Salimo 87:1-7
-
Ziyoni ndi mzinda wa Mulungu woona
-
Amene anabadwira mu Ziyoni (4-6)
-
Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
87 Maziko a mzinda wa Mulungu ali mʼmapiri opatulika.+
2 Yehova amakonda kwambiri mageti a Ziyoni+Kuposa matenti onse a Yakobo.
3 Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ (Selah)
4 Ndidzaika Rahabi* ndi Babulo mʼgulu la amene+ akundidziwa.Filisitiya, Turo ndi Kusi alinso mʼgulu la amene akundidziwa.
Ine ndidzati: “Amenewa anabadwira mʼZiyoni.”
5 Ponena za Ziyoni anthu adzati:
“Aliyense anabadwira mmenemo.”
Ndipo Wamʼmwambamwamba adzakhazikitsa mzinda umenewo ndi kuulimbitsa.
6 Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti:
“Amenewa anabadwira mu Ziyoni.” (Selah)
7 Oimba+ komanso ovina magule amene amavina mozungulira+ adzanena kuti:
“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”*+
Mawu a M'munsi
^ Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo.
^ Kapena kuti, “Zinthu zanga zonse zimachokera kwa iwe.”