Salimo 57:1-11
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene anathawa Sauli nʼkukalowa mʼphanga.+
57 Ndikomereni mtima inu Mulungu, ndikomereni mtima,Chifukwa ine ndathawira kwa inu.+Ndathawira mumthunzi wa mapiko anu mpaka mavuto atadutsa.+
2 Ndikufuulira Mulungu Wamʼmwambamwamba,Mulungu woona amene akuthetsa mavuto amenewa kuti zinthu zindiyendere bwino.
3 Adzatumiza thandizo kuchokera kumwamba nʼkundipulumutsa.+
Adzasokoneza wofuna kundiwakha ndi pakamwa pake. (Selah)
Mulungu adzasonyeza chikondi chake chokhulupirika ndi choonadi chake.+
4 Ndazunguliridwa ndi mikango.+Ndikuyenera kugona pakati pa anthu amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+
5 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+
6 Iwo atchera ukonde kuti akole mapazi anga.+Ndili ndi nkhawa yaikulu.+
Anakumba dzenje panjira yanga,Koma agweramo okha.+ (Selah)
7 Ndatsimikiza mtima, Inu Mulungu,+Ndatsimikiza mtima.
Ndidzakuimbirani nyimbo ndi zipangizo zoimbira.
8 Dzuka, iwe ulemerero wanga.
Dzuka, iwe choimbira cha zingwe, ndi iwenso zeze.
Ine ndidzadzuka mʼbandakucha.+
9 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+
10 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchachikulu moti chafika kumwamba,+Ndipo kukhulupirika kwanu kwafika kuthambo.
11 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.