Salimo 1:1-6
1 Wosangalala ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa,Saima mʼnjira ya anthu ochimwa,+Ndipo sakhala pansi pamodzi ndi anthu onyoza.+
2 Koma amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova,+Ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama* chilamulocho masana ndi usiku.+
3 Iye adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa ngalande za madzi,Umene umabereka zipatso mʼnyengo yake,Umenenso masamba ake safota.
Ndipo zonse zimene amachita zimamuyendera bwino.+
4 Koma si mmene oipa alili.Iwo ali ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo.
5 Nʼchifukwa chake oipa sadzalephera kulangidwa,+Ndipo ochimwa sadzapezekanso pamene pali olungama.+
6 Chifukwa Yehova amadziwa zochita za olungama,+Koma oipa adzawonongedwa pamodzi ndi zochita zawo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “ndi kusinkhasinkha.”
^ “Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa popuntha mbewu ngati mpunga ndipo amatha kuuluzika ndi mphepo.