Salimo 48:1-14

  • Ziyoni ndi mzinda wa Mfumu Yaikulu

    • Anthu padziko lonse amasangalala ndi phiri la Ziyoni (2)

    • Yenderani mzindawo ndi nsanja zake (11-13)

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ 48  Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri,Mumzinda wa Mulungu wathu, mʼphiri lake loyera.  2  Phiri la Ziyoni limene lili mʼdera lakutali lakumpoto,Ndi lokongola chifukwa lili pamalo okwezeka komanso anthu padziko lonse lapansi akusangalala nalo,+Ndipo ndi mzinda wa Mfumu Yaikulu.+  3  Munsanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,Mulungu wasonyeza kuti iye ndi malo othawirako otetezeka.*+  4  Taonani! Mafumu asonkhana,*Onse pamodzi abwera.  5  Iwo ataona mzindawo, anadabwa. Anapanikizika nʼkuthawa mwamantha.  6  Kumeneko iwo anayamba kunjenjemera,Anavutika ngati mkazi amene akubereka.  7  Pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu yakumʼmawa, munaswa sitima za ku Tarisi.  8  Zimene tinangomva, tsopano taziona tokha,Mumzinda wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mumzinda wa Mulungu wathu. Mulungu adzakhazikitsa mzindawo mpaka kalekale.+ (Selah)  9  Inu Mulungu, ife timaganizira mozama za chikondi chanu chokhulupirika,+Tili mʼkachisi wanu. 10  Inu Mulungu, mofanana ndi dzina lanu, mawu okutamandaniAfika kumalire a dziko lapansi.+ Dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.+ 11  Phiri la Ziyoni likondwere,+Matauni* a ku Yuda asangalale chifukwa cha zigamulo zanu.+ 12  Gubani mozungulira Ziyoni. Zungulirani mzinda wonsewo,Werengani nsanja zake.+ 13  Ganizirani mofatsa za mpanda wake wolimba.+ Yenderani nsanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,Kuti mudzafotokozere mibadwo yamʼtsogolo. 14  Chifukwa Mulungu uyu ndi Mulungu wathu+ mpaka muyaya. Iye adzatitsogolera mpaka kalekale.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Kapena kuti, “anakumana atapangana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aakazi.”
Mabaibulo ena amati, “kufikira imfa.”