Salimo 83:1-18
Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
83 Inu Mulungu, musakhale chete.+Musakhale chete osalankhula kanthu kapena kuchita chilichonse, inu Mulungu.
2 Taonani! Adani anu akuchita phokoso.+Anthu amene amadana nanu akuchita zinthu modzikuza.*
3 Mwachinsinsi komanso mochenjera iwo amakonzera chiwembu anthu anu.Iwo amakonzera chiwembu anthu anu omwe ndi amtengo wapatali.*
4 Iwo akunena kuti: “Bwerani tiwawononge kuti asakhalenso mtundu,+Kuti dzina la Isiraeli lisadzakumbukiridwenso.”
5 Mogwirizana iwo amapangana zoti achite,*Iwo apanga mgwirizano* kuti atsutsane ndi inu+—
6 Aedomu, mbadwa za Isimaeli, Amowabu+ komanso mbadwa za Hagara,+
7 Agebala, Aamoni,+ Aamaleki,Afilisiti+ pamodzi ndi anthu a ku Turo.+
8 Asuri nawonso agwirizana nawo,+Ndipo amathandiza* ana aamuna a Loti.+ (Selah)
9 Muwachitire zimene munachitira Midiyani,+Komanso zimene munachitira Sisera ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni.*+
10 Iwo anawonongedwa ku Eni-dori.+Anasanduka manyowa munthaka.
11 Anthu awo olemekezeka muwachititse kukhala ngati Orebi ndi Zeebi.+Ndipo akalonga* awo muwachititse kukhala ngati Zeba ndi Zalimuna.+
12 Chifukwa iwo anena kuti: “Tiyeni tilande dziko limene Mulungu amakhala.”
13 Inu Mulungu wanga, achititseni kukhala ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo,+Ngati mapesi amene amauluka ndi mphepo.
14 Ngati moto umene umayatsa nkhalango,Ngati malawi a moto umene ukuyaka mʼmapiri,+
15 Muwathamangitse ndi mphepo yanu yamphamvu,+Ndipo muwaopseze ndi mphepo yanu yamkuntho.+
16 Phimbani* nkhope zawo ndi manyazi,Kuti afunefune dzina lanu, inu Yehova.
17 Achititsidwe manyazi ndipo akhale ndi mantha mpaka kalekale.Anyozeke ndipo atheretu.
18 Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+Inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “atukula mitu yawo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “omwe ndi obisika.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndi mtima wonse iwo amagawana nzeru.”
^ Kapena kuti, “pangano.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Amakhala ngati dzanja kwa.”
^ Kapena kuti, “kukhwawa la Kisoni.”
^ Kapena kuti, “atsogoleri.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzazani.”