Salimo 139:1-24

  • Mulungu amadziwa bwino atumiki ake

    • Palibe amene angathawe mzimu wa Mulungu (7)

    • “Munandipanga modabwitsa” (14)

    • “Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza” (16)

    • “Munditsogolere mʼnjira yamuyaya” (24)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide. 139  Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.+  2  Inu mumadziwa ndikakhala pansi komanso ndikaimirira.+ Mumadziwa maganizo anga muli kutali.+  3  Mumandiona* ndikamayenda komanso ndikagona.Mumadziwa chilichonse chimene ndikuchita.+  4  Ndisananene kanthu,Inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.+  5  Mwandizungulira mbali zonse,Ndipo mwaika dzanja lanu pa ine.  6  Kwa ine nʼzovuta kwambiri kuti ndimvetse zinthu zimenezi.* Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+  7  Kodi ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu,Ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu?+  8  Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko,Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda,* taonani! inunso mudzakhala komweko.+  9  Ngati ndingauluke pamapiko amʼbandakuchaKuti ndikakhale mʼnyanja yakutali kwambiri, 10  Ngakhale kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogoleraNdipo dzanja lanu lamanja lidzandigwira.+ 11  Ngati ndinganene kuti: “Ndithudi mdima undibisa!” Pamenepo mdima umene wandizungulira udzasanduka kuwala. 12  Ngakhale mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,Koma usiku udzawala ngati masana.+Mdima udzangokhala ngati kuwala kwa inu.+ 13  Inu munapanga impso zanga.Munanditeteza* ndili mʼmimba mwa mayi anga.+ 14  Ndimakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa+ ndipo zimenezi zimandichititsa mantha. Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+Ine ndikudziwa bwino zimenezi. 15  Mafupa anga sanali obisika kwa inuPa nthawi imene ndinkapangidwa kumalo amene aliyense sakanatha kuona,Pamene munkandiwomba ngati nsalu mʼmalo apansi kwambiri padziko lapansi.+ 16  Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza.*Ziwalo zanga zonse zinalembedwa mʼbuku lanuMʼbukumo munalembedwa za masiku amene zinapangidwa,Zinalembedwa chiwalo chilichonse chisanapangidwe. 17  Choncho kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambiri, inu Mulungu,+ Ndipo ndi ochuluka kwambiri.+ 18  Nditati ndiyese kuwawerenga, angakhale ochuluka kwambiri kuposa mchenga.+ Podzuka ndingakhale ndikuwawerengabe.*+ 19  Inu Mulungu, zikanakhala bwino mukanapha oipa.+ Zikanatero anthu achiwawa* akanachoka kwa ine, 20  Anthu amene amanena zinthu zokhudza inu ndi zolinga zoipa.*Amenewa ndi adani anu amene amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.+ 21  Inu Yehova, pajatu ine ndimadana ndi anthu amene amadana nanu,+Ndipo ndimanyansidwa ndi anthu amene amakupandukirani.+ 22  Ndimadana nawo kwambiri.+Kwa ine akhala adani enieni. 23  Ndifufuzeni inu Mulungu, ndipo mudziwe mtima wanga.+ Ndifufuzeni ndipo mudziwe maganizo anga amene akundidetsa nkhawa.*+ 24  Muone ngati mwa ine muli chilichonse choipa,+Ndipo munditsogolere+ mʼnjira yamuyaya.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mumandiyeza.”
Kapena kuti, “Zinthu zimenezi ndi zodabwitsa kwambiri kwa ine.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “Munandiwumba pamodzi.”
“Mluza” ndi mwana amene wangoyamba kumene kupangidwa mʼmimba mwa mayi ake.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimakhala ndidakali ndi inu.”
Kapena kuti, “amene ali ndi mlandu wa magazi.”
Kapena kuti, “Anthu amene amanena zamʼmutu mwawo zokhudza inu.”
Kapena kuti, “amene akundisowetsa mtendere.”