Salimo 86:1-17
Pemphero la Davide.
86 Tcherani khutu* inu Yehova ndipo mundiyankhe,Chifukwa ndavutika komanso ndasauka.+
2 Tetezani moyo wanga chifukwa ndine wokhulupirika.+
Pulumutsani mtumiki wanu amene amakukhulupirirani,Chifukwa ndinu Mulungu wanga.+
3 Ndikomereni mtima inu Yehova,+Chifukwa ndimaitana inu tsiku lonse.+
4 Chititsani kuti mtumiki wanu asangalale,*Chifukwa ndimayangʼana kwa inu, Yehova.
5 Inu Yehova ndinu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+Mumasonyeza chikondi chokhulupirika chochuluka kwa onse amene amaitana inu.+
6 Mvetserani pemphero langa inu Yehova.Ndipo mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+
7 Pa tsiku limene ndakumana ndi mavuto ndidzaitana inu,+Chifukwa inu mudzandiyankha.+
8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu,+Palibe aliyense amene wachita zinthu zofanana ndi zimene inu mwachita.+
9 Mitundu yonse ya anthu imene munapangaIdzabwera nʼkudzagwada pamaso panu, inu Yehova,+Ndipo idzalemekeza dzina lanu.+
10 Chifukwa inu ndinu wamkulu ndipo mumachita zinthu zodabwitsa.+Inu nokha ndinu Mulungu.+
11 Ndilangizeni inu Yehova, za njira yanu.+
Kuti ndiyende mʼchoonadi chanu.+
Ndithandizeni kuti ndiziopa dzina lanu ndi mtima wonse.*+
12 Ndimakutamandani ndi mtima wanga wonse, inu Yehova Mulungu wanga,+Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale,
13 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika chimene mumandisonyeza ndi chachikuluNdipo mwapulumutsa moyo wanga ku dzenje la Manda.*+
14 Inu Mulungu, anthu onyada andiukira.+Gulu la anthu ankhanza likufuna kuchotsa moyo wanga,Ndipo iwo sakulemekezani.*+
15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima,Wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka ndiponso wokhulupirika.*+
16 Ndiyangʼaneni ndipo mundikomere mtima.+
Patsani mtumiki wanu mphamvu,+Ndipo pulumutsani mwana wa kapolo wanu wamkazi.
17 Ndisonyezeni chizindikiro cha* ubwino wanu,Kuti anthu amene amadana nane aone ndipo achititsidwe manyazi,
Chifukwa inu Yehova ndi amene mumandithandiza komanso kundilimbikitsa.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Weramani ndipo mumvetsere.”
^ Kapena kuti, “moyo wa mtumiki wanu usangalale.”
^ Kapena kuti, “Ndipatseni mtima wosagawanika.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “sanaike inu patsogolo pawo.”
^ Kapena kuti, “wachoonadi.”
^ Kapena kuti, “umboni wa.”