Malaki 4:1-6

  • Eliya adzabwera tsiku la Yehova lisanafike (1-6)

    • ‘Dzuwa la chilungamo lidzawala’ (2)

4  “Taonani! Tsiku loyaka ngati ngʼanjo likubwera,+ ndipo anthu onse odzikuza ndi onse ochita zoipa adzakhala ngati mapesi. Pa tsikulo iwo adzawonongedwa moti sipadzatsala mizu kapena nthambi zawo,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 2  “Koma inu amene mukulemekeza* dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakuwalirani ndipo kuwala kwake* kudzakhala ndi mphamvu yochiritsa. Mudzadumphadumpha ngati ana a ngʼombe amphongo onenepa.” 3  “Mudzapondaponda anthu oipa. Iwo adzakhala ngati fumbi kuphazi kwanu pa tsiku limene ndidzachitepo kanthu,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 4  “Kumbukirani Chilamulo cha Mose mtumiki wanga. Kumbukirani malamulo ndi ziweruzo zomwe ndinamupatsa ku Horebe kuti Aisiraeli onse azitsatira.+ 5  Tamverani! Tsiku la Yehova lalikulu ndi lochititsa mantha lisanafike,+ ndidzakutumizirani mneneri Eliya.+ 6  Iye adzachititsa mitima ya abambo kubwerera kwa ana awo+ ndi mitima ya ana kubwerera kwa abambo awo.* Adzachita zimenezi kuti ine ndisabwere kudzawononga dziko lapansi.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mukuopa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmapiko mwake.”
Kapena kuti, “adzachititsa mitima ya abambo kuti ikhale ngati ya ana ndipo mitima ya ana kuti ikhale ngati ya abambo.”