Salimo 137:1-9
137 Tinakhala pansi mʼmphepete mwa mitsinje ya ku Babulo.+
Tinalira titakumbukira Ziyoni.+
2 Tinapachika azeze athu+Pamitengo ya msondodzi imene inali mmenemo.*
3 Chifukwa kumeneko, anthu amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+Amene ankatinyozawo ankafuna kuti tiwasangalatse. Iwo anati:
“Tiimbireni nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.”
4 Tingaimbe bwanji nyimbo ya YehovaMʼdziko lachilendo?
5 Ndikakuiwala iwe Yerusalemu,Dzanja langa lamanja liiwale luso lake.+
6 Lilime langa limamatire mʼkamwa mwangaNgati sindingakukumbukire,Ngati sindingaike Yerusalemu pamwambaPa chilichonse chimene chimandisangalatsa kwambiri.+
7 Inu Yehova, kumbukiraniZimene Aedomu ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa.
Iwo anati: “Gwetsani mzindawo! Ugwetseni mpaka pamaziko ake!”+
8 Iwe mwana wamkazi wa Babulo,* amene watsala pangʼono kuwonongedwa,+Wosangalala adzakhala amene adzakubwezereZimene iwe watichitira.+
9 Wosangalala adzakhala amene adzagwire ana akoNʼkuwaphwanya powawombetsa pathanthwe.+
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza mu Babulo.
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.