Wolembedwa ndi Maliko 12:1-44
12 Kenako anayamba kulankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ nʼkumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa nʼkumanga nsanja.+ Atatero anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina.+
2 Ndiye nyengo ya zipatso itakwana, anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso zamʼmunda wa mpesawo.
3 Koma iwo anamugwira nʼkumumenya ndipo anamubweza chimanjamanja.
4 Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema mʼmutu komanso kumuchitira zachipongwe.+
5 Anatumizanso wina koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha.
6 Iye anatsala ndi mmodzi yekha woti amutumize, mwana wake wokondedwa.+ Choncho anamutumizadi nʼkunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’
7 Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa! uyu ndi amene adzalandire cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’
8 Choncho anamugwira nʼkumupha ndipo anamutulutsa mʼmunda wa mpesawo.+
9 Kodi mwiniwake wa mundawo adzachita chiyani? Iye adzabwera nʼkupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.+
10 Kodi simunawerengepo zimene lemba limanena? Paja limanena kuti: ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.*+
11 Umenewu wachokera kwa Yehova* ndipo ndi wodabwitsa mʼmaso mwathu.’”+
12 Atamva zimenezo ankafuna kumugwira,* koma anaopa gulu la anthu, chifukwa iwo anadziwa kuti iye ananena fanizolo akuganiza za iwowo. Choncho anangomusiya nʼkuchokapo.+
13 Pambuyo pake anamutumizira ena mwa Afarisi ndi anthu amene ankatsatira Herode kuti akamupezere zifukwa pa zimene angalankhule.+
14 Atafika, iwo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo simuchita zinthu pongofuna kusangalatsa munthu, chifukwa simuyangʼana maonekedwe a anthu, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. Kodi nʼzololeka* kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?
15 Kodi tizipereka kapena tisamapereke?” Yesu anazindikira chinyengo chawo ndipo anawafunsa kuti: “Bwanji mukundiyesa? Bweretsani khobidi la dinari* kuno ndilione.”
16 Iwo anamubweretsera ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi komanso mawu akewa nʼzandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.”
17 Choncho Yesu ananena kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ Ndipo iwo anadabwa naye kwambiri.
18 Kenako Asaduki amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+
19 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati mwamuna wamwalira nʼkusiya mkazi koma osasiya mwana, mchimwene wake akuyenera kutenga mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.+
20 Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma anamwalira alibe ana.
21 Wachiwiri anakwatira mkaziyo, koma nayenso anamwalira osasiya mwana. Zinachitikanso chimodzimodzi kwa wachitatu.
22 Ndipo onse 7 aja sanasiye mwana. Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso.
23 Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.”
24 Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu?+
25 Chifukwa akufa akadzaukitsidwa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+
26 Koma pa mfundo yakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge mʼbuku la Mose munkhani yokhudza chitsamba chaminga, kuti Mulungu anamuuza kuti: ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakoboʼ?+
27 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.”+
28 Mmodzi wa alembi amene anafika nʼkuwamva akutsutsana, anadziwa kuti anawayankha bwino. Choncho anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo loyamba* ndi liti pa malamulo onse?”+
29 Yesu anayankha kuti: “Loyamba ndi lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova* Mulungu wathu ndi Yehova* mmodzi.
30 Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.’+
31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Palibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.”
32 Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi ndipo palibenso Mulungu wina kupatulapo iyeyo.’+
33 Ndipo kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, nʼzofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.”+
34 Yesu atazindikira kuti mlembiyo wayankha mwanzeru, anamuuza kuti: “Iwe suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” Koma panalibe amene analimba mtima kuti amufunsenso.+
35 Komabe, pamene Yesu ankaphunzitsa mʼkachisi, ananena kuti: “Nʼchifukwa chiyani alembi amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+
36 Kudzera mwa mzimu woyera,+ Davideyo ananena kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako pansi pa mapazi ako.”’+
37 Davideyo anamutchula kuti Ambuye, ndiye zingatheke bwanji kuti akhale mwana wake?”+
Ndipo gulu lalikulu la anthu linkamumvetsera mosangalala.
38 Pophunzitsapo Yesu ananenanso kuti: “Chenjerani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo komanso amakonda kupatsidwa moni mʼmisika.+
39 Amakondanso kukhala mʼmipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso mʼmalo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo.+
40 Iwo amalanda chuma cha akazi* amasiye ndipo amapereka mapemphero ataliatali pofuna kudzionetsera.* Anthu amenewa adzalandira chilango chowawa kwambiri.”*
41 Ndiyeno anakhala pansi pamalo amene ankatha kuona moponyeramo zopereka*+ ndipo anayamba kuona mmene gulu la anthu linkaponyera ndalama moponyera zoperekamo. Anaona anthu ambiri olemera akuponyamo makobidi ambiri.+
42 Kenako panafika mkazi wamasiye wosauka ndipo anaponyamo timakobidi tiwiri tatingʼono, tochepa mphamvu kwambiri.*+
43 Ndiyeno Yesu anaitana ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama moponyera zoperekamo.+
44 Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “kumumanga.”
^ Kapena kuti, “nʼzoyenera.”
^ Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “lofunika kwambiri.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “mʼmipando yabwino kwambiri.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Iwo amadya nyumba za akazi.”
^ Kapena kuti, “mwachiphamaso.”
^ Kapena kuti, “champhamvu.”
^ Kapena kuti, “bokosi la zopereka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malepitoni awiri amene anali okwana kwadiransi imodzi.” Onani Zakumapeto B14.