Maliro 1:1-22

  • Yerusalemu anayerekezeredwa ndi mkazi wamasiye

    • Yerusalemu anatsala yekhayekha wopanda munthu (1)

    • Machimo aakulu a Ziyoni (8, 9)

    • Ziyoni anakanidwa ndi Mulungu (12-15)

    • Palibe aliyense amene akutonthoza Ziyoni (17)

א [Aleph]* 1  Yerusalemu amene anali ndi anthu ambiri tsopano watsala yekhayekha wopanda anthu.+ Amene anali ndi anthu ambiri poyerekeza ndi mitundu ina, wakhala ngati mkazi wamasiye.+ Amene anali wolemekezeka pakati pa zigawo zina wayamba kugwira ntchito yaukapolo.+ ב [Beth]  2  Iye akulira kwambiri usiku+ ndipo misozi ikutsika mʼmasaya ake. Pa anthu onse amene ankamukonda, palibe aliyense amene akumutonthoza.+ Anzake onse amuchitira zachinyengo+ ndipo asanduka adani ake. ג [Gimel]  3  Yuda watengedwa kupita kudziko lina+ ndipo akuvutika komanso akugwira ntchito yaukapolo.+ Iye akuyenera kukhala pakati pa mitundu ina ya anthu+ ndipo sanapeze malo oti azikhala mwamtendere. Onse amene amamufunafuna amupeza ali pamavuto. ד [Daleth]  4  Misewu yopita ku Ziyoni ikulira chifukwa palibe amene akupita kuchikondwerero.+ Mageti ake onse awonongedwa.+ Ansembe ake akuusa moyo. Anamwali* ake agwidwa ndi chisoni ndipo iyeyo akumva ululu mumtima. ה [He]  5  Tsopano adani ake akumulamulira. Iwo sakuda nkhawa.+ Yehova wamuchititsa kuti akhale ndi chisoni chifukwa cha kuchuluka kwa machimo ake.+ Ana ake agwidwa ndi adani ndipo atengedwa kupita ku ukapolo.+ ו [Waw]  6  Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoni* wamuchokera.+ Akalonga ake ali ngati mbawala zamphongo zimene zikusowa msipu,Ndipo akuyenda mofooka pamaso pa amene akuwathamangitsa. ז [Zayin]  7  Pa nthawi imene ankazunzika komanso pamene ankasowa pokhala, Yerusalemu anakumbukiraZinthu zake zonse zamtengo wapatali zimene anali nazo kalekale.+ Anthu ake atagwidwa ndi adani moti panalibe munthu woti amuthandize,+Adaniwo anamuona ndipo anamuseka* chifukwa chakuti wagwa.+ ח [Heth]  8  Yerusalemu wachita tchimo lalikulu.+ Nʼchifukwa chake wakhala chinthu chonyansa. Anthu onse amene ankamulemekeza ayamba kumuona ngati chinthu chochititsa manyazi, chifukwa aona maliseche ake.+ Iyenso akulira+ ndipo watembenukira kumbali chifukwa cha manyazi. ט [Teth]  9  Zovala zake zadetsedwa. Iye sanaganizire za tsogolo lake.+ Wagwa modabwitsa ndipo palibe aliyense woti amutonthoze. Inu Yehova, onani kuvutika kwanga, chifukwa mdani wanga akudzitukumula.+ י [Yod] 10  Mdani wamulanda zinthu zake zonse zamtengo wapatali.+ Yerusalemu waona anthu a mitundu ina akulowa mʼmalo ake opatulika,+Mitundu imene munalamula kuti isamalowe mumpingo wanu. כ [Kaph] 11  Anthu ake onse akuusa moyo. Iwo akufunafuna chakudya.+ Asinthanitsa zinthu zawo zamtengo wapatali ndi chakudya kuti akhale ndi moyo. Inu Yehova ndiyangʼaneni. Onani kuti ndakhala ngati mkazi* wachabechabe. ל [Lamed] 12  Inu nonse amene mukudutsa munsewu, kodi mukuona ngati imeneyi ndi nkhani yaingʼono? Ndiyangʼaneni kuti muone. Kodi palinso ululu wina woposa ululu umene ndikumva chifukwa cholangidwa,Ululu umene Yehova wachititsa kuti ndiumve pa tsiku la mkwiyo wake woyaka moto?+ מ [Mem] 13  Iye watumiza moto mʼmafupa mwanga+ kuchokera kumwamba ndipo wafooketsa fupa lililonse. Watchera ukonde kuti ukole mapazi anga. Wandikakamiza kuti ndibwerere mʼmbuyo. Wandichititsa kuti ndikhale mkazi amene wasiyidwa yekhayekha. Ndikudwala tsiku lonse. נ [Nun] 14  Machimo anga amangidwa mʼkhosi mwanga ngati goli. Iye wawamanga mwamphamvu ndi dzanja lake. Aikidwa mʼkhosi mwanga moti mphamvu zanga zatha. Yehova wandipereka mʼmanja mwa anthu amene sindingathe kulimbana nawo.+ ס [Samekh] 15  Yehova wandichotsera anthu anga onse amphamvu nʼkuwakankhira pambali.+ Wandiitanitsira msonkhano kuti aphwanye anyamata anga.+ Yehova wapondaponda namwali, mwana wamkazi wa Yuda, moponderamo mphesa.+ ע [Ayin] 16  Ndikulira chifukwa cha zinthu zimenezi.+ Misozi ikutuluka mʼmaso mwanga. Chifukwa aliyense amene akananditonthoza kapena kunditsitsimula, ali kutali ndi ine. Ana anga awonongedwa ndipo mdani wanga wapambana. פ [Pe] 17  Ziyoni watambasula manja ake.+ Palibe aliyense woti amutonthoze. Yehova walamula adani onse a Yakobo amene amuzungulira kuti amuukire.+ Yerusalemu wakhala chinthu chonyansa kwa iwo.+ צ [Tsade] 18  Yehova ndi wolungama,+ koma ine ndapandukira malamulo ake.*+ Mvetserani, inu anthu a mitundu yonse ndipo muone ululu umene ndikumva. Anamwali* anga ndi anyamata anga atengedwa kupita ku ukapolo.+ ק [Qoph] 19  Ndaitana anthu amene ankandikonda, koma anthuwo andichitira zachinyengo.+ Ansembe anga ndiponso akuluakulu atha mumzinda.Atha pamene amafunafuna chakudya choti adye kuti akhale ndi moyo.+ ר [Resh] 20  Taonani, inu Yehova. Ine ndili pamavuto aakulu. Mʼmimba mwanga mukubwadamuka. Mtima wanga wasweka, chifukwa ndapanduka kwambiri.+ Panja, lupanga lapha ana anga.+ Mʼnyumba, anthu akufanso. ש [Shin] 21  Anthu amva mmene ndikuusira moyo, koma palibe aliyense woti anditonthoze. Adani anga onse amva za tsoka langa. Iwo akusangalala chifukwa inu mwatibweretsera tsoka.+ Koma inu mubweretsadi tsiku limene munanena,+ kuti iwowo adzakhale ngati ine.+ ת [Taw] 22  Kuipa kwawo konse kuonekere pamaso panu ndipo muwalange koopsa,+Ngati mmene mwandilangira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse. Ndikuusa moyo kwambiri ndipo mtima wanga ukudwala.

Mawu a M'munsi

Chaputala 1-4 ndi nyimbo zoimba polira ndipo anazilemba potsatira afabeti ya Chiheberi kapena mwandakatulo.
Kapena kuti, “Atsikana.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Kapena kuti, “anamunyoza.”
Apa Yerusalemu akumuyerekezera ndi munthu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pake.”
Kapena kuti, “Atsikana.”