Salimo 27:1-14
Salimo la Davide.
27 Yehova ndi kuwala kwanga+ komanso ndi amene amandipulumutsa.
Ndingaope ndani?+
Yehova ali ngati malo amene amateteza moyo wanga.+
Ndingachite mantha ndi ndani?
2 Anthu oipa atandiukira kuti adye mnofu wanga,+Adani angawo ndi amene anapunthwa nʼkugwa.
3 Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire,Mtima wanga sudzachita mantha.+
Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika,Pameneponso ndidzadalira Mulungu.
4 Ndapempha chinthu chimodzi kwa Yehova,Chimenecho ndi chimene ndikuchilakalaka.Chinthu chake nʼchakuti, ndikhale mʼnyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+Kuti ndione ubwino wa Yehova,Komanso kuti ndiyangʼane kachisi wake* moyamikira.*+
5 Chifukwa pa tsiku la tsoka, adzandibisa mʼmalo ake otetezeka.+Adzandibisa mʼmalo obisika a mutenti yake.+Adzandiika pamwamba, pathanthwe.+
6 Tsopano ndapambana pamaso pa adani anga onse amene andizungulira.Ndidzapereka nsembe patenti yake ndikufuula mosangalala.Ndidzaimba nyimbo zotamanda Yehova.
7 Inu Yehova, ndimvetsereni pamene ndikuitana.+Ndikomereni mtima ndipo mundiyankhe.+
8 Mtima wanga wandikumbutsa za lamulo lanu lakuti:
“Funafunani nkhope yanga anthu inu.”
Ndidzafunafuna nkhope yanu, inu Yehova.+
9 Musandibisire nkhope yanu.+
Musabweze mtumiki wanu mutakwiya.
Inu ndi amene mumandithandiza.+Musanditaye kapena kundisiya, inu Mulungu amene mumandipulumutsa.
10 Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya,+Yehova adzanditenga.+
11 Ndilangizeni, inu Yehova, kuti ndiyende mʼnjira yanu.+Nditsogolereni mʼnjira yoyenera kuti nditetezeke kwa adani anga.
12 Musandipereke kwa adani anga,+Chifukwa mboni zabodza zikundinamizira mlandu,+Ndipo akundiopseza kuti andichitira zachiwawa.
13 Kodi ndikanakhala ndili kuti ndikanapanda kukhala ndi chikhulupiriroChoti ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo?*+
14 Yembekezera Yehova.+Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.+
Inde, yembekezera Yehova.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “malo opatulika ake.”
^ Kapena kuti, “Komanso kuti ndiyangʼane ndi kuganizira mozama za kachisi wake.”
^ Mabaibulo ena amati, “Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi; ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.”