Salimo 100:1-5
Nyimbo yoyamikira.
100 Dziko lonse lapansi lifuulire Yehova mosangalala chifukwa wapambana.+
2 Tumikirani Yehova mokondwera.+
Bwerani kwa iye mukufuula mosangalala.
3 Dziwani* kuti Yehova ndi Mulungu.+
Iye ndi amene anatipanga, ndipo ndife ake.+
Ndife anthu ake komanso nkhosa zimene akuweta.+
4 Lowani pamageti ake mukumuyamikira,+Lowani mʼmabwalo ake mukumutamanda.+
Muyamikeni, tamandani dzina lake.+
5 Chifukwa Yehova ndi wabwino.+Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,Ndipo kukhulupirika kwake kudzakhalapo ku mibadwo yonse.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Vomerezani.”