Salimo 47:1-9

  • Mulungu ndi Mfumu yolamulira dziko lonse lapansi

    • ‘Yehova ndi wochititsa mantha’ (2)

    • Imbani nyimbo zotamanda Mulungu (6, 7)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ 47  Inu anthu nonse, ombani mʼmanja. Fuulani mosangalala chifukwa Mulungu wapambana.  2  Chifukwa Yehova, Wamʼmwambamwamba ndi wochititsa mantha,+Iye ndi Mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.+  3  Iye amagonjetsa mitundu ya anthu kuti tiziilamulira.Amaika mitundu ya anthu pansi pa mapazi athu.+  4  Amatisankhira cholowa,+Chimene Yakobo, amene amamukonda, amasangalala nacho.+ (Selah)  5  Mulungu wakwera kumalo ake, anthu akufuula mosangalala,Yehova wakwera kumalo ake, anthu akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.  6  Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zotamanda Mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.  7  Chifukwa Mulungu ndi Mfumu ya dziko lonse lapansi.+Imbani nyimbo zotamanda ndiponso sonyezani kuti ndinu ozindikira.  8  Mulungu wakhala Mfumu ya mitundu ya anthu.+ Mulungu wakhala pampando wake wachifumu wopatulika.  9  Atsogoleri a mitundu ya anthu asonkhana pamodziNdi anthu a Mulungu wa Abulahamu. Chifukwa Mulungu ali ndi mphamvu pa olamulira a* dziko lapansi. Iye ndi wokwezeka kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “zishango za.”