Salimo 21:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala chifukwa mwasonyeza kuti ndinu wamphamvu.+Ikusangalala kwambiri chifukwa mwaipulumutsa.+
2 Mwaipatsa zimene mtima wake umalakalaka,+Ndipo simunaimane zopempha za milomo yake. (Selah)
3 Mumaipatsa madalitso ambiri,Ndipo munaiveka chisoti chachifumu chagolide woyenga bwino.+
4 Mfumuyo inakupemphani moyo wautali ndipo munaipatsadi.+Munaipatsa moyo wautali* kuti ikhale mpaka kalekale.
5 Ulemerero wake ndi waukulu chifukwa mwaipulumutsa.+
Mwaipatsa ulemu ndi ulemerero.
6 Mwaipatsa madalitso mpaka kalekale.+Mwaichititsa kuti ikhale yosangalala chifukwa muli nayo pafupi.*+
7 Mfumu imakhulupirira Yehova.+Chifukwa cha chikondi chokhulupirika cha Wamʼmwambamwamba, mfumuyo sidzagwedezeka.*+
8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse.Dzanja lanu lamanja lidzapeza anthu amene amadana nanu.
9 Mudzawawononga ngati kuti mwawaponya mungʼanjo yamoto, pa nthawi imene mudzaonekere.
Yehova adzawameza atakwiya ndipo moto udzawapsereza.+
10 Ana awo mudzawawononga kuwachotsa padziko lapansi,Ndipo mbadwa zawo mudzazichotsa pakati pa ana a anthu.
11 Chifukwa akonza zoti akuchitireni zoipa.+Akonza ziwembu zimene zidzalephereka.+
12 Inu mudzawachititsa kuti athawe.+Mudzachita zimenezi powalozetsa* muvi wa uta wanu.
13 Nyamukani, inu Yehova, muonetse mphamvu zanu.
Tidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ochuluka.”
^ Kapena kuti, “chifukwa ili pamaso panu.”
^ Kapena kuti, “sidzadzandira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “polozetsa nkhope zawo.”