Salimo 129:1-8
-
Kuukiridwa koma osagonjetsedwa
-
Odana ndi Ziyoni achititsidwa manyazi (5)
-
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
129 “Akhala akundiukira nthawi zonse kuyambira ndili mnyamata,”+
Tsopano Isiraeli anene kuti,
2 “Akhala akundiukira nthawi zonse kuyambira ndili mnyamata,+Koma sanandigonjetse.+
3 Olima ndi ngʼombe andilima pamsana.+Iwo alima mizere italiitali.”
4 Koma Yehova ndi wolungama.+Iye wadula zingwe za oipa.+
5 Onse amene amadana ndi Ziyoni,Adzanyozeka ndipo adzabwerera mwamanyazi.+
6 Adzakhala ngati udzu umene wamera padengaUmene umauma usanazulidwe,
7 Umene sungadzaze mʼdzanja la munthu amene akukololaKapena mʼmanja mwa munthu amene akumanga mitolo ya zokolola.
8 Anthu odutsa sadzanena kuti:
“Madalitso a Yehova akhale nanu.Tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”