mose ndi Mulungu.”
12 Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri akulu, alembi ndiponso anthu ena. Ndiyeno anabwera modzidzimutsa nʼkumugwira ndipo anapita naye ku Khoti Lalikulu la Ayuda.
13 Iwo anabweretsa mboni zonama, zimene zinanena kuti: “Munthu uyu akungokhalira kulankhula mawu onyoza malo oyerawa ndiponso Chilamulo.
14 Mwachitsanzo, ife tamumva akunena kuti Yesu wa ku Nazareti uja adzawononga malo oyerawa nʼkusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”
15 Anthu onse amene anali mʼbwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda atayangʼanitsitsa Sitefano, anaona kuti nkhope yake ikuoneka ngati ya mngelo.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “anawaika manja.”