Salimo 145:1-21

  • Kutamanda Mulungu, Mfumu yaikulu

    • ‘Ndidzalengeza za ukulu wa Mulungu’ (6)

    • “Yehova ndi wabwino kwa anthu onse” (9)

    • “Okhulupirika anu adzakutamandani” (10)

    • Ufumu wamuyaya wa Mulungu (13)

    • Dzanja la Mulungu limakwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse (16)

Nyimbo ya Davide yotamanda Mulungu. א [Aleph] 145  Ndidzakukwezani, inu Mfumu ndi Mulungu wanga,+Ndidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.+ ב [Beth]  2  Ndidzakutamandani tsiku lonse.+Ndidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.+ ג [Gimel]  3  Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri,+Palibe amene angamvetse ukulu wake.+ ד [Daleth]  4  Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo.Adzanena za ntchito zanu zamphamvu.+ ה [He]  5  Iwo adzanena za mphamvu zanu zodabwitsa+Ndipo ndidzaganizira mozama za ntchito zanu zodabwitsa. ו [Waw]  6  Anthu adzanena za zochita zanu zochititsa mantha,*Ndipo ine ndidzalengeza za ukulu wanu. ז [Zayin]  7  Iwo azidzalankhula mosangalala akadzakumbukira ubwino wanu wochuluka,+Ndipo adzafuula mosangalala chifukwa cha chilungamo chanu.+ ח [Heth]  8  Yehova ndi wokoma mtima* komanso wachifundo,+Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi chikondi chokhulupirika.+ ט [Teth]  9  Yehova ndi wabwino kwa aliyense,+Ndipo ntchito zake zonse zimasonyeza kuti ndi wachifundo. י [Yod] 10  Ntchito zanu zonse zidzakutamandani, inu Yehova,+Ndipo okhulupirika anu adzakutamandani.+ כ [Kaph] 11  Iwo adzalengeza za ulemerero wa ufumu wanu+Komanso adzalankhula za mphamvu zanu,+ ל [Lamed] 12  Kuti anthu adziwe za ntchito zanu zamphamvu+Ndiponso kukula kwa ulemerero wa ufumu wanu.+ מ [Mem] 13  Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,Ndipo ulamuliro wanu udzakhalapo ku mibadwo yonse.+ ס [Samekh] 14  Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pangʼono kugwa+Ndipo amadzutsa onse amene awerama chifukwa cha mavuto.+ ע [Ayin] 15  Zamoyo zonse zimayangʼana kwa inu mwachiyembekezo.Mumazipatsa chakudya pa nyengo yake.+ פ [Pe] 16  Mumatambasula dzanja lanuNʼkukwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse.+ צ [Tsade] 17  Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,+Ndipo ndi wokhulupirika pa chilichonse chimene amachita.+ ק [Qoph] 18  Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana,+Onse amene amamuitana mʼchoonadi.*+ ר [Resh] 19  Amakwaniritsa zolakalaka za anthu amene amamuopa.+Amamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo amawapulumutsa.+ ש [Shin] 20  Yehova amayangʼanira onse amene amamukonda,+Koma oipa onse adzawawononga.+ ת [Taw] 21  Pakamwa panga padzalankhula zotamanda Yehova.+Zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zochita zanu zamphamvu.”
Kapena kuti, “wachisomo.”
Kapena kuti, “moona mtima.”