Salimo 93:1-5
93 Yehova wakhala Mfumu!+
Iye wavala ulemerero.Yehova wavala mphamvuWazivala ngati lamba wamʼchiuno.
Dziko lapansi lakhazikika,Moti silingasunthidwe.*
2 Mpando wanu wachifumu unakhazikika kalekale.+Munakhalako kuyambira kalekale.+
3 Inu Yehova, mitsinje yasefukira,Mitsinje yasefukira ndipo ikuchita mkokomo.Mitsinje ikupitiriza kusefukira komanso kuchita mkokomo.
4 Ulemerero wa Yehova ndi waukulu kumwamba,Kuposa mkokomo wa madzi ambiri,+Ndi wamphamvu kuposa mafunde amphamvu amʼnyanja.+
5 Zikumbutso zanu ndi zodalirika kwambiri.+
Inu Yehova, nyumba yanu ndi yokongola komanso yoyera+ nthawi zonse.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Moti silingagwedezeke.”