Salimo 37:1-40
-
Anthu amene amadalira Yehova zinthu zimawayendera bwino
Salimo la Davide.
א [Aleph]
37 Usakhumudwe* chifukwa cha anthu oipaKapena kuchitira nsanje anthu ochita zoipa.+
2 Iwo adzafota mwamsanga ngati udzu+Ndipo adzanyala ngati msipu wobiriwira.
ב [Beth]
3 Uzikhulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino.+Ukhale padziko lapansi* ndipo uzichita zinthu mokhulupirika.+
4 Uzisangalala* chifukwa cha Yehova,Ndipo adzakupatsa zimene mtima wako umalakalaka.
ג [Gimel]
5 Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako,*+Uzimudalira ndipo iye adzakuthandiza.+
6 Iye adzachititsa kuti kulungama kwako kuwale ngati mʼmawa,Ndipo chilungamo chako adzachichititsa kuti chiwale ngati dzuwa masana.
ד [Daleth]
7 Khala chete pamaso pa Yehova+Ndipo umuyembekezere moleza mtima.
Usakhumudwe ndi munthuAmene amakonza ziwembu nʼkuzikwaniritsa popanda vuto lililonse.+
ה [He]
8 Usapse mtima ndipo uzipewa kukwiya.+Usapse mtima nʼkuchita zoipa.*
9 Chifukwa anthu oipa adzaphedwa,+Koma amene akuyembekezera Yehova adzalandira dziko lapansi.+
ו [Waw]
10 Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso.+Udzayangʼana pamene ankakhala,Ndipo sadzapezekapo.+
11 Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi,+Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.+
ז [Zayin]
12 Munthu woipa amakonzera chiwembu munthu wolungama,+Ndipo amamukukutira mano.
13 Koma Yehova adzamuseka,Chifukwa akudziwa kuti mapeto ake adzafika.+
ח [Heth]
14 Oipa asolola malupanga awo ndipo akunga mauta* awo,Kuti agwetse oponderezedwa ndi osauka,Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zolungama.
15 Koma lupanga lawo lidzalasa mtima wawo womwe,+Mauta awo adzathyoledwa.
ט [Teth]
16 Zinthu zochepa zimene munthu wolungama ali nazo ndi zabwinoKusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+
17 Chifukwa manja a anthu oipa adzathyoledwa,Koma Yehova adzathandiza anthu olungama.
י [Yod]
18 Yehova amadziwa mavuto amene anthu osalakwa akukumana nawo,*Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+
19 Pa nthawi ya tsoka sadzachita manyazi,Ndipo pa nthawi ya njala adzakhala ndi chakudya chochuluka.
כ [Kaph]
20 Koma oipa onse adzatheratu,+Adani a Yehova adzasowa mofulumira ngati malo okongola odyetsera ziweto amene msipu wake wobiriwira suchedwa kufota.Iwo adzatha mofulumira ngati utsi.
ל [Lamed]
21 Munthu woipa amabwereka zinthu za ena koma osabweza,Koma wolungama amakhala wowolowa manja* ndipo amagawira ena zinthu zake.+
22 Anthu amene Mulungu wawadalitsa adzalandira dziko lapansi,Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+
מ [Mem]
23 Yehova akasangalala ndi njira za munthu+Amamusonyeza zoyenera kuchita pa moyo wake.+
24 Ngakhale atapunthwa, sadzagweratu,+Chifukwa Yehova wamugwira dzanja kuti amuthandize.*+
נ [Nun]
25 Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula,Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+
26 Nthawi zonse amakongoza ena zinthu zake mokoma mtima,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso.
ס [Samekh]
27 Pewani kuchita zoipa ndipo muzichita zabwino,+Mukatero mudzakhala padziko lapansi mpaka kalekale.
28 Chifukwa Yehova amakonda chilungamo,Ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.+
ע [Ayin]
Adzawateteza nthawi zonse.+Koma mbadwa za anthu oipa zidzaphedwa.+
29 Olungama adzalandira dziko lapansi,+Ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.+
פ [Pe]
30 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,*Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+
31 Chilamulo cha Mulungu wake chili mumtima mwake.+Iye adzachitsatira nthawi zonse.+
צ [Tsade]
32 Woipa amayangʼanitsitsa munthu wolungama,Ndipo amafuna kuti amuphe.
33 Koma Yehova sadzasiya wolungama mʼmanja mwa woipayo+Kapena kumupeza wolakwa akamaweruzidwa.+
ק [Qoph]
34 Yembekezera Yehova ndi kutsatira njira zake,Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi.
Oipa akamadzaphedwa,+ iwe udzaona.+
ר [Resh]
35 Ine ndaona munthu wankhanza komanso woipaZinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+
36 Koma anafa mwadzidzidzi ndipo sanapezekenso.+Ndinamufunafuna ndipo sindinamupeze.+
ש [Sin]
37 Onani munthu wosalakwa,*Ndipo yangʼanitsitsani munthu wolungama,+Chifukwa tsogolo la munthu ameneyo lidzakhala lamtendere.+
38 Koma anthu onse ochimwa adzawonongedwa.Mʼtsogolo, anthu oipa adzaphedwa.+
ת [Taw]
39 Chipulumutso cha anthu olungama chimachokera kwa Yehova.+Iye ndi malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya mavuto.+
40 Yehova adzawathandiza nʼkuwapulumutsa.+
Adzawalanditsa kwa oipa nʼkuwapulumutsa,Chifukwa athawira kwa iye.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Usakwiye.”
^ Kapena kuti, “mʼdzikoli.”
^ Kapena kuti, “Uzipeza chisangalalo chako chachikulu.”
^ Kapena kuti, “Pereka njira yako kwa Yehova.”
^ Mabaibulo ena amati, “chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoipa.”
^ Kapena kuti, “zingwe.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amadziwa masiku a anthu osalakwa.”
^ Kapena kuti, “amakomera ena mtima.”
^ Kapena kuti, “akumuthandiza ndi Dzanja Lake.”
^ Kapena kuti, “pamalankhula zinthu zanzeru chapansipansi.”
^ Kapena kuti, “munthu wokhulupirika.”