Salimo 41:1-13

  • Pemphero la munthu amene akudwala pabedi lake

    • Mulungu amasamalira anthu amene akudwala (3)

    • Kuukiridwa ndi mnzanga wapamtima (9)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 41  Wosangalala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.  2  Yehova adzamuteteza nʼkusunga moyo wake. Anthu ena adzaona kuti akusangalala,+Ndipo Mulungu sadzamupereka kwa adani ake.*+  3  Yehova adzathandiza munthu woganizira wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.+Mudzamusamalira bwino kwambiri pa nthawi imene akudwala.  4  Ine ndinati: “Inu Yehova, ndikomereni mtima.+ Ndichiritseni,+ chifukwa ndakuchimwirani.”+  5  Koma adani anga amanena zoipa zokhudza ine kuti: “Kodi ameneyu afa liti kuti dzina lake liiwalike?”  6  Mmodzi wa iwo akabwera kudzandiona, sanena zinthu moona mtima. Amasonkhanitsa nkhani zoipa.Akatero amachoka nʼkukafalitsa nkhani zoipazo.  7  Onse amene amadana nane akunongʼonezana zokhudza ine.Akupangana zoti andichitire chiwembu. Iwo akuti:  8  “Chinthu chochititsa mantha chamuchitikira.Tsopano popeza iye ali chigonere, sadzadzukanso.”+  9  Ngakhale munthu amene ndinkakhala naye mwamtendere, amene ndinkamukhulupirira,+Munthu amene ankadya chakudya changa, watukula chidendene chake nʼkundiukira.+ 10  Koma inu Yehova, ndikomereni mtima nʼkundidzutsa,Kuti ndiwapatse chilango chifukwa cha zimene anachita. 11  Mdani wanga akapanda kundigonjetsa nʼkufuula mosangalala, Ndidzadziwa kuti mukusangalala nane.+ 12  Koma ine mumandithandiza chifukwa choti ndine wokhulupirika,+Ndipo mudzasangalala nane mpaka kalekale.*+ 13  Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli,Kuyambira panopo mpaka kalekale.*+ Ame! Ame!

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kwa adani ake kuti achite naye zimene akufuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mudzandiika pamaso panu mpaka kalekale.”
Kapena kuti, “Kuyambira kalekale mpaka kalekale.”