Salimo 126:1-6

  • Kubwezeretsedwa kosangalatsa kwa Ziyoni

    • “Yehova watichitira zazikulu” (3)

    • Kusiya kulira nʼkuyamba kusangalala (5, 6)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 126  Yehova atabwezeretsa anthu a ku Ziyoni kuchokera ku ukapolo,+Tinkangoona ngati tikulota.  2  Pa nthawiyo tinasekaNdipo tinasangalala kwambiri.+ Pa nthawi imeneyo anthu a mitundu ina anayamba kuuzana kuti: “Yehova wachitira anthu amenewa zinthu zazikulu.”+  3  Yehova watichitira zazikulu,+Ndipo tasangalala kwambiri.  4  Inu Yehova, bwezeretsani anthu athu amene anagwidwa ukapolo,Ngati mmene mvula imadzazitsira mitsinje ya ku Negebu.*  5  Amene akukhetsa misozi pofesa mbewuAdzakolola akufuula mosangalala.  6  Amene akupitabe kumunda, ngakhale kuti akulira,Atasenza thumba lake la mbewu,Ndithu adzabwerako akufuula mosangalala,+Atasenza mtolo wake wa zokolola.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “imadzazitsira makhwawa akumʼmwera.”