Salimo 146:1-10
146 Tamandani Ya!*+
Moyo wanga wonse utamande Yehova.+
2 Ndidzatamanda Yehova kwa moyo wanga wonse.
Ndidzaimbira Mulungu wanga nyimbo zomutamanda kwa moyo wanga wonse.
3 Musamakhulupirire anthu olemekezeka*Kapena mwana wa munthu amene sangabweretse chipulumutso.+
4 Mpweya* wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.+
5 Wosangalala ndi munthu amene amathandizidwa ndi Mulungu wa Yakobo,+Amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake,+
6 Amene anapanga kumwamba komanso dziko lapansi,Nyanja ndiponso zonse zimene zili mmenemo,+Amene amakhala wokhulupirika nthawi zonse,+
7 Amene amaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa anthu amene achitiridwa chinyengo,Amene amapereka chakudya kwa anthu anjala.+
Yehova akumasula anthu amene ali mʼndende.*+
8 Yehova akutsegula maso a anthu amene ali ndi vuto losaona.+Yehova akudzutsa anthu amene awerama chifukwa cha mavuto.+Yehova amakonda anthu olungama.
9 Yehova akuteteza alendo amene akukhala mʼdziko la eni.Amathandiza mwana wamasiye komanso mkazi wamasiye.+Koma amasokoneza mapulani a anthu oipa.*+
10 Yehova adzakhala Mfumu kwamuyaya,+Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzakhala Mfumu ku mibadwomibadwo.
Tamandani Ya!*
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “Musamakhulupirire akalonga.”
^ Kapena kuti, “Mzimu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amangidwa.”
^ Kapena kuti, “Koma amakhotetsa njira ya anthu oipa.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.